Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp1 tsamba 48
  • Chitsanzo Chabwino—Yakobo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino—Yakobo
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Nkhani Yofanana
  • Yakobo ndi Esau Akhululukirana
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Amapasa Amene Anali Osiyana
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yakobo Analandira Madalitso
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yakobo Anaona Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
yp1 tsamba 48

Chitsanzo Chabwino​—Yakobo

Yakobo ndi mchimwene wake Esau anatenga nthawi yaitali asanalankhulane. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Esau ankadana kwambiri ndi Yakobo. Ngakhale kuti Yakobo sanalakwitse chilichonse, anachita zonse zomwe akanatha kuti akhazikitsenso mtendere ndi m’bale wake. Cholinga chake sichinali kuti awine mkanganowo koma kuti agwirizanenso ndi m’bale wake. Ngakhale kuti sanasinthe mfundo zimene ankatsatira pa moyo wake, sanakakamize m’bale wakeyo kuti apepese kaye kenako agwirizanenso.​—Genesis 25:27-34; 27:30-41; 32:3-22; 33:1-9.

Kodi inuyo mumatani mukasemphana maganizo ndi m’bale wanu? Nthawi zina mungaone kuti inuyo simunalakwitse chilichonse koma m’bale wanu kapena makolo anu ndi amene alakwitsa. Kodi zimenezi zikachitika mumayembekezera kuti munthu winayo ndi amene akuyenera kuyambitsa zoti mukambirane? Kapena mungatengere chitsanzo cha Yakobo? Ngati nkhaniyo siikukhudza mfundo za m’Baibulo, kodi mudzachita zonse zomwe mungathe kuti mukhazikitsenso mtendere? (1 Petulo 3:8, 9) Yakobo sanalole kuti kunyada kusokoneze banja lawo. Anachita zinthu modzichepetsa ndipo anayambanso kugwirizana ndi m’bale wake. Kodi nanunso mudzayesetsa kukhazikitsa mtendere ndi abale anu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena