Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 26 tsamba 30
  • Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • “Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mauthenga a Ungelo Kaamba ka Tsiku Lathu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 26 tsamba 30
Yesu wakhala pampando wachifumu

GAWO 26

Dziko Lapansi Lidzakhalanso Paradaiso

Kudzera mu Ufumu wa Khristu, Yehova adzayeretsa dzina lake, adzasonyeza kuti iye yekha ndi woyenera kulamulira ndiponso adzathetsa mavuto onse

BUKU la Chivumbulutso, lomwe ndi lomaliza m’Baibulo, lili ndi uthenga wothandiza anthu onse kukhala ndi chiyembekezo. Mtumwi Yohane ndi amene analemba bukuli ndipo muli masomphenya ambiri amene akusonyeza mmene chifuniro cha Yehova chidzakwaniritsidwire.

M’masomphenya oyamba, Yesu amene anali ataukitsidwa anapereka malangizo kumipingo ingapo ndiponso anaiyamikira. Masomphenya otsatira amasonyeza mpando wachifumu wa Mulungu kumwamba, kumene angelo akumutamanda.

Pamene chifuniro cha Mulungu chinapitiriza kukwaniritsidwa, Mwanawankhosa amene ndi Yesu Khristu, analandira mipukutu 7 yokhala ndi zidindo. Pamene zidindo zinamatulidwa pamipukutu inayi yoyambirira, anthu anayi okwera pamahatchi ophiphiritsa anaonekera padziko lapansi. Munthu woyamba anali Yesu, atavala chisoti chachifumu ndipo anakwera pahatchi yoyera. Kenako anthu enawo anaonekera atakwera pamahatchi a mitundu yosiyanasiyana ndipo akuimira nkhondo, njala ndiponso miliri. Zinthu zonsezi zikuchitika m’masiku otsiriza a dziko loipali. Chidindo cha 7 chitamatulidwa, malipenga 7 ophiphiritsa anaimbidwa ndipo zimenezi zinalengeza kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu. Kenako kunachitika miliri 7 yophiphiritsa imene inasonyeza mkwiyo wa Mulungu.

Ufumu wa Mulungu, womwe m’masomphenyawa uli ngati mwana wakhanda wamwamuna, unakhazikitsidwa kumwamba. Kenako nkhondo inayambika ndipo Satana ndi angelo ake oipa anaponyedwa padziko lapansi ndipo panamveka mawu amphamvu akuti: “Tsoka dziko lapansi.” Mdyerekezi ali ndi mkwiyo waukulu chifukwa akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.—Chivumbulutso 12:12.

Yohane anaona Yesu ali kumwamba ndipo ankaoneka ngati mwana wa nkhosa. Kumwambako anali limodzi ndi anthu okwana 144,000 osankhidwa pakati pa anthu. Anthu amenewa “adzalamulira monga mafumu limodzi” ndi Yesu. Choncho buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti mbali yachiwiri ya mbewu yolonjezedwa inapangidwa ndi anthu okwana 144,000.—Chivumbulutso 14:1; 20:6.

Masomphenyawa akusonyeza kuti olamulira osiyanasiyana a dziko lapansi adzasonkhana “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” yotchedwa Aramagedo. Iwo adzamenya nkhondo polimbana ndi Yesu amene anakwera hatchi yoyera uja. Pa nkhondoyi, iye adzatsogolera magulu ankhondo akumwamba. Atsogoleri onse a dzikoli adzawonongedwa, Satana adzamangidwa ndipo Yesu ndi anthu 144,000 aja adzayamba kulamulira dziko lapansi kwa “zaka 1,000.” Zaka zimenezi zikadzatha, Satana adzawonongedwa.—Chivumbulutso 16:14; 20:4.

Kodi Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu ndi olamulira anzake udzachita zotani kwa anthu okhulupirika? Yohane analemba kuti: “[Yehova] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso.

Choncho, buku la Chivumbulutso limamaliza bwino uthenga wa m’Baibulo. Kudzera mwa Ufumu wa Mesiya, dzina la Yehova lidzayeretsedwa ndipo zidzaonekeratu kuti iye yekha ndi woyenera kulamulira mpaka muyaya.

​—Nkhaniyi yachokera m’buku la Chivumbulutso.

  • Kodi anthu okwera mahatchi ophiphiritsa akuimira chiyani?

  • Kodi ndi zinthu zochititsa chidwi ziti zimene zikuchitika pamene cholinga cha Mulungu chikupitiriza kukwaniritsidwa?

  • Kodi Aramagedo n’chiyani, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani?

“BABULO WAMKULU”

M’buku la Chivumbulutso, zipembedzo zonse zonyenga zimene zimatsutsana ndi Mulungu woona zimatchedwa “hule lalikulu.” Hule limeneli limatchedwa “Babulo Wamkulu,” ndipo limachita zachiwerewere ndi maboma andale. Buku la Chivumbulutso limanena kuti nthawi imene Yehova Mulungu waika ikadzakwana, maboma andale amenewa adzaukira hule limeneli ndi kuliwonongeratu.—Chivumbulutso 17:1-5, 16, 17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena