Kodi Mwasangalala Ndi Zimene Mwaphunzira?
Kodi mungakonde kudziwa zambiri zimene Baibulo limaphunzitsa?
Iyi ndi mbali yochepa chabe ya zimene mungaphunzire m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana.
Palibe amene adzakuuzeni kuti mugule bukuli kapenanso kuti mulipire kuti muziphunzira. Tidzasangalala kuphunzira nanu pa nthawi ndi malo amene mungasankhe.
Mukamaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito bukuli muphunzira nkhani zambiri kuphatikizapo:
Cholinga cha moyo
Zimene mungachite kuti mupeze mtendere weniweni
Zimene mabanja angachite kuti azisangalala
Zimene Baibulo limalonjeza zokhudza m’tsogolo
Kuti mupeze bukuli komanso kuti mupitirize kuphunzira Baibulo, pemphani wa Mboni za Yehova aliyense kapenanso lembani fomu yopempha phunziro la Baibulo kudzera pa jw.org.