Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fg phunziro 10 mafunso 1-4
  • Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Pa Nkhani ya Kulambira Koona
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Mungachipeze Motani Chipembedzo Choona?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
fg phunziro 10 mafunso 1-4

PHUNZIRO 10

Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?

1. Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?

Yesu akuphunzitsa

“Chenjerani ndi aneneri onyenga.”—MATEYU 7:15.

Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chokha, ndipo otsatira ake anali m’chipembedzo chimenecho. Chipembedzocho chili ngati msewu womwe ukulowera ku moyo wosatha. Ponena za msewu umenewu, Yesu ananena kuti: “Amene akuupeza ndi anthu owerengeka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomereza anthu okhawo amene akumulambira mogwirizana ndi mfundo zochokera m’Mawu ake Baibulo, omwe ndi choonadi. Anthu onse omwe ndi olambira oona amakhulupirira zinthu zofanana.​—Werengani Yohane 4:23, 24; 14:6; Aefeso 4:4, 5.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

2. Kodi Yesu ananena chiyani chokhudza Akhristu onyenga?

Mtsogoleri wachipembedzo akulalikira m’tchalitchi. Kenako akudalitsa asilikali amene akupita kunkhondo.

“Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amamukana ndi zochita zawo.”—TITO 1:16.

Yesu anachenjeza kuti aneneri onyenga adzayamba kuphunzitsa zinthu zabodza pakati pa Akhristu. Pamaso chabe, aneneri onyenga amenewa amaoneka ngati amalambira Mulungu m’njira yoyenera. Komanso amanena kuti zipembedzo zawo ndi zachikhristu. Komabe, munthu angathe kuwazindikira kuti si Akhristu oona. Kodi angawazindikire bwanji? Angawazindikire chifukwa chakuti ndi chipembedzo choona chokha chimene anthu ake ndi Akhristu enieni ndipo makhalidwe awo komanso zochita zawo zimakhala zabwino.​—Werengani Mateyu 7:13-23.

3. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mudziwe olambira oona?

Taonani zinthu zisanu zomwe ndi zizindikiro za olambira oona a Mulungu:

  • Olambira oona amalemekeza Baibulo monga Mawu a Mulungu. Iwo amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Choncho chipembedzo choona chimasiyana ndi chipembedzo chimene chimayendera maganizo a anthu. (Mateyu 15:7-9) Komanso olambira oona samangophunzitsa chabe koma amayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amaphunzitsazo.​—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17.

  • Mkhristu akukamba nkhani ya m’Baibulo. Kenako akulalikira zokhudza Uthenga Ufumu, akuthandiza pa ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi tsoka lachilengedwe, akuthandiza okalamba.

    Otsatira a Yesu enieni amalemekeza dzina la Mulungu lakuti Yehova. Yesu analemekeza dzina la Mulungu polidziwikitsa kwa anthu ena. Iye anathandiza anthu ena kudziwa Mulungu komanso anawaphunzitsa kupemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Mateyu 6:9) M’dera limene mukukhala, kodi ndi chipembedzo chiti chomwe chimauza anthu ena za dzina la Mulungu?​—Werengani Yohane 17:26; Aroma 10:13, 14.

  • Akhristu enieni amalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzalalikire uthenga wabwino wa Ufumu. Tsogolo la anthu likudalira pa Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse madalitso ambiri. Yesu ankauza anthu za Ufumu umenewu mpaka pa tsiku la imfa yake. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye ananenanso kuti otsatira ake azilalikira za Ufumuwo. Ndiyeno kodi munthu wina atakupezani n’kumakuuzani za Ufumu wa Mulungu, mungaganize kuti munthu ameneyu ndi wachipembedzo chiti?​—Werengani Mateyu 24:14.

  • Otsatira a Yesu sali mbali ya dziko loipali. Otsatira a Yesu mungawadziwe chifukwa chakuti iwo salowerera nkhani zandale kapena mikangano imene imachitika m’madera amene iwo akukhala. (Yohane 17:16; 18:36) Komanso samatengera makhalidwe ndi maganizo oipa a m’dzikoli.​—Werengani Yakobo 4:4.

  • Akhristu enieni amakondana kuchokera pansi pa mtima. Iwo amaphunzira m’Mawu a Mulungu kuti ayenera kulemekeza anthu a mitundu yonse. Ngakhale kuti zipembedzo zonyenga zakhala zikulowerera nkhondo mayiko osiyanasiyana akamamenyana, olambira oona amakana kuchita zimenezi. (Mika 4:1-3) M’malomwake, Akhristu oona amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chuma chawo kuti athandize ena komanso kuwalimbikitsa.​—Werengani Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20.

4. Kodi tsopano mwachidziwa chipembedzo choona?

Kodi ndi chipembedzo chiti chomwe mfundo zake zonse zimachokera m’Mawu a Mulungu, chimalemekeza dzina la Mulungu komanso chimalalikira zoti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe ungabweretse madalitso kwa a anthu padziko lapansi? Kodi ndi gulu liti la anthu lomwe limakondana kuchokera pansi pa mtima komanso lomwe limakana kumenya nkhondo? Tikukhulupirira kuti mwalidziwa tsopano.​—Werengani 1 Yohane 3:10-12.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena