Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 4/1 tsamba 4-7
  • Mwayi Woti Aliyense Aphunzire Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwayi Woti Aliyense Aphunzire Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MAYANKHO A MAFUNSO AMENE ANTHU AMAKONDA KUFUNSA, OKHUDZA PHUNZIRO LA BAIBULO
  • Kodi Phunziro la Baibulo lomwe a Mboni za Yehova Amachititsa Limakhala Lotani?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?
    Kodi Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo Tingawapeze Kuti?
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizisangalala Ndikamawerenga Baibulo?
    Galamukani!—2012
  • Kodi Mwasangalala Ndi Zimene Mwaphunzira?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 4/1 tsamba 4-7
Akuphunzira Baibulo

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGAKONDE KUPHUNZIRA BAIBULO?

Mwayi Woti Aliyense Aphunzire Baibulo

A Mboni za Yehovafe timadziwika ndi ntchito yathu yolalikira. Koma kodi mukudziwa kuti timaphunziranso Baibulo ndi anthu padziko lonse?

Bambo akuphunzira Baibulo kuntchito kwake

M’chaka cha 2014, a Mboni za Yehova pafupifupi 8,000,000 omwe akupezeka m’mayiko 240 ankaphunzira Baibulo ndi anthu pafupifupi 9,500,000 mwezi uliwonse.a Chiwerengero chimenechi ndi chachikulu kuposa chiwerengero cha anthu a m’mayiko 140.

Kuti tithe kugwira ntchitoyi, timasindikiza Mabaibulo, mabuku, magazini ndi zinthu zina zothandiza kuphunzira Baibulo zokwana 500 miliyoni m’zinenero pafupifupi 700. Zimenezi zimathandiza kuti anthu athe kuphunzira Baibulo m’chinenero chomwe amachidziwa bwino.

“Kuphunzira Baibulo kunkandisangalatsa kwabasi, ngakhale kuti ndili kusukulu sindinkakonda kuphunzira. Komansotu zomwe ndinkaphunzira m’Baibulo zinkandilimbikitsa kwambiri.”—Katlego wa ku South Africa.

“Nditayamba kuphunzira Baibulo ndinapeza mayankho a mafunso onse omwe ndinali nawo ndi enanso ambiri.”—A Bertha a ku Mexico.

“Phunziro la Baibulo linkachitikira kunyumba kwathu pa nthawi yomwe ndinasankha. Zimenezi zinachititsa kuti ndiziona kuti palibe chomwe chingandilepheretse kuphunzira Baibulo.”—A Eziquiel a ku Brazil.

“Nthawi zambiri ndinkaphunzira kwa maminitsi 15 kapena 30. Koma pena ndinkaphunzira nthawi yochulukirapo kuposa pamenepa. Zinkangodalira nthawi yomwe ndili nayo.”—A Viniana a ku Australia.

“Phunziroli linali laulere komanso losangalatsa kwabasi.”—A Aimé a ku Benin.

“Wa Mboni amene ankandiphunzitsa Baibulo anali woleza mtima komanso wokoma mtima kwambiri. Zimenezi zinapangitsa kuti tiyambe kugwirizana kwambiri, moti anali mnzanga wapamtima.”—A Karen a ku Northern Ireland.

“Anthu ambiri amaphunzira Baibulo koma sakhala a Mboni za Yehova. Choncho si bwino kulephera kuphunzira Baibulo chifukwa choopa kuti mukhala wa Mboni.”—A Denton a ku England.

MAYANKHO A MAFUNSO AMENE ANTHU AMAKONDA KUFUNSA, OKHUDZA PHUNZIRO LA BAIBULO

Kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji?

Timasankha mutu ndipo kenako timakambirana mavesi osiyanasiyana a m’Baibulo ogwirizana ndi mutuwo. Mwachitsanzo, pophunzira Baibulo, tingathe kupeza mayankho a mafunso monga akuti: Kodi Mulungu ndi ndani, nanga ndi wotani? Kodi Mulungu ali ndi dzina? Nanga amakhala kuti? Kodi n’zotheka kukhala naye pa ubwenzi? Koma mwina mungadabwe kuti, kodi timadziwa bwanji mavesi a m’Baibulo omwe akunena za nkhaniyo?

Pophunzira Baibulo ndi anthu, timagwiritsa ntchito buku la masamba 224 lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?b Bukuli limatithandiza kudziwa mavesi amene akugwirizana ndi nkhani imene tikukambirana. Buku limeneli linapangidwa n’cholinga choti lithandize anthu kumvetsa mfundo zosavuta zimene Baibulo limaphunzitsa. M’bukuli muli mutu womwe umanena kuti akufa adzaukitsidwa. Mulinso mutu wonena za Mulungu, wonena za Yesu Khristu, za pemphero, chifukwa chake anthufe timavutika ndi ina yambiri.

Kodi phunziroli limachitikira kuti ndipo limachitika nthawi yanji?

Phunziroli limachitika pa nthawi ndi malo amene mungakonde.

Nanga limatenga nthawi yaitali bwanji?

Anthu ambiri amaphunzira Baibulo kwa ola limodzi mlungu uliwonse. Komabe, kutalika kwa nthawi ya phunziroli kumasiyanasiyana potengera zimene munthu angakonde. Ifeyo timatha kusintha kuti tigwirizane ndi zimene inuyo mukufuna. Ena amaphunzira kwa maminitsi 10 kapena 15 basi pa mlungu.

Kodi munthu amalipira ndalama zingati kuti aziphunzira Baibulo?

Phunziroli ndi laulere, ndipo mabuku amene timagwiritsa ntchito pophunzira sitilipiritsa. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.

Pamatenga nthawi yaitali bwanji kuti munthu adzamalize kuphunzira?

Mukhoza kuphunzira Baibulo kwa nthawi imene inuyo mukufuna. Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lili ndi mitu 19. Mukhoza kusankha mitu imene mukufuna kuphunzira kapena mukhoza kusankha kuphunzira mitu yonseyo. Zili kwa inunso kusankha kuti muziphunzira nthawi yaitali bwanji pa tsiku.

Ndikavomera kuti ndiziphunzira Baibulo, kodi ndiye kuti ndiyenera kukhala wa Mboni za Yehova?

Ayi. Timadziwa kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha chipembedzo chimene akufuna. Komabe timadziwanso kuti munthu akaphunzira Baibulo angathe kusankha bwino pa nkhani ya chipembedzo.

Kodi ndingatani ngati ndikufuna kudziwa zambiri?

Pitani pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Webusaitiyi ingakuthandizeni kudziwa zambiri zokhudza a Mboni za Yehova.

Kodi ndingatani ngati ndikufuna kuphunzira Baibulo?

  • Anthu amapempha kuti aziphunzira Baibulo polemba kalata, kudzera pa Intaneti kapena pofunsa a Mboni za Yehova a kudera lawo

    Mungalembe pa webusaiti yathu ya jw.org/ny kuti mupemphe munthu woti aziphunzira nanu Baibulo.

  • Mukhozanso kutilembera kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali patsamba 2.

  • Mungathenso kufunsa a Mboni za Yehova a kudera lanulo.

a Pophunzira Baibulo, timaphunzira ndi munthu mmodzi payekha kapena anthu angapo nthawi imodzi.

b Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo likupezeka m’zinenero 260. Mabuku amene asindikizidwa ndi oposa 230 miliyoni.

KUPHUNZIRA BAIBULO KUMATHANDIZA MABANJA

Baibulo lotsegula

“Mkazi wanga atayamba kuphunzira Baibulo, ndinaona kuti wasintha kwambiri. Banja lathunso linayamba kuyenda bwino. Zimenezi zinandichititsa chidwi, moti nanenso ndinayamba kuphunzira Baibulo. Zimene ndinaphunzira zinachititsa kuti nanenso ndisinthe n’kuyamba kuchita zabwino. Kuphunzira Baibulo kwathandiza kuti ine ndi mkazi wanga tizikondana kwambiri.”—A Eziquiel.

A Eziquiel

“Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa komanso kukwiya msanga. Panopa m’nyumba mwathu mumaoneka mwaukhondo kwambiri. Komanso panopa ana ndi mwamuna wanga akachita zabwino, ndimawayamikira ndipo inenso ndimayesetsa kuchita zinthu zowasangalatsa. Ndikuona kuti tsopano ndine munthu wosangalala kusiyana ndi kale.”—A Karen.

A Karen

“Nditayamba kuphunzira Baibulo, anthu ena ankandinyoza. Koma mwamuna wanga anandilimbikitsa kuti ndipitirize. Ankandiuza kuti: ‘Zonena za anthu ine ndilibe nazo ntchito. Zimene mukuphunzirazi zikukuthandizani kukhala munthu wabwino. Musasiye kuphunzira.’ Ndikuona kuti kuphunzira Baibulo kwathandiza kuti banja lathu likhale losangalala.”—A Viniana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena