Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 8 tsamba 18-19
  • Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani Bwanji?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chigawo 8
    Mverani Mulungu
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 8 tsamba 18-19

CHIGAWO 8

Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani Bwanji?

Yesu anafa kuti ife tikhale ndi moyo. Yohane 3:16

Azimayi akuyang’ana m’manda a Yesu ndipo sakumuonamo

Patapita masiku atatu Yesu atamwalira, amayi ena anapita kumanda ake ndipo sanapezeko kanthu. Yehova anali ataukitsa Yesu.

Yesu waonekera kwa atumwi ake kenako akupita kumwamba

Kenako Yesu anaonekera kwa atumwi ake.

Inde, Yehova anaukitsa Yesu kuti akhale mngelo wamphamvu ndipo anam’patsa moyo umene sungafe. Ophunzira a Yesu anamuona pamene iye ankapita kumwamba.

  • Kodi “malipiro” a uchimo n’chiyani?​—Aroma 6:23.

  • Yesu anatsegula njira ya kumoyo wosatha.​—Aroma 5:21.

Mulungu anaukitsa Yesu ndipo anamuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Danieli 7:13, 14

Yesu ali pampando kumwamba ndipo akulamulira anthu omwe ali m’Paradaiso padzikoli

Yesu anapereka moyo wake dipo kuti awombole anthu. (Mateyu 20:28) Kudzera mu dipo limenelo, Mulungu wakonza zoti tidzakhale ndi moyo wosatha.

Yehova anasankha Yesu kukhala Mfumu kuti alamulire dziko lapansi. Iye adzalamulira limodzi ndi anthu okhulupirika okwanira 144,000 amene amaukitsidwa kuchokera padziko lapansi kupita kumwamba. Yesu pamodzi ndi anthu 144,000 amenewo adzalamulira m’boma lakumwamba, kapena kuti, Ufumu wa Mulungu.​—Chivumbulutso 14:1-3.

Ufumu wa Mulungu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi. Ndipo sipadzakhalanso nkhondo, chiwawa, umphawi ndiponso njala. Anthu adzakhala osangalala kwambiri.—Salimo 145:16.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso otani?​—Salimo 72.

  • Tiyenera kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti ubwere.​—Mateyu 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena