MUTU 13
“Chitani Zonse Kuti Zibweretse Ulemerero kwa Mulungu”
MONGA atumiki a Mulungu, zolankhula komanso zochita zathu zonse ziyenera kusonyeza ulemerero wa Mulungu. Mtumwi Paulo anatipatsa mfundo yoti tizitsatira pa nkhaniyi pamene analemba kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akor 10:31) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kutsatira mfundo zolungama za Yehova zomwe zingatithandize kusonyeza makhalidwe ake apamwamba. (Akol. 3:10) Monga anthu oyera, tiyenera kutsanzira Mulungu.—Aef. 5:1, 2.
2 Pofuna kuwasonyeza Akhristu kufunika kokhala oyera, mtumwi Petulo analemba kuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse, chifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Pet. 1:14-16) Mofanana ndi Aisiraeli, anthu onse mu mpingo wachikhristu ayenera kukhala oyera nthawi zonse. Zimenezi zikutanthauza kuti Akhristu ayenera kukhala osadetsedwa ndi zochitika za m’dzikoli. Kuchita zimenezi kumawapangitsa kukhala anthu apadera komanso oyenera kutumikira Mulungu.—Eks. 20:5.
3 Kuti munthu akhale woyera amafunika kupitiriza kutsatira malamulo komanso mfundo za Yehova zimene zimapezeka m’Malemba Oyera. (2 Tim. 3:16) Kuphunzira Baibulo kunatithandiza kumudziwa Yehova komanso zimene amafuna ndipo tinafunitsitsa kukhala naye pa ubwenzi. Kunatithandizanso kuti tizifunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndiponso kuti tiziona kuti kuchita zimene Mulungu amafuna ndi kofunika kwambiri pa moyo wathu. (Mat. 6:33; Aroma 12:2) Kuti tithe kuchita zimenezi, timafunika kuvala umunthu watsopano.—Aef. 4:22-24.
TIYENERA KUKHALA OYERA
4 Nthawi zina kutsatira mfundo zolungama za Yehova kumakhala kovuta. Zimenezi zili choncho chifukwa mdani wathu Satana Mdyerekezi amafuna kutipatutsa pa choonadi. Kuwonjezera pamenepo, timalimbananso ndi zinthu zoipa za m’dzikoli komanso zilakolako za thupi lathu lochimwali. Choncho tiyenera kuchita khama kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Malemba amatiuza kuti tisamadabwe tikamatsutsidwa kapena tikamakumana ndi mayesero chifukwa atumiki a Mulungu ayenera kuvutika chifukwa cha chilungamo. (2 Tim. 3:12) Tiyenera kukhala osangalala tikamakumana ndi mayesero chifukwa mayeserowo amasonyeza kuti tikuchita zimene Mulungu amafuna.—1 Pet. 3:14-16; 4:12, 14-16.
5 Yesu anali wangwiro ndipo ngakhale kuti anakumana ndi mavuto osiyanasiyana, anakhalabe womvera. Iye sanagonjere ngakhale pang’ono mayesero a Satana ndiponso sanakhalepo ndi maganizo a dziko ofuna kutchuka. (Mat. 4:1-11; Yoh. 6:15) Yesu sanalole chilichonse kumusokoneza potumikira Mulungu. Anatsatirabe mfundo zolungama za Yehova ngakhale kuti kukhala wokhulupirikako kunachititsa kuti anthu azidana naye. Atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti nawonso adzadedwa ndi dzikoli. Kungoyambira nthawi imeneyo otsatira a Yesu akhala akuzunzidwa. Koma amalimba mtima chifukwa chodziwa kuti Mwana wa Mulungu anagonjetsa dziko.—Yoh. 15:19; 16:33; 17:16.
6 Kuti ifenso tigonjetse dzikoli, tiyenera kutsatira mfundo zolungama za Yehova ngati mmene anachitira Ambuye wathu. Kuwonjezera pa kusalowerera ndale ndi zochitika za m’dzikoli, tiyeneranso kupewa makhalidwe amene angatiipitse. Timamvera malangizo ofunika kwambiri opezeka pa Yakobo 1:21, akuti: “Siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe lochita zoipa, lomwe ndi losafunika, ndipo vomerezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu, kuti abzalidwe mwa inu.” Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kusonkhana nthawi zonse kungachititse kuti mawu a choonadi ‘abzalidwe’ m’mitima ndi m’maganizo athu, ndipo sitingayambe kusirira zimene anthu m’dzikoli amachita. Yakobo analemba kuti: “Kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu? Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.” (Yak. 4:4) Apa Baibulo likutipatsa malangizo amphamvu otithandiza oti tizitsatira mfundo zolungama za Yehova n’cholinga choti tikhalebe osiyana ndi dzikoli.
7 Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti tisamachite makhalidwe oipa. Amatiuza kuti: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira.” (Aef. 5:3) Choncho sitiyenera kuganizira ngakhale pang’ono za zinthu zolaula kapena zoipa ndipo sitiyeneranso kuzitchula n’komwe pamene tikucheza. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikufunitsitsa kutsatira mfundo zolungama za Yehova za makhalidwe abwino.
UKHONDO
8 Kuwonjezera pa kukhala oyera mwauzimu komanso kukhala ndi makhalidwe abwino, Akhristu amadziwanso kufunika kokhala aukhondo. Mu nthawi ya Aisiraeli, Mulungu yemwe ndi woyera, ankafuna kuti mumsasa muzikhala mwaukhondo. Ifenso tiyenera kukhala aukhondo kuti Yehova ‘asamaone choipa chilichonse pakati pathu.’—Deut. 23:14.
9 Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kukhala oyera mwauzimu ndi kukhala aukhondo. Mwachitsanzo, Paulo analemba kuti: “Okondedwanu, . . . tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akor. 7:1) Choncho Akhristu ayenera kuyesetsa kukhala aukhondo. Ayenera kumasamba ndi kuchapa zovala zawo nthawi zonse. Ngakhale kuti anthu amapeza zinthu mosiyanasiyana, Akhristu amayesetsa kupeza sopo ndi madzi kuti azikhala aukhondo. Amaonetsetsanso kuti ana awo ndi aukhondo.
10 Chifukwa cha ntchito yathu yolalikira, timadziwika kwambiri m’dera limene timakhala. Kukhala ndi nyumba yooneka bwino kunja ndi mkati, kumachititsa kuti tizilalikira mosavuta kwa anthu oyandikana nawo. Aliyense m’banja ayenera kukhala ndi udindo wosamalira nyumba yawo kuti izioneka bwino. Abale ayenera kuonetsetsa kuti m’nyumba ndi panja pakuoneka bwino chifukwa nyumba yooneka bwino imachititsa chidwi anthu ena. Abale akamachita zimenezi komanso akamatsogolera mabanja awo pa zinthu zauzimu, amasonyeza kuti ndi odziwa kuyang’anira bwino mabanja awo. (1 Tim. 3:4, 12) Nawonso alongo ali ndi udindo wosamalira zinthu, makamaka m’nyumba. (Tito 2:4, 5) Ana akaphunzitsidwa bwino amadziwa kudzisamalira komanso kusamalira zipinda zawo kuti zizioneka zaukhondo. Choncho mabanja ayenera kuchita zinthu mogwirizana kuti onse akhale aukhondo chifukwa khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri panopo komanso m’dziko latsopano lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu.
11 Atumiki ambiri a Yehova masiku ano amagwiritsa ntchito njinga kapena magalimoto popita kumisonkhano. M’madera enanso amagwiritsa ntchito zinthu zimenezi popita mu utumiki. Choncho nthawi zonse galimoto kapena njingazo ziyenera kukhala zoyera ndi zokonzedwa bwino. Nyumba, magalimoto ndiponso njinga zathu zizisonyeza kuti ndife anthu a Yehova, aukhondo ndi oyera. Malangizo amenewa akukhudzanso mmene tingasamalirire zikwama zimene timapita nazo mu utumiki komanso Baibulo.
12 Mmene timavalira ndi kudzikongoletsera, ziyenera kugwirizana ndi mfundo za Mulungu. Sitingapite kukaonekera kwa munthu wolemekezeka ngati sitinavale bwino. Ndiye kuli bwanji tikamaimira Yehova mu utumiki kapena papulatifomu? Mmene timaonekera ndiponso masitayilo a zovala zathu zimakhudza mmene ena amaonera kulambira Yehova. Ndiye si bwino kuvala ndi kudzikongoletsa mopitirira malire kapena mosaganizira ena. (Mika 6:8; 1 Akor. 10:31-33; 1 Tim. 2:9, 10) Choncho tikamakonzekera kupita mu utumiki, kumisonkhano yampingo kapena kumisonkhano ikuluikulu, tizikumbukira zimene Malemba amanena pa nkhani ya ukhondo ndi kaonekedwe koyenera. Tikatero tidzalemekeza ndi kutamanda Yehova nthawi zonse.
Monga atumiki a Mulungu, zolankhula komanso zochita zathu zonse ziyenera kusonyeza ulemerero wa Mulungu
13 Tingatsatirenso malangizo amenewa tikamapita kukaona malo kulikulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse kapena maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Tizikumbukira kuti dzina loti Beteli limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Choncho tiyenera kuvala ndi kudzikongoletsa mofanana ndi mmene timachitira tikamapita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu.
14 Tiyeneranso kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera pa nthawi imene tikuchita zosangalatsa. Tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi maonekedwe anga angachititse kuti ndilephere kulalikira kwa anthu amene ndingakumane nawo?’
ZOSANGALATSA ZABWINO
15 Kupuma komanso kuchita zosangalatsa n’kofunika kuti munthu apezenso mphamvu. Tsiku lina Yesu anauza ophunzira ake kuti apite kwaokha n’cholinga choti ‘akapumule pang’ono.’ (Maliko 6:31) Zimenezi zikusonyeza kuti kupuma ndi kuchita zosangalatsa zabwino kungatitsitsimule. Kungatipatse mphamvu kuti tipitirize kugwira ntchito zathu zatsiku ndi tsiku.
16 Popeza masiku ano pali zosangalatsa zambiri, Akhristu ayenera kusankha bwino ndi kugwiritsa ntchito malangizo a Mulungu kuti asankhe zosangalatsa zoyenera. N’zoona kuti zosangalatsa zili ndi ubwino wake, koma sikuti ndi zofunika kwambiri. Timachenjezedwa kuti ‘m’masiku otsiriza,’ ano anthu ndi “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Tim. 3:1, 4) Zosangalatsa zambiri masiku ano zimakhala zosayenera kwa anthu amene amafuna kutsatira mfundo zolungama za Yehova.
17 Akhristu oyambirira ankafunika kuchita khama kuti asatengere makhalidwe oipa a anthu a mu nthawi yawo omwe nthawi zonse ankangofuna zosangalatsa. M’mabwalo a masewera a ku Roma, anthu ankasangalala akamaonerera anthu ena akuzunzidwa. Anthu ambiri ankakondanso kuonera zinthu zachiwawa komanso zachiwerewere koma Akhristu ankapewa zinthu zimenezi. Masiku anonso zosangalatsa zambiri zimakhala zoipa komanso zongofuna kukhutiritsa zilakolako zathupi. Choncho tiyenera ‘kusamala kwambiri’ ndi mmene timayendera, kuti tipewe zosangalatsa zimene zimawononga makhalidwe abwino. (Aef. 5:15, 16; Sal. 11:5) Ngakhale kuti zosangalatsa zina zikhoza kukhala zabwinobwino, nthawi zambiri khalidwe ndi zochita za anthu amene amapezeka kumene zosangalatsazo zimachitikira zimakhala zoipa.—1 Pet. 4:1-4.
18 Pali zosangalatsa zabwino zambiri zimene Akhristu angachite. Malangizo a m’Baibulo komanso opezeka m’mabuku athu athandiza abale ndi alongo ambiri kuti azisankha zosangalatsa zoyenera.
19 Nthawi zina, mabanja ena amaitana Akhristu anzawo kunyumba kwawo kuti adzacheze. Abale ndi alongo enanso angaitanidwe ku ukwati kapena ku zochitika zina. (Yoh. 2:2) Pa zochitika zimenezi, woitana anthuyo ayenera kudziwa kuti ndi udindo wake kuyang’anira zonse zimene zikuchitika pamalopo. Choncho m’pofunika kusamala ngati taitana anthu ambiri chifukwa pamaphwando ngati amenewo, anthu ena amamasuka kwambiri mpaka amafika poiwala makhalidwe abwino achikhristu, n’kuyamba kudya ndi kumwa mosadziletsa, ngakhalenso kuchita zolakwa zina zazikulu. Poganizira zimenezi, Akhristu ozindikira amaona kuti ndi bwino kuitana anthu ochepa ndiponso kuchepetsa nthawi ya phwandolo. Ngati paphwandopo pali mowa, usakhale wambiri ndipo anthu sayenera kumwa mopitirira malire. (Afil. 4:5) Ngati phwando lakonzedwa bwino, limakhala lotsitsimula ndi lolimbikitsa mwauzimu ndipo silichita kufuna kukhala ndi zakudya komanso zakumwa zambirimbiri.
20 Kuchereza anthu ena n’kwabwino kwambiri. (1 Pet. 4:9) Tikamaitanira anthu ena kunyumba kwathu kuti adzadye chakudya, kupuma, kapena kucheza, tizikumbukiranso kuitana anthu osauka a mu mpingo. (Luka 14:12-14) Ngati taitanidwa pa zochitika zoterozo, tiyenera kusonyeza khalidwe labwino, mogwirizana ndi malangizo opezeka pa Maliko 12:31. Ndi bwino kumayamikira zabwino zimene ena atichitira.
21 Akhristu amasangalala ndi mphatso zambiri zochokera kwa Mulungu ndipo amadziwa kuti ayenera ‘kudya, kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti agwira ntchito mwakhama.’ (Mlal. 3:12, 13) Oitana anthu komanso oitanidwa akamachita zinthu “zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu,” amachititsa kuti machezawo akhale osaiwalika komanso olimbikitsa mwauzimu.
ZOCHITIKA ZA KUSUKULU
22 Ana a Mboni za Yehova amapindula ndi maphunziro akusukulu, chifukwa amawathandiza kuti adziwe kuwerenga ndi kulemba. Maphunziro ena akupulayimale komanso kusekondale amawathandiza kuti akwaniritse bwino zolinga zawo zauzimu. Pa zaka zimene ali kusukulu, iwo amayesetsa ‘kukumbukira Mlengi wawo Wamkulu’ poonetsetsa kuti akuika zinthu zauzimu patsogolo.—Mlal. 12:1.
23 Ngati ndinu Mkhristu wachinyamata ndipo muli pa sukulu, mufunika kusamala kwambiri kuti musatengere makhalidwe oipa a achinyamata a m’dzikoli. (2 Tim. 3:1, 2) Yehova amapereka malangizo otiteteza kuti tithe kupewa makhalidwe oipa a dzikoli. (Sal. 23:4; 91:1, 2) Choncho tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo onse amene Yehova amatipatsa kuti tikhale otetezeka.—Sal. 23:5.
24 Kuti akhale osiyana ndi dziko pa nthawi imene ali pa sukulu, achinyamata ambiri a Mboni amasankha kusachita nawo zinthu zina zosakhudzana ndi maphunziro. Kuchita zimenezi kumakhala kovuta kwambiri chifukwa anzawo a m’kalasi komanso aphunzitsi samvetsa chifukwa chake iwo sachita nawo zinthu zina. Komabe kusangalatsa Mulungu ndi komwe kuli kofunika kwambiri. Kuti mukwanitse kuchita zimenezi, muyenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo kuti mutsimikize mtima kusachita nawo mipikisano ya dziko kapena zochitika zina zosonyeza kukonda kwambiri dziko lanu. (Agal. 5:19, 26) Achinyamatanu mukamamvera malangizo a m’Malemba amene makolo anu achikhristu amakupatsani komanso mukamacheza ndi anthu abwino a mu mpingo, mudzatha kutsatira mosavuta mfundo zolungama za Yehova.
NTCHITO NDIPONSO ANTHU OCHEZA NAWO
25 Malemba amasonyeza kuti mitu ya mabanja ili ndi udindo wopezera mabanja awo zinthu zofunika. (1 Tim. 5:8) Komabe ngakhale zili choncho, atumiki a Mulungu amadziwa kuti ntchito si yofunika kwambiri kuposa zinthu za Ufumu. (Mat. 6:33; Aroma 11:13) Chifukwa chokhala odzipereka kwa Mulungu, iwo amakhala okhutira ndi chakudya ndi zovala zimene ali nazo. Zimenezi zimathandiza kuti asamakhale ndi nkhawa komanso kuti asakodwe mu msampha wokonda chuma.—1 Tim. 6:6-10.
26 Akhristu onse odzipereka kwa Mulungu amene ali pa ntchito, ayenera kumatsatira mfundo za m’Malemba nthawi zonse. Ayenera kumakumbukira kuti, kuti apeze zofunika pa moyo wawo, sayenera kuchita zinthu zosemphana ndi malamulo a Mulungu kapena a boma. (Aroma 13:1, 2; 1 Akor. 6:9, 10) Nthawi zonse ayeneranso kusamala ndi anthu amene amacheza nawo. Popeza ndife asilikali a Khristu, timapewa kuchita malonda alionse omwe angatichititse kuphwanya malamulo a Mulungu. Sitilowereranso ndale kapena kuchita chilichonse chimene chingawononge moyo wathu wauzimu. (Yes. 2:4; 2 Tim. 2:4) Ndiponso sitigwirizana ngakhale pang’ono ndi “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga zimene Mulungu amadana nazo.—Chiv. 18:2, 4; 2 Akor. 6:14-17.
27 Kutsatira mfundo zolungama za Yehova kudzatithandiza kuti tisamaone nthawi ya misonkhano yathu ngati nthawi yoti tiziuza ena za malonda athu kapena zinthu zina. Cholinga cha misonkhano yachikhristu, kaya ikhale yampingo, yadera kapena yachigawo, ndi choti tilambire Yehova. Pa nthawiyi timadya chakudya chauzimu komanso ‘kulimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12; Aheb. 10:24, 25) Choncho nthawi imeneyi tiyenera kumakambirana zinthu zauzimu.
AKHRISTU AMAKHALA OGWIRIZANA
28 Yehova amafuna kuti anthu ake amene amatsatira mfundo zake zolungama aziyesetsa ‘kusunga umodzi wawo mwa mzimu, ndi mwamtendere monga chomangira chowagwirizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) M’malo momangochita zinthu zokomera iyeyo, Mkhristu aliyense amayesetsa kuchitira ena zabwino. (1 Ates. 5:15) Mosakayikira, zimenezi ndi zomwenso mumaona zikuchitika mu mpingo wanu. Kaya ndife a fuko lanji, dziko lanji, olemera kapena osauka, ophunzira kapena osaphunzira, tonse timakhala ogwirizana chifukwa timatsatira mfundo zolungama za Yehova. Ngakhale anthu omwe si Mboni amaona khalidwe lapadera kwambiri limeneli la anthu a Yehova.—1 Pet. 2:12.
29 Popitiriza kufotokoza zomwe zimachititsa Akhristu kukhala ogwirizana, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pali thupi limodzi ndi mzimu umodzi, mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi chimene munaitanidwira. Palinso Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, ndi Mulungu mmodzi amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse ndipo amachita zinthu kudzera mwa onse ndiponso mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse.” (Aef. 4:4-6) Zimenezi zikusonyeza kuti atumiki a Mulungu ayeneranso kukhala ogwirizana pa ziphunzitso zoyambirira komanso zozamirapo za m’Baibulo pa nkhani ya kuzindikira ulamuliro wa Yehova. Yehova wapatsa anthu ake chinenero choyera cha choonadi, chimene chimawathandiza kuti azimutumikira mogwirizana.—Zef. 3:9.
30 Anthu onse amene amalambira Yehova amatsitsimulidwa chifukwa cha mtendere komanso mgwirizano umene umapezeka mumpingo wachikhristu. Timaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola.” (Mika 2:12) Tiyenera kutsatira mfundo zolungama za Yehova nthawi zonse kuti tipitirize kukhala mwamtendere komanso mogwirizana.
31 Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala mu mpingo woyera wa Yehova. Komanso kudziwika ndi dzina la Yehova ndi chinthu cha mtengo wapatali kuposa chilichonse chimene tingakhale nacho. Choncho pamene tikupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kuyesetsa kutsatira mfundo zake zolungama komanso kuuza ena mfundozo.—2 Akor. 3:18.