Phunzirani Zimene Mawu A Mulungu Amanena
Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.
1. Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?
Yesu anaphunzitsa otsatira ake chipembedzo chimodzi chokha choona. Chipembedzo chimenechi chili ngati msewu wopita ku moyo wosatha. Pofotokoza za msewu umenewu, Yesu ananena kuti: “Amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomereza kulambira kumene kumagwirizana ndi Mawu ake omwe ndi choonadi. Choncho Akhristu oona onse amakhulupirira zofanana.—Werengani Yohane 4:23, 24; 14:6; Aefeso 4:4, 5.
2. N’chifukwa chiyani pali zipembedzo zambiri zimene zimati ndi Akhristu?
Aneneri onyenga asokoneza Chikhristu ndipo akuchigwiritsa ntchito pofuna kudzipindulitsa okha. Mogwirizana ndi zimene Yesu analosera, iwo amaoneka ngati “nkhosa” zake koma amachita zinthu ngati mimbulu yolusa. (Mateyu 7:13-15, 21, 23) Chikhristu chonyenga chinakula kwambiri atumwi a Yesu atamwalira.—Werengani Machitidwe 20:29, 30.
3. Kodi kulambira koona kuyenera kuphatikizapo zinthu ziti?
Anthu amene ali m’chipembedzo choona amalemekeza Baibulo ndipo amaliona kuti ndi Mawu a Mulungu. Iwo amayesetsa kutsatira mfundo zake. Choncho chipembedzo choona chimasiyana ndi zipembedzo zimene zimaphunzitsa maganizo a anthu. (Mateyu 15:7-9) Anthu amene ali m’chipembedzo choona amachita zinthu zogwirizana ndi zimene amalalikira.—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17.
Chipembedzo choona chimalemekeza dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Yesu anathandiza anthu kudziwa Mulungu. Anawathandizanso kudziwa dzina la Mulunguyo komanso anawaphunzitsa kuti azipemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Mateyu 6:9) Kudera limene mumakhala, kodi ndi chipembedzo chiti chimene chimalimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?—Werengani Yohane 17:26; Aroma 10:13, 14.
4. Kodi Akhristu oona mungawadziwe bwanji?
Akhristu oona amalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzalalikire za Ufumu. Tsogolo la anthu onse likudalira pa Ufumu wa Mulungu. Yesu ankauza anthu za Ufumu umenewu mpaka pa tsiku la imfa yake. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye anauzanso otsatira ake kuti azilalikira za Ufumu wa Mulungu. Ndiyeno kodi munthu wina atakupezani n’kumakuuzani za Ufumu wa Mulungu, mungaganize kuti munthu ameneyu ndi wachipembedzo chiti?—Werengani Mateyu 10:7; 24:14.
Otsatira a Yesu sali mbali ya dziko loipali. Iwo salowerera nkhani zandale kapena mikangano imene imachitika m’dzikoli. (Yohane 17:16) Komanso, iwo satengera makhalidwe ndi maganizo oipa a m’dzikoli.—Werengani Yakobo 1:27; 4:4.
5. Kodi chizindikiro chachikulu cha Akhristu oona ndi chiyani?
Akhristu oona amakondana kwambiri. Mawu a Mulungu awaphunzitsa kulemekeza anthu amitundu yonse. Ngakhale kuti chipembedzo chonyenga chakhala chikuthandiza kwambiri pa nkhondo za mayiko, anthu a m’chipembedzo choona amakana kuchita nawo zimenezo. (Mika 4:1-4) M’malomwake, amagwiritsa ntchito nthawi yawo, mphamvu zawo komanso ndalama zawo pothandiza anthu ena ndi kuwalimbikitsa, ndipo sachita zimenezi n’cholinga chakuti apeze phindu.—Werengani Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20, 21.
Pali umboni wosonyeza kuti zonse zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa zimachokera m’Baibulo. Kuwonjezera apo, a Mboni amalemekeza dzina la Mulungu, amalalikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse amene anthu ali nawo komanso iwo amasonyeza chikondi chenicheni ndipo sachita nawo nkhondo.—1 Yohane 3:10-12.
Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 16]
“Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amamukana ndi zochita zawo.”—Tito 1:16