MUTU 18
Anaona Chitsamba Chikuyaka
Mose anakhala ku Midiyani kwa zaka 40. Iye anakwatira n’kukhala ndi ana. Tsiku lina akudyetsa nkhosa pafupi ndi phiri la Sinai, anaona zinthu zodabwitsa. Anaona chitsamba chikuyaka koma sichinkapsa. Atayandikira kuti aone zimene zikuchitika, anamva mawu ochokera m’chitsambacho akuti: ‘Mose! Usayandikire kuno. Vula nsapato zakozo chifukwa malo amene waimawo ndi oyera.’ Yehova ndi amene ankamulankhula ndipo anagwiritsa ntchito mngelo.
Mose anachita mantha kwambiri moti anaphimba nkhope yake. Yehova anamuuza kuti: ‘Ndaona kuti Aisiraeli akuvutika kwambiri. Ndikufuna kuwapulumutsa ku Iguputo n’kuwapititsa kudziko labwino. Iweyo ndi amene uwatsogolere pochoka ku Iguputo.’ Mose ayenera kuti anadabwa kwambiri ndi zimenezi.
Iye anafunsa kuti: ‘Nanga akakandifunsa kuti wakutuma ndi ndani, ndikayankhe kuti chiyani?’ Mulungu anamuuza kuti: ‘Ukawauze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo, ndi amene wandituma kwa inu.’ Kenako Mose anati: ‘Nanga akakapanda kundimvera?’ Yehova anapatsa Mose umboni womutsimikizira kuti adzamuthandiza. Yehova anamuuza kuti aponye ndodo yake pansi. Nthawi yomweyo ndodoyo inasanduka njoka. Koma ataigwira kumchira, inasandukanso ndodo. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukakachita zimenezi, akakhulupirira kuti ndakutumadi.’
Koma Mose anati: ‘Pajatu ine ndimavutika kulankhula.’ Ndiyeno Yehova anamulonjeza kuti: ‘Ineyo ndizikakuuza zoyenera kunena ndipo ndikupatsa m’bale wako Aroni kuti azikakuthandiza.’ Mose atadziwa kuti Yehova amuthandiza, anatenga mkazi ndi ana ake n’kuyamba ulendo wopita ku Iguputo.
“Musadzade nkhawa kuti mudzalankhula bwanji kapena kuti mudzanena chiyani, chifukwa zoti mulankhule mudzapatsidwa nthawi yomweyo.”—Mateyu 10:19