Nyimbo 46
Yehova ndi Mfumu Yathu
1. Kondwa, lemekeza Yehova.
Kumwamba kulengeza chilungamo.
Timuimbire Mulungu mokondwera
Pa ntchito zake zazikulu.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
2. Nena za kukwezeka kwake,
Za kupulumutsa kwake kwamphamvu.
Yehova ndi Mfumu, Timutamandetu.
Tiyeni, tim’gwadire tonse.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
3. Wakhazikitsatu Ufumu.
Waika Mwana wake pampandowo.
Milungu yonyenga ichite manyazi,
Ulemu wonse n’ngwa Yehova.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu!
(Onaninso 1 Mbiri 16:9; Sal. 68:20; 97:6, 7.)