CHIGAWO 5
Zoona Zake za Matsenga ndi Ufiti
1. Kodi okhulupirira matsenga ndi ufiti ndi ochuluka bwanji?
“MU Africa, m’posafunika kuchita kufunsa ngati mfiti ziliko kapena kulibe,” likutero buku lakuti African Traditional Religion. Likuwonjeza kuti: “Mwafirika aliyense kaya wolemera kapena wosauka, wotchuka kapena munthu wamba amaona kuti nkhani ya ufiti ndi yofunika kwambiri.” Onse osaphunzira ndi ophunzira amakhulupirira matsenga ndi ufiti. Atsogoleri achipembedzo m’Chisilamu ndi m’Matchalitchi Achikristu amakhulupiriranso zimenezi.
2. Malinga ndi zimene ambiri amakhulupirira, kodi mphamvu ya matsenga imachoka kuti?
2 Malinga ndi zimene ambiri mu Africa muno amakhulupirira, pali mphamvu inayake yauzimu yopambana mphamvu ya anthu. Mulungu ndiye amailamulira. Mizimu ndi makolo angathe kuigwiritsa ntchito mphamvuyo. Ndipo amati anthu ena amadziŵanso mmene angaipezere ndi kuigwiritsa ntchito pa zinthu zabwino (kutsirika) kapena kuchita zoipa (kulodza).
3. Kodi kuchita matsenga n’kutani, ndipo anthu amakhulupirira zoti matsenga angachite chiyani?
3 Munthu amachitira matsenga adani ake. Anthu amakhulupirira kuti amatsenga ali ndi mphamvu yotumiza mileme, mbalame, ntchentche, ndi nyama zina kuti zikapweteke anthu anzawo. Ambiri amakhulupirira kuti matsenga amachititsa mikangano, kusabala, matenda, ngakhale imfa.
4. Kodi ambiri amakhulupirira chiyani za mfiti, ndipo ena amene anali mfiti aulula zoti chiyani?
4 Zimenezi sizisiyana ndi ufiti. Anthu amati mfiti zimasiya matupi awo usiku ndi kuuluka kupita kwina, kaya kukakumana ndi mfiti zina kapena kukawononga miyoyo ya adani awo. Popeza matupi a mfiti amakhalabe aligone pabedi, umboni wotsimikiza nkhani zimenezi umaperekedwa makamaka ndi anthu amene anasiya ufiti. Mwachitsanzo, magazini ina ya mu Africa muno ili ndi mawu onenedwa ndi anthu ena amene anali mfiti (makamaka atsikana). Iwo anaulula kuti: “Ndinapha anthu 150 mwa kuchititsa ngozi za galimoto.” “Ndinapha ana asanu mwa kuyamwa magazi awo onse.” “Ndinapha anyamata atatu amene ndinali nawo pachibwenzi chifukwa anathetsa chibwenzi chathu.”
5. Kodi kutsirika n’kutani, ndipo okonda kutsirika amachita zotani?
5 Kutsirika amati kumateteza munthu ku zoipa. Okonda kutsirika amavala mphete kapena makoza amatsenga. Amamwa kapena kudzola m’thupi mankhwala owateteza. M’nyumba zawo amabisa kapena kukumbira pansi zinthu zimene amaganiza kuti zili ndi mphamvu yowateteza. Amakhulupirira njirisi zolembapo mawu a m’Koran kapena a m’Baibulo.
Mabodza Ndiponso Chinyengo
6. Kodi Satana ndi ziŵanda zake atani m’mbuyomu, ndipo mphamvu zawo tiyenera kuziona bwanji?
6 N’zoona kuti Satana ndi ziŵanda zake ali adani oopsa kwa anthu. Ali ndi mphamvu yosokoneza maganizo ndi moyo wa anthu, ndipo m’mbuyomu aloŵa ndi kukhala mwa anthu ndi nyama zomwe. (Mateyu 12:43-45) Pamene sitiyenera kuganiza kuti zili ndi mphamvu zochepa, sitiyeneranso kuzikokomeza.
7. Kodi Satana amafuna kuti ife tikhulupirire chiyani, ndipo ndi fanizo lotani limene likusonyeza zimenezi?
7 Satana ndi katswiri ponyenga anthu. Amapusitsa anthu kuganiza kuti iye ali ndi mphamvu kwambiri kusiyana ndi zimene ali nazo. Tifotokoze mwafanizo: Pankhondo yaposachedwapa m’dziko lina mu Africa muno, asilikali anagwiritsa ntchito zokuzira mawu poopseza adani awo. Asilikaliwo akafuna kuukira anzawo, anali kuliza kwambiri makaseti amene anajambulamo kulira kwa mizinga ndi mfuti. Chimene anali kufuna n’chakuti adani awo aganize kuti gulu limene likuwaukiralo lili ndi zida zambiri zoopsa. N’chimodzimodzinso ndi Satana. Iye amafuna kuti anthu azikhulupirira kuti ali ndi mphamvu zopanda malire. Cholinga chake n’chakuti aopseze anthu kuti achite zofuna zake m’malo mwa zofuna za Yehova. Tiyeni tsopano tipende mabodza atatu amene Satana amafuna kuti anthu akhulupirire.
8. Kodi bodza loyamba limene Satana amalifalitsa n’lotani?
8 Nali bodza loyamba limene Satana amafalitsa: Kulibe tsoka limene limadza mwangozi; tsoka lililonse limene palibe munthu wina woliyambitsa mwachindunji limadza chifukwa cha mphamvu ina yopambana mphamvu ya anthu. Mwachitsanzo, tinene kuti mwana wamwalira ndi malungo. Mayi ake angadziŵe kuti malungo ndi matenda amene amayamba chifukwa cha udzudzu. Koma angakhulupirirebe kuti munthu wina anagwiritsa ntchito ufiti kutumiza udzudzu umene unaluma mwana wakeyo.
Nthawi zina zoipa zimangochitika
9. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Satana sachititsa mavuto onse?
9 Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu yoyambitsa mavuto ena, ndi kulakwa kuganiza kuti ali ndi mphamvu yoyambitsa mavuto onse. Baibulo limati: “Omwe athamanga msanga sapambana m’liŵiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; [chifukwa nthaŵi ndi zochitika zosayembekezera zimawagwera iwo onse, NW].” (Mlaliki 9:11) Pa mpikisano wothamanga, wina angakhale ndi liŵiro loposa anzake onse, koma sangapambane. “Zochitika zosayembekezera” zingam’lepheretse. Zingachitike kuti mmene akuthamanga n’kukhumudwa ndi kugwa kapena angadwale kapena kubzungunyuka mwendo. Zimenezi zingachitike kwa wina aliyense. Sikuti Satana ndiye amachititsa zimenezo kapena kuti zimachitika chifukwa cha ufiti; zimangochitika basi.
10. Kodi anthu amati chiyani za mfiti, ndipo tikudziŵa bwanji kuti limeneli ndi bodza?
10 Nali bodza lachiŵiri limene Satana amafalitsa: Mfiti zimasiya matupi awo ndi kuyenda usiku wonse kukakumana ndi mfiti zina kapena kukamwa magazi kapena kukapha adani awo. Ndiye taganizani izi: ‘Ngati mfiti zimatha kuchita zimenezo, kodi chimachoka kusiya thupilo n’chiyani?’ Monga mmene taonera, palibe chimene chimachoka kusiya thupi la munthu. Ndipotu mzimu ndi mphamvu ya moyo imene imagwira ntchito m’thupi koma siitha kuchita kalikonse popanda thupilo.
Mfiti sizingasiye matupi awo
11. Tikudziŵa bwanji kuti mfiti sizitha kusiya matupi awo, ndipo kodi mukukhulupirira zimenezi?
11 N’zosatheka kuti mzimu uchoke kusiya thupi ndi kukachita chilichonse, kaya chabwino kapena choipa. Choncho, mfiti sizingathe kusiya matupi awo. Sizichita zinthu zimene zimati zimachita kapena zimene zimaganiza kuti zachita.
12. Kodi Satana amatani pofuna kuti anthu akhulupirire kuti iwo achita zinthu zimene sanachite?
12 Nanga tingazifotokoze bwanji zonena za aja amene anali mfiti? Satana angachititse anthu kuganiza kuti iwo achita zinthu zimene sanachite. Iye angagwiritse ntchito masomphenya kuchititsa anthu kuganiza kuti aona zimene sanaone, kumva zimene sanamve, ndi kuchita zinthu zimene sanachite. Pochita zimenezi, Satana amafuna kupandutsa anthu kuwachotsa kwa Yehova ndi kuti iwo aziganiza kuti Baibulo n’labodza.
13. (a) Kodi kutsirika n’kwabwino? (b) Kodi Malemba amati chiyani za matsenga?
13 Bodza lachitatu ndi ili: Kutsirika, kumene amati kumateteza munthu ku matsenga, n’kwabwino. Baibulo silisiyanitsa matsenga ndi kutsirika. Limaletsa zonsezi. Taonani malamulo amene Yehova anapatsa mtundu wa Israyeli okhudza zamatsenga ndi okonda matsenga:
‘Musamaombeza ula.’—Levitiko 19:26.
“Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu.”—Levitiko 20:27.
“Asapezeke mwa inu . . . wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta.”—Deuteronomo 18:10-14.
14. N’chifukwa chiyani Yehova anapereka malamulo oletsa zamatsenga?
14 Malamulo ameneŵa anamveketsa mfundo yakuti Mulungu sanafune anthu ake kuchita zamatsenga. Yehova anawapatsa malamulo ameneŵa chifukwa anawakonda ndipo sanafune kuti iwo azikhala amantha ndiponso akapolo chifukwa cha zikhulupiriro. Sanafune kuti ziŵanda ziziwavuta.
15. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana?
15 Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zimene ziŵanda zingachite ndi zimene sizingachite, limasonyezabe kuti Yehova Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana ndi ziŵanda. Yehova ndiye anachititsa kuti Satana am’pitikitse kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Kumbukiraninso kuti Satana anachita kupempha kuti ayese Yobu ndipo analabadira chenjezo la Mulungu lakuti asaphe Yobu.—Yobu 2:4-6.
16. Ngati tikufuna chitetezo, tiyenera kuyang’ana kwa ndani?
16 Miyambo 18:10 imati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” Chotero tiyenera kuyang’ana kwa Yehova kuti atiteteze. Atumiki a Mulungu sakhulupirira kuti zithumwa kapena mankhwala angawateteze ku zoipa zimene Satana ndi ziŵanda zake amachita, ndipo saopa kuti mfiti zingawalodze. Atumiki a Mulungu amakhulupirira zimene Baibulo limanena kuti: “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 Mbiri 16:9.
17. Kodi Yakobo 4:7 amatitsimikizira za chiyani, nanga tifunika kuchita chiyani?
17 Inunso mungakhale ndi chidaliro chimenechi ngati mukutumikira Yehova. Yakobo 4:7 amati: “Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” Ngati mukutumikira Mulungu woona ndi kumvera iye, Yehova adzakutetezani.