Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wt mutu 17 tsamba 151-158
  • Khalani Odzipereka kwa Mulungu Panyumba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Odzipereka kwa Mulungu Panyumba
  • Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ukwati Uyenera Kukhala Mpaka Liti?
  • Aliyense Azichita Mbali Yake
  • Kumene Tingapeze Mayankho
  • Tifunikira Kugwiritsira Ntchito Kudzipereka Kwaumulungu pa Nyumba
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kumaumanga Moyo Wabanja Wacimwemwe
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Lambirani Mulungu Woona Yekha
wt mutu 17 tsamba 151-158

Mutu 17

Khalani Odzipereka kwa Mulungu Panyumba

YEHOVA ndiye anayambitsa ukwati, ndipo Mawu ake ali ndi malangizo abwino kwambiri kwa anthu a m’banja. Chifukwa chotsatira malangizo amenewo, anthu ambiri akhala ndi maukwati abwino. N’zopatsa chidwi kuti ena amene anangotengana alembetsa maukwati awowo ku boma potsatira malangizo amenewo. Ena asiya kuyenda ndi amuna ena kapena akazi ena. Amuna achiwawa amene anali kuzunza akazi awo ndi ana awo aphunzira kukhala okoma mtima ndi achifundo.

2 Banja labwino lachikristu limadalira zinthu zambiri monga, mmene timaonera mfundo yakuti ukwati n’ngwachikhalire, zimene timachita kuti tikwaniritse maudindo athu m’banja, ndiponso mmene timachitira zinthu ndi anthu m’banja lathu. (Aefeso 5:33–6:4) Inde, tingadziŵedi zimene Baibulo limanena zokhudza mmene anthu pabanja ayenera kukhalira, komatu kutsatira uphungu wa Baibulowo ndi nkhani inanso payokha. Tonsefe sitifuna kukhala ngati anthu omwe Yesu anawatsutsa kuti sanali kutsatira malamulo a Mulungu. Iwo anali kudzinyenga okha poganiza kuti kungokhala wodzipereka pa chipembedzo n’kokwanira. (Mateyu 15:4-9) Ife tikufuna ‘kukhala odzipereka kwa Mulungu panyumba zathu’ osati kumangooneka chabe ngati ndife otero. Inde, tikufuna kumadziperekadi kwa Mulungu, chifukwa ‘kumapindulitsa kwakukulu.’—1 Timoteo 5:4, NW; 6:6; 2 Timoteo 3:5.

Kodi Ukwati Uyenera Kukhala Mpaka Liti?

3 Maukwati ambiri sakulimba. Ena amene akhala pabanja zaka zambiri amasudzulana n’kukwatiranso kapena kukwatiwanso. Ndiponso masiku ano si zachilendo kumva kuti achinyamata amene akwatirana posachedwapa apatukana. Komabe, kaya ena amachita zotani, ife tiyenera kufuna kusangalatsa Yehova. Choncho tiyeni tipende mafunso otsatiraŵa ndi malemba ake kuti tione zimene Mawu a Mulungu amanena pankhani yakuti ukwati n’ngwachikhalire.

Mwamuna ndi mkazi akakwatirana, kodi ayenera kuyembekeza kukhala limodzi mpaka liti? (Marko 10:6-9; Aroma 7:2, 3)

Kodi anthu okwatirana angasudzulane pa chifukwa chimodzi chiti chovomerezeka kwa Mulungu chomwe chingawalole kupezanso mabanja ena? (Mateyu 5:31, 32; 19:3-9)

Kodi Yehova amamva bwanji pamene anthu asudzulana pa zifukwa zimene Mawu ake savomereza? (Malaki 2:13-16)

Kodi Baibulo limalimbikitsa kupatukana monga njira yothetsera mavuto m’banja? (1 Akorinto 7:10-13)

Kodi kupatukana kungakhale koyenera pa zifukwa ziti? (Salmo 11:5; Luka 4:8; 1 Timoteo 5:8)

4 Maukwati ena amayenda bwino moti amakhalitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi ndicho kuyembekeza kuti onse aŵiri, mwamuna ndi mkazi, akule kaye. Komanso china ndi kupeza womanga naye banja wokhala ndi zolinga zofanana ndi zako, yemwe mutha kukambirana nkhani momasuka. Komabe, chofunika kwambiri ndi kupeza munthu amene amakonda Yehova ndipo amalemekeza Mawu a Mulungu pozindikira kuti ndiwo amathetsa mavuto. (Salmo 119:97, 104; 2 Timoteo 3:16, 17) Munthu wotereyu sadzakhala ndi maganizo akuti zinthu zikangovuta, basi mungangopatukana kapena kusudzulana. Zimene mnzakeyo amalephera kuchita sadzaziona kukhala zifukwa zoti iye azinyalanyaza udindo wake. M’malo mwake, adzalimbana nawo mavutowo n’kupeza njira zabwino zowathetsera.

5 Satana amati tidzasiya kutsata njira za Yehova pamene tavutika. (Yobu 2:4, 5; Miyambo 27:11) Koma ambiri a Mboni za Yehova amene avutika chifukwa chokhala pabanja ndi mnzawo wotsutsa chikhulupiriro chawo sanasinthe maganizo n’kunyanyala zimene analumbira pokwatirana. Ndi okhulupirikabe kwa Yehova ndi malamulo ake. (Mateyu 5:37) Ena amene apirira asangalala kuona kuti nayenso mnzawoyo wayamba kutumikira Yehova limodzi nawo—ngakhale kuti anali kutsutsa kwa zaka zambirimbiri! (1 Petro 3:1, 2) Koma Akristu amene amuna awo kapena akazi awo sasonyeza n’komwe kuti asintha kapenanso amene amawasiya chifukwa chakuti Akristuwo akutumikira Yehova, nawonso amadziŵa kuti adzadalitsidwa chifukwa chosonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu panyumba zawo.—Salmo 55:22; 145:16.

Aliyense Azichita Mbali Yake

6 N’zoona kuti pamafunika zambiri kuti anthu akhale ndi ukwati wabwino. Sikungokhalira limodzi chabe. Chinthu chachikulu chimene chimafunika kwa onse aŵiri ndicho kulemekeza makonzedwe a Yehova a umutu. Izi zimathandiza kuti panyumba pakhale dongosolo labwino ndipo onse amadziŵa kuti ndi otetezeka. Timaŵerenga pa 1 Akorinto 11:3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono, kuti: “Kristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Kristu.”

7 Kodi mwaona zimene vesilo layamba kutchula? Inde, mwamuna aliyense ali ndi Mutu, Kristu, yemwe ayenera kumugonjera. Izi zikutanthauza kuti mwamuna monga mutu ayenera kuchita zinthu m’njira imene imaonetsa makhalidwe a Yesu. Kristu amagonjera Yehova, amakonda kwambiri mpingo, ndipo amausamalira. (1 Timoteo 3:15) Ndipotu iye ‘anadzipereka yekha m’malo [mwa mpingowo].’ Yesu si wonyada kapenanso wosaganizira ena, koma ndi “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” Anthu amene iye ali Mutu wawo ‘amapeza mpumulo wa miyoyo [yawo].’ Mwamuna akamachita zinthu moteremu ndi banja lake, amasonyeza kuti akugonjera Kristu. Ndiyeno mkazi wachikristu akamagwirizana ndi mwamuna wake ndi kugonjera umutu wake, aziona phindu lake lochita zimenezo ndipo azipeza mpumulo.—Aefeso 5:25-33; Mateyu 11:28, 29; Miyambo 31:10, 28.

8 Koma mavuto adzabukabe. Chifukwa china chingakhale chakuti onse m’banjamo asanayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo, ena angakhale kuti anali ndi khalidwe losafuna kuuzidwa zochita. Nthaŵi zina ngakhale kuwapempha mokoma mtima ndi kuwasonyeza chikondi sikungathandize. Tikudziŵa kuti Baibulo limati tiyenera kusiya “kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano.” (Aefeso 4:31) Koma ngati ena m’banjamo akuoneka kuti satha kulankhula mwanjira ina, kodi tiyenera kuchitanji? Eya, Yesu sanatsanzire anthu amene anali kumuopseza ndi kumuchitira chipongwe, koma anadalira Atate ake. (1 Petro 2:22, 23) Choncho panyumba pakabuka mavuto, onetsani kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu mwa kupemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni m’malo motengera njira za dziko.—Miyambo 3:5-7.

9 Sikuti anthu nthaŵi zonse amasintha mofulumira ayi, komabe uphungu wa m’Baibulo umathandizadi mukautsatira moleza mtima ndiponso mwakhama. Amuna ambiri aona kuti ukwati wawo unayamba kuyenda bwino pamene anazindikira mmene Kristu amachitira zinthu ndi mpingo. Mumpingo umenewo sikuti muli anthu angwiro. Komatu Yesu amaukonda, amaupatsa chitsanzo chabwino, ndipo amagwiritsa ntchito Malemba pouthandiza kuwongolera. Anapereka moyo wake m’malo mwa mpingowo. (1 Petro 2:21) Chitsanzo chake chalimbikitsa amuna achikristu ambiri kukhala mitu ya mabanja yabwino ndi kupereka thandizo mwachikondi kuti awongolere ukwati wawo. Akamatere zinthu zimayenda bwino kwambiri kusiyana n’kupeza ena zifukwa kapena kusiya kulankhula.

10 Nanga bwanji ngati mwamuna sachita chidwi kuti adziŵe zimene zili mu mtima mwa a pabanja lake kapena ngati sayambitsa zoti banja likambirane za Baibulo ndiponso zoti lichite zinthu zina? Kapena bwanji ngati mkazi sagwirizana ndi zochita za mwamuna wake ndiponso sasonyeza kugonjera kumene Mulungu amafuna? Ena zinthu zimayamba kuwayendera bwino mwa kukambirana mavutowo mwaulemu monga banja. (Genesis 21:10-12; Miyambo 15:22) Koma ngakhale zimene zingachitike sizimene tinali kuyembekezera, tonse tingathandize kuti zinthu panyumbapo ziziyenda bwino mwa kukhala ndi zipatso za mzimu wa Mulungu pamoyo wathu. Tikatero tidzawaganizira ena m’banjamo chifukwa chowakonda. (Agalatiya 5:22, 23) Chimene chidzathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino sikudikira kuti mnzathuyo achitepo zinazake, koma kuchita mbali yathu ifeyo, ndipo tidzasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.—Akolose 3:18-21.

Kumene Tingapeze Mayankho

11 Pali malo ambiri kumene anthu amafunako uphungu wokhudza mmene angayendetsere banja lawo. Koma ife timadziŵa kuti Mawu a Mulungu ali ndi malangizo abwino koposa, ndipo timayamikira kuti Mulungu kudzera m’gulu lake looneka amatithandiza kuwagwiritsa ntchito. Kodi mukupinduladi ndi thandizo limeneli?—Salmo 119:129, 130; Mika 4:2.

12 Kuwonjezera pa kufika pa misonkhano ya mpingo, kodi muli ndi nthaŵi imene munakonza kuti muziphunzira Baibulo mokhazikika pabanja panu? Mabanja amene amachita zimenezi zimawathandiza kukhala ogwirizana pa kulambira kwawo. Banja lawo limayenda bwino pamene atsatira Mawu a Mulungu pa moyo wawo.—Deuteronomo 11:18-21.

13 Mwina mungakhale ndi mafunso okhudza nkhani za m’banja. Mwachitsanzo, kodi kulera n’koyenera? Kodi ilipo nthaŵi imene kuchotsa mimba kungakhale koyenera? Ngati mwana sakusangalala kwenikweni ndi zinthu zauzimu, kodi iye afunika kumalambira limodzi ndi banja mpaka pati? Mafunso ambiri otereŵa ayankhidwa m’mabuku olembedwa ndi Mboni za Yehova. Dziŵani kugwiritsa ntchito mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, kuphatikizapo zolozera nkhani, kuti mupeze mayankho. Ngati mulibe mabuku amene akulozerani mu cholozera nkhani, kaoneni mu laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu. Mwinanso ena angakhale nawo mabuku ameneŵa pa kompyuta. Mukhozanso kukambirana mafunso anuwo ndi Akristu anzanu okhwima mwauzimu, amuna kapena akazi. Koma musayembekeze kupeza yankho lonena mwatchutchutchu zimene mufunika kuchita ndi zimene simufunika kuchita pa funso lililonse. Nthaŵi zambiri inuyo nokha kapena limodzi ndi mkazi wanu kapena mwamuna wanu, mufunika kusankha. Ndiyeno sankhani zinthu zimene zimasonyeza kuti ndinu wodzipereka kwa Mulungu pamene muli pagulu komanso ngakhale mukakhala panyumba panu.—Aroma 14:19; Aefeso 5:10.

Bwerezani Zimene Mwakambirana

• Kodi kukhulupirika kwathu pabanja kumakhudzana motani ndi kukhulupirika kwathu kwa Yehova?

• Pamene tapanikizika ndi mavuto a m’banja, n’chiyani chidzatithandiza kuchita zokondweretsa Mulungu?

• Ngakhale pamene ena m’banjamo akulephera pa zinthu zina, kodi ife tingachite chiyani kuti zinthu ziwongokere?

[Mafunso]

1. Kodi kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu kwakhudza motani maukwati?

2. Kodi banja labwino lachikristu limadalira chiyani?

3. (a) Kodi n’chiyani chikuchitikira maukwati ambiri, koma ife tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji? (b) Pogwiritsa ntchito Baibulo lanu, yankhani mafunso amene ali m’munsi mwa ndime ino.

4. N’chifukwa chiyani maukwati ena amakhalitsa?

5. (a) Kodi kukhala wokhulupirika kwa Yehova kumakhudza ukwati motani? (b)  Ngakhale pamene wina amatsutsa chikhulupiriro cha mnzake, kodi pamakhala phindu lanji ngati wotsutsidwayo amatsatabe miyezo ya Yehova?

6. Kuti anthu akhale ndi ukwati wabwino, kodi ayenera kulemekeza makonzedwe ati?

7. Kodi umutu m’banja uyenera kuchitidwa motani?

8. (a) N’chifukwa chiyani m’mabanja ena kuchita zinthu mwachikristu kungaoneke ngati sikukuthandiza? (b) Kodi tiyenera kuchitanji ngati takumana ndi vuto loterolo?

9. M’malo mopeza ena zifukwa, kodi amuna achikristu ambiri aphunzira kuchitanji?

10. (a) Kodi mwamuna kapena mkazi, ngakhale yemwe amanena kuti ndi Mkristu, angapangitse motani zinthu kukhala zovuta kwa ena panyumba? (b) Kodi chingachitike n’chiyani kuti zinthu ziziyenda bwino?

11, 12. Kodi Yehova watipatsa chiyani chotithandiza kukhala ndi mabanja abwino?

13. (a) Ngati tili ndi mafunso okhudza nkhani za m’banja, kodi nthaŵi zambiri mayankho ofunika tingawapeze kuti? (b) Kodi zonse zimene timasankha ziyenera kuonetsanji?

[Chithunzi patsamba 155]

Mwamuna monga mutu ayenera kuonetsa makhalidwe a Yesu

[Chithunzi patsamba 157]

Kuphunzira Baibulo ndi banja lanu kumathandiza kuti likhale logwirizana

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena