Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 7 tsamba 16-17
  • Kodi Yesu Anali Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Anali Ndani?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chigawo 7
    Mverani Mulungu
  • Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 7 tsamba 16-17

CHIGAWO 7

Kodi Yesu Anali Ndani?

Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi. 1 Yohane 4:9

Yesu ali kudzanja lamanja la Mulungu kumwamba

Ngati tikufuna kukondweretsa Yehova, tiyenera kumvera munthu winanso wofunika kwambiri. Kale kwambiri Yehova asanalenge Adamu, analenga mngelo wamphamvu kwambiri kumwamba.

Mariya ali woyembekezera komanso Yesu atabadwa

Patapita nthawi, Yehova anatumiza mngelo ameneyu kudzabadwa ngati mwana ku Betelehemu kwa namwali wina dzina lake Mariya. Mwana ameneyo anam’patsa dzina lakuti Yesu.​—Yohane 6:38.

Yesu akuphunzitsa anthu za Yehova

Ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Mulungu. Iye anali wachifundo, wachikondi ndiponso anthu ankafika kwa iye momasuka. Ankaphunzitsa anthu choonadi chonena za Yehova mopanda mantha.

Yesu ankachita zinthu zabwino koma anthu ankadana naye. 1 Petulo 2:21-24

Yesu akuukitsa kamtsikana komanso kuchiritsa munthu

Yesu anachiritsanso odwala ndi kuukitsa anthu ena amene anafa.

Atsogoleri a chipembedzo ankadana ndi Yesu chifukwa iye ankaulula zochita zawo zoipa ndipo ankaululanso kuti iwo ankaphunzitsa zinthu zabodza.

Yesu akumenyedwa kenako kuphedwa

Atsogoleri a chipembedzo anachititsa Aroma kuti amenye ndi kupha Yesu.

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira za Yesu?​—Yohane 17:3.

  • Kodi Yesu ankachita chiyani kumwamba asanabwere padziko lapansi?​—Akolose 1:15-17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena