Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 22-23
  • “Sanadziŵa Kanthu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sanadziŵa Kanthu”
  • Dikirani!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumatani Mulungu Weniweniyo Akamakuchenjezani?
  • Kunyalanyaza Machenjezo ndi Kuyesa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mudzalabadira Machenjezo a Tsoka Lomwe Likudzalo?
    Galamukani!—1988
  • Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kumbukirani Mkazi wa Loti
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 22-23

“Sanadziŵa Kanthu”

KUNYALANYAZA machenjezo kungachititse ngozi.

Mu mzinda wa Darwin ku Australia, anthu anali pakalikiliki kukonzekera mapwando a patchuthi mu 1974 pamene kunamveka chenjezo loti kukubwera chimphepo chamkuntho. Koma mzinda wa Darwin unali utakhala zaka pafupifupi 30 usanawonongeke ndi chimphepo cha mkuntho. Ndiye zimenezi zikanachitika bwanji panopa? Anthu ambiri a mumzindawo sanaone kuti analidi pangozi mpaka pamene mphepo yoopsa inayamba kusasula matsindwi ndi kugwetsa makoma a nyumba zimene anthu anabisalamo. Pofika m’maŵa wotsatira, mzindawo unali utawonongekeratu.

Ku Colombia mu November 1985, phiri linaphulika. Madzi oundana atasungunuka anapanga chithope chimene chinakwirira anthu opitirira 20,000 okhala m’tauni ya Armero. Kodi panalibe chenjezo lililonse zimenezi zisanachitike? Phirilo linakhala likunjenjemera kwa miyezi ingapo. Komabe, chifukwa chakuti anali atazoloŵera kukhala pafupi ndi phiri loti limaphulika, anthu ambiri ku Armero sanade nazo nkhaŵa. Akuluakulu a boma anauzidwa kuti kuchitika ngozi posachedwa, koma sanachitepo kanthu kalikonse kuti achenjeze anthu awo. Analengeza pa wailesi mawu olimbikitsa anthu kuti asade nkhaŵa. Anagwiritsa ntchito zokuzira mawu za kutchalitchi kulengeza kuti anthu akhazike mitima yawo pansi. Madzulo amenewo, phirilo linaphulika kaŵiri mochititsa mantha kwambiri. Kodi mukanasiya katundu wanu n’kuthaŵa? Ndi anthu ochepa okha amene anachita zimenezo nthaŵi yoti n’kuthaŵa ikanalipo.

Nthaŵi zambiri akatswiri a nthaka amaneneratu molondola ndithu kumene kuchitike zivomezi. Koma nthaŵi zambiri sanganeneretu molondola nthaŵi imene zichitike. Mu 1999, zivomezi zinapha anthu pafupifupi 20,000 padziko lonse lapansi. Ambiri mwa anthu amene anafawo ankaganiza kuti zimenezo sizingawachitikire.

Kodi Mumatani Mulungu Weniweniyo Akamakuchenjezani?

Baibulo linafotokoza kalekale momveka bwino zinthu zimene zidzachitike m’masiku otsiriza. Mogwirizana ndi zimenezo, limatilimbikitsa kuganizira “masiku a Nowa.” “M’masiku aja, chisanafike chigumula,” anthu anali otanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku, ngakhale kuti mosakayikira ankada nkhaŵa ndi chiwawa chimene chinalipo. Ponena za chenjezo limene Mulungu anapereka kudzera mwa mtumiki wake Nowa, anthuwo “sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:37-39) Kodi inu mukanamvera chenjezolo? Kodi mumamvera panopa?

Bwanji mukanakhala ku Sodomu, pafupi ndi Nyanja Yakufa, m’masiku a Loti, mwana wa mchimwene wake wa Abrahamu? Dziko lake linali ngati paradaiso. Mzindawo unali wotukuka. Anthu ake sankatekeseka ndi chilichonse. M’masiku a Loti, “anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba.” Anthu ake analinso achiwerewere koopsa. Kodi mukanamvera pamene Loti anachenjeza anthu kusiya kuchita makhalidwe oipa? Kodi mukanamvera pamene anakuuzani kuti Mulungu wakonza zowononga mzinda wa Sodomu? Kapena mukanangoziona ngati zocheza, monga momwe anachitira anthu amene akanadzakhala akamwini a Loti? Kodi mwina mukanayamba kuthaŵa, kenaka n’kuyang’ana kumbuyo, ngati mmene anachitira mkazi wa Loti? Ngakhale kuti ena ananyalanyaza machenjezowo, pa tsiku limene Loti anatuluka m’Sodomu, “udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zinawawononga onsewo.”—Luka 17:28, 29.

Masiku ano anthu ambiri sachitapo kanthu. Koma zitsanzo zimenezi zasungidwa m’Mawu a Mulungu monga chenjezo kwa ife, kutilimbikitsa KUDIKIRA!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]

Kodi Panachitikadi Chigumula cha Padziko Lonse?

Anthu ambiri otsutsa amati ayi sichinachitike. Koma Baibulo limati chinachitika.

Yesu Kristu weniweniyo analankhula za Chigumulacho. Iye anali moyo pamene chinkachitika ndipo ankachiona ali kumwamba.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]

Kodi Mizinda ya Sodomu ndi Gomora Inawonongedwadi?

Anthu ofukula m’mabwinja amavomereza zimenezi.

Olemba mbiri yakale amatchula zimenezi.

Yesu Kristu anasonyeza kuti zimenezi zinachitikadi ndipo zimene zinachitikazo zatchulidwa m’mabuku osiyanasiyana 14 a m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena