Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-26 tsamba 1-6
  • Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
  • Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerenga Baibulo?
  • Thandizo Kuti Timvetse Baibulo
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kupatula Nthaŵi Mlungu Uliwonse Kuti Mumvetse Baibulo?
  • Pempho Lakuti Muphunzire
  • Thandizo Lofunika Kuti Mumvetse Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mwayi Woti Aliyense Aphunzire Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Baibulo ndi Inu
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Gwiritsitsani Mawu a Mulungu
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
T-26 tsamba 1-6

Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerenga Baibulo?

BAIBULO silifanana ndi buku lina lililonse. Ilo lili ndi malangizo achikondi ochokera kwa Mulungu. (1 Atesalonika 2:13) Ngati muchita zimene Baibulo limaphunzitsa, mudzapindula kwambiri. Mudzam’konda kwambiri Mulungu ndipo mudzam’yandikira iye Wopatsa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Mudzadziŵa mmene mungam’fikire m’pemphero. Nthaŵi ya mavuto, Mulungu angakuthandizeni. Mukatsatira miyezo imene ili m’Baibulo, Mulungu adzakupatsani moyo wosatha.—Aroma 6:23.

Baibulo lili ndi choonadi chimene chimaunikira. Anthu amene aphunzira Baibulo amamasuka ku zikhulupiriro zolakwika zimene zikulamulira anthu miyandamiyanda. Mwachitsanzo, kudziŵa zoonadi za zimene zimachitika tikamwalira, kumatichotsa mantha akuti anthu akufa angativulaze, kapena akuti abale athu ndi mabwenzi athu amene tinali kuwakonda koma anamwalira akuvutika. (Ezekieli 18:4) Zimene Baibulo limaphunzitsa za kuuka kwa akufa zimatonthoza aja amene okondedwa awo anamwalira. (Yohane 11:25) Kudziŵa zoonadi pankhani ya angelo oipa kumatithandiza kuzindikira kuopsa kwa kukhulupirira mizimu ndiponso kumatithandiza kudziŵa chifukwa chake pali mavuto ambiri padziko lapansi.

Mfundo zachikhalidwe za Mulungu zimene zili m’Baibulo zimatithandiza kudziŵa mmene tingakhalire ndi moyo kuti tipindule mwakuthupi. Mwachitsanzo, kukhala “wodzisunga” kumatithandiza kukhala ndi thanzi labwino. (1 Timoteo 3:2) Mwa ‘kudzikonzera tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu,’ timapewa kuwononga thanzi lathu. (2 Akorinto 7:1) Kugwiritsa ntchito uphungu umene uli m’Baibulo kumalimbikitsa chimwemwe muukwati ndiponso kumatithandiza kukhala odzilemekeza.—1 Akorinto 6:18.

Mukachita zimene Mawu a Mulungu amanena, mudzakhala munthu wachimwemwe. Kulidziŵa Baibulo kumatithandiza kupeza mtendere wa mumtima ndi kukhala okhutira ndiponso kumatipatsa chiyembekezo. Kumatithandiza kukulitsa makhalidwe abwino kwambiri monga chifundo, chikondi, chimwemwe, mtendere, ndi chikhulupiriro. (Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 4:24, 32) Makhalidwe ameneŵa amatithandiza kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino, tate kapena mayi wabwino, mnyamata kapena mtsikana wabwino.

Kodi mukufuna kudziŵa za m’tsogolo? Maulosi a Baibulo akutiuza kuti tikukhala m’nthaŵi yofunika kwambiri m’mbiri ya anthu. Kuphatikiza pa kulongosola mmene dziko lilili lerolino, maulosi ameneŵa akutiuzanso kuti posachedwapa Mulungu asintha dziko lapansi kukhala paradaiso.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Thandizo Kuti Timvetse Baibulo

Mwina mwayesapo kuŵerenga Baibulo koma limakuvutani kumva. Mwina simukudziŵa kuti mungayang’ane pati m’Baibulo kuti mupeze mayankho a mafunso anu. Ngati ndi choncho, palinso ena ambiri amene sakudziŵa si inu nokha. Tonsefe timafuna thandizo kuti timvetse Mawu a Mulungu. Mboni za Yehova zikuphunzitsa Baibulo kwaulere kwa anthu miyandamiyanda m’mayiko pafupifupi 235. Adzakhala okondwa kukuthandizani inunso.

Kaŵirikaŵiri zimakhala bwino kwambiri kuphunzira Baibulo pang’onopang’ono, kuyamba ndi ziphunzitso zoyambirira. (Ahebri 6:1) Pamene mukupitiriza, mudzatha kudya “chakudya chotafuna” chomwe ndi choonadi chakuya. (Ahebri 5:14) Baibulo ndiye gwero lake. Mabuku ofotokoza Baibulo, monga kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, adzakuthandizani kumvetsa Malemba amene amafotokoza nkhani zosiyanasiyana.

Kodi Ndinu Wokonzeka Kupatula Nthaŵi Mlungu Uliwonse Kuti Mumvetse Baibulo?

Phunziro la Baibulo lingakonzedwe kuti lizichitika pamalo ndi nthaŵi imene inu mukufuna. Ambiri amaphunzira kunyumba kwawo. Ena amaphunzira kudzera patelefoni. Phunziroli silili ngati kalasi la anthu ambiri. M’malo mwake limachitika mogwirizana ndi mmene inu panokha mulili, kuphatikizapo zimene mukudziŵa ndi maphunziro anu. Sipakhala mayeso, ndipo sadzakuchititsani manyazi. Adzayankha mafunso anu okhudza Baibulo, ndipo mudzaphunzira mmene mungam’kondere kwambiri Mulungu.

Simudzalipira chilichonse paphunziro la Baibuloli. (Mateyu 10:8) Ndi laulere ndipo ndi la anthu a chipembedzo chilichonse, ndiponso anthu amene sali m’chipembedzo koma akufunitsitsa kudziŵa zambiri za Mawu a Mulungu.

Kodi ndani amene angakhale nawo pa phunziroli? Banja lanu lonse. Mungauzenso anzanu ena onse kuti adzakhale nawo pa phunziroli. Ngati mukufuna, akhoza kumaphunzira ndi inu nokha basi.

Ambiri amapatula ola limodzi pamlungu kuti aphunzire Baibulo. Kaya mungathe kupatula nthaŵi yambiri yoposa pamenepa kapena ayi, kapena mumakhala ndi nthaŵi yochepa, Mboni zidzakuthandizani.

Pempho Lakuti Muphunzire

Tikukupemphani kuti muonane ndi Mboni za Yehova. Njira ina imene mungachitire zimenezi ndiyo kulembera ku adiresi ili m’munsiyi. Ndiyeno adzakonza kuti munthu wina adzaphunzire nanu Baibulo panyumba panu kwaulere.

□ Nditumizireni kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

□ Chonde fikani kudzaphunzira nane Baibulo panyumba panga kwaulere.

Baibulo limene tagwiritsa ntchito ndi Revised Nyanja (Union) Version, kusiyapo ngati tasonyeza lina. Komabe tatsatira kalembedwe kamakono.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena