Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 29
  • Chifukwa Chake Mose Akuthawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Mose Akuthawa
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Moyo wa Mose Umakukhudzirani
    Galamukani!—2004
  • Chitsamba Choyaka Moto
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Anaona Chitsamba Chikuyaka
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kodi Mose Anali Munthu Weniweni Kapena Wongopeka?
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 29

NKHANI 29

Chifukwa Chake Mose Akuthawa

MUKUONA Mose’yo akuthawa m’Igupto. Mukuona amuna’wo akum’thamangitsa? Kodi mukudziwa chifukwa chake akufuna kupha Mose? Tiyeni tione ngati tingathe.

Mose anakulira m’nyumba ya Farao, wolamulira wa Igupto. Iye anakhala munthu wanzeru ndi wamphamvu kwambiri. Iye anadziwa kuti sanali Muigupto, koma kuti makolo ake eni-eni anali Aisrayeli.

Tsiku lina, ali ndi zaka 40, Mose analingalira kupita kukaona m’mene mtundu wake unaliri. Kuchitiridwa kwao kunali koopsya. Iye anaona Muigupto akumenya kapolo Wachiisrayeli. Mose anaunguza-unguza, ndipo posaona ali yense, anakantha Muigupto, nafa. Pompo Mose anakwirira mtembo wake mu mchenga.

M’mawa mwake Mose anakaona’nso anthu ake. Iye anaganiza kuti akawathandiza kuti asakhale’nso akapolo. Koma anaona Aisrayeli awiri akumenyana, nati iye kwa wolakwa’yo: ‘Kodi umenyeranji mbale wako?’

Munthu’yo anati: ‘Wakuika ndani kukhala wolamulira ndi woweruza wathu? Kodi ufuna undiphe monga muja unaphera Muigupto uja?’

Mose tsopano anaopa. Anadziwa kuti anthu adziwa zimene iye anachitira Muigupto. Ngakhale Farao anazimva, natumiza anthu kukapha Mose. Ndicho chifukwa chake Mose anafunikira kuthawa mu Igupto.

Mose atachoka mu Igupto, anamka kutali ku Midyani. Kumene’ko anakumana ndi banja la Yetero, nakwatira mwana wake wamkazi mmodzi wochedwa Zipora. Mose anakhala mbusa wa nkhosa woweta nkhosa za Yetero. Kwa zaka 40 iye anakhala m’Midyani. Tsopano anali ndi zaka 80. Tsiku lina, akuyang’anira nkhosa za Yetero, chozizwitsa chinachitika chimene chinasintha moyo wonse wa Mose. tsegulani kutseri’ku, tione chozizwitsa’chi.

Eksodo 2:11-25; Machitidwe 7:22-29.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena