Nyimbo 136
Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere
Yehova Mulungu wathu,
Ndinu wamuyaya.
Mwapatsa Yesu Ufumu,
Mwa kufuna kwanu.
Ufumu udzalamula
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Zafika tsopano
Ufumu chipulumutso.
Ufumu ‘lamula.
Tipempha kuti “Ubwere.”
Nthawi ya Satana yatha
Dziko latsopano
Lili pafupi kwambiri.
Mavuto adzatha.
Ufumu udzalamula
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Zafika tsopano
Ufumu chipulumutso.
Ufumu ‘lamula.
Tipempha kuti “Ubwere.”
Angelo asangalala,
Aimba mokondwa.
Satana wachotsedwako,
Onse akondwera.
Ufumu udzalamula
Padziko lonse lapansi.
(KOLASI)
Zafika tsopano
Ufumu chipulumutso.
Ufumu ‘lamula.
Tipempha kuti “Ubwere.”
(Onaninso Dan. 2:34, 35; 2 Akor. 4:18.)