Lingaliro la Baibulo
Kodi Chimachititsa Ufiti N’chiyani?
“AFITI.” Kodi mawu amenewo amakuganizitsani za chiyani? Zithunzithunzi za tinkhalamba tikutamba kapena za akazi osadziletsa akuyankhulitsana ndi Satana? Mosiyana ndi maganizo opereŵera ameneŵa, ambiri amene amadzitcha mfiti masiku ano, amaoneka ngati anthu ena onse. Ena ndi anthu a zintchito zapamwamba, monga maloya, aphunzitsi, olemba mabuku, ndi anamwino. Padziko lonse payambanso kubuka magulu a zipembedzo amene amaoneka kuti ndi a zamizimu, monga zipembedzo za chilengedwe ndi neopaganism.a “Mukapita ku Russia masiku ano, kulikonse kumene mungaloŵere, ufiti ndi moyo wa anthu watsiku ndi tsiku,” anatero wapolisi wa m’dzikolo. Dziko la United States akuti lili ndi chiŵerengero chapakati pa 50,000 ndi 300,000 cha mfiti kapena kuti a “Wiccan” monga ena amadzitchulira.b
Lerolino mawu akuti “mfiti” nthaŵi zambiri amagwiritsidwa ntchito kutanthauza zinthu zosiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyananso. Zikuoneka kuti gwero lalikulu la kufalanso kwa ufiti masiku ano ndi zikhulupiriro zotsalira za chipembedzo cholambira milungu yaikazi, chozikidwa pa chilengedwe ndiponso chokhala ndi chikhulupiriro cholimba pa mphamvu zamizimu. Mfiti zina zimatamba pazokha, zimayang’ana kusintha kwa nyengo, kukula kwa mwezi, ndi zinthu zina zochitika m’chilengedwe. Ena amalambira ndi kuchita nyanga zawo mogwirizana pakagulu, nthaŵi zambiri kokhala ndi mfiti 13.
N’zoona kuti masiku ano m’mayiko ena otukuka anthu akuona mfiti mosiyana kwambiri ndi mmene amazionera M’nyengo Zapakati, zimene zinachititsa kuti aziziotcha. Komabe, mwapatalipatali, anthu adakachitabe chiwawa kulimbana ndi mfiti. Mwachitsanzo, kumayambiriro a October 1998 ku Indonesia, magulu a anthu atatenga zikwanje anapha anthu opitirira 150 amene anali kuwaganizira kuti anali mfiti. Ku South Africa malipoti a ziwawa zoposa 2,000, zolimbana ndi mfiti, kuphatikizapo anthu ophedwa 577, aperekedwa pakati pa 1990 ndi 1998. Poti zinthu zanyanya mbali zonse—anthu akuchita chidwi ndi ufiti ndiponso akudana ndi mfiti—kodi Akristu ayenera kuiona motani nkhaniyi?
Zofunika Zosakwaniritsidwa
Kodi chimachititsa anthu ufiti wamakono n’chiyani? Iwo amati chifukwa chimodzi ndicho kulemekeza chilengedwe komanso moyo. Ena amalongosola kuti pa mwambo wawo akamalambira sapereka nsembe za nyama. Ena amanena kuti amachita nawo ufiti monga mbali ya kufuna anthu amene angathe kukambirana nawo zakukhosi, kukhulupirirana, ndi kukhala ndi zofuna zauzimu zofanana. “Munthu aliyense amene ndikum’dziŵa m’gulu la akunja ameneŵa ndi wansangala kwambiri ndiponso wochezeka . . . Ndi anthu abwino kwambiri,” ikutero mfiti ina yaikazi yamakono. Ndipo ambiri amakana kuti sachita zausatana ngakhale pang’ono, ndipo amalongosola kuti m’chipembedzo chawo mulibe mulungu wololeza kuchita chilichonse choipa.
Kwa ambiri a iwo, chifukwa chachikulu chimene anakhalira mfiti ndicho kusoŵa zinthu zauzimu ndipo chifukwa chomasulidwa ku chinyengo cha zipembedzo zotchuka. Ponenapo za gulu lake la mfiti, mayi Phyllis Curott, amene ali wansembe wamkulu wa mfiti za chi Wiccan, anati: “Tonsefe sitinakhutire ndi ziphunzitso ndiponso zochita za zipembedzo zimene tinakuliramo.” Curott analongosola kuti mfiti zamakono zimayesa kuyankha mafunso monga akuti, ‘Kodi tingatulukirenso bwanji chopatulika?’ Koma kodi ufiti ndi njira yopita ku mkhalidwe wauzimu weniweni?
Mkhalidwe Wauzimu Weniweni—Umachokera Kuti?
Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona ndiponso Wamphamvuyonse. (Salmo 73:28; 1 Petro 1:15, 16; Chivumbulutso 4:11) Iye akuitana anthu onse kuti amufunefune “ndi kum’peza.” (Machitidwe 17:27) Motero, mkhalidwe wauzimu weniweni ungapezeke kokha mwakukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu woona, Yehova. Zimenezi zingatheke poŵerenga Mawu ake, Baibulo Loyera. Wolemba Baibulo Yakobo akutitsimikizira kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
Komatu, Mawu a Mulungu, amachenjeza kuti pali gwero lina lonyenga la mkhalidwe woipa wauzimu. (1 Yohane 4:1) Limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi, amene ali mdani wamkulu wa Yehova, komanso ziwanda zake ndiwo amachititsa mkhalidwe wauzimu wosocheretsa umene wafala lerowu.c Baibulo limati, Satana ‘wachititsa khungu maganizo’ a anthu ambiri. Kwenikweni iye ‘akunyenga dziko lonse,’ kuphatikizapo anthu amene amachita ufiti—zilibe kanthu kaya amakana kuti salambira Mdyerekezi kapena amavomera kuti amatero. N’chifukwa chiyani zimenezi zili choncho?—2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9.
Zochita ndiponso miyambo yambiri ya ufiti wamakono ndi yofanana kwambiri ndi zochita zoyankhulana ndi mizimu za chipembedzo cha Satana. Motero, ngakhale kungofuna kudziŵa chabe kungachititse kulankhulana ndi mizimu yoipa. Inde, anthu ambiri agonja ndi chikoka choipa cha Satana m’njira imeneyi.
Tisaiwalenso kuti nthaŵi zina anthu ochita ufiti wamakono amakopeka nawo chifukwa chakuti akulakalaka atakhala ndi ulamuliro kapena akufuna kubwezera. “Pali anthu ena amene angadzitche kuti mfiti ndipo n’kugwiritsa ntchito ufitiwu m’njira yoipa kwambiri,” anatero Jennifer, mfiti yamakono. Mulimonsemo, mfiti zimene zimati ndi zabwino komanso zimene zimafuna kubwezera zili pangozi yokhaliratu pansi pa ulamuliro wa Satana ndi ziwanda. Afiti ena angakane kuti zolengedwa zauzimu zoipa zoterezi kulibe, koma akatero ndiye kuti akuzipatsa mphamvu kuti ziwanyenge.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 10:20, 21.
Baibulo limaletsa maula, nyanga, kuchita matsenga, kutsirika, ndi kuchita chilichonse chofuna kulankhulana ndi akufa. Limanena momvekera bwino kuti: “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Inde, Akristu ali ofunitsitsa ‘kuchitira onse chokoma,’ ndipo muutumiki wawo athandiza anthu ambiri kusiya kukhulupirira mizimu m’njira iliyonse. (Agalatiya 6:10; Machitidwe 16:14-18) Komanso, Akristu oona amakana kuchita chilichonse chokhudza chipembedzo chonyenga, kuphatikizapo mtundu uliwonse wa ufiti.—2 Akorinto 6:15-17.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu akuti “chipembedzo chachilengedwe” amatanthauza chikhulupiriro chakuti dziko lapansi ndi zinthu zonse zamoyo zili mbali ya zinthu zauzimu ndi kuti zonse zili ndi mphamvu ya moyo yofanana; mawu akuti “neopaganism” amatanthauza kulambira milungu imene inkalambiridwa kale Chikristu chisanabwere.
b Malingana ndi buku la matanthauzo a mawu lotchedwa American Heritage College Dictionary, a wicca ndi otsatira “chipembedzo chachikunja cha Wicca chimene chimalambira chilengedwe ndipo chinayambira Kummwera kwa Europe nyengo ya Chikristu isanakwane”.
c Nkhani za “Lingaliro la Baibulo” za m’Galamukani! zakhala zikuyankha mafunso monga “Kodi Mdyerekezi Alikodi?” (January 8, 1990, masamba 12-13) ndi “Kodi Ziwanda Zilipodi?” (April 8, 1998, masamba 18-19).
[Chithunzi patsamba 31]
Picture Book of Devils, Demons and Witchcraft/Ernst and Johanna Lehner/Dover