10 MOSE
Anasankha Zinthu Mwanzeru
MOSE sanapatsidwe dzinali ndi makolo ake a Chiheberi, koma anapatsidwa ndi mwana wamkazi wa mfumu amene anamulera. Dzinali limatanthauza kuti “Wovuulidwa M’madzi” chifukwa ndi zomwe zinachitikadi. Iye ankayembekezera kuti Mose adzakhala munthu wolemekezeka m’banja lachifumu ku Iguputo. N’kutheka kuti anasangalala kumuona akulandira maphunziro apamwamba a ku Iguputo. Baibulo limati: “Mose anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo.”
Mose anakula n’kukhala mnyamata wamphamvu. Baibulo limati: “Ankalankhula mwamphamvu ndiponso ankachita zinthu zazikulu.” Iye akanatha kukhala munthu wolemera, wotchuka komanso kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana. Koma anadziwa kuti moyo umenewu sungamuthandize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Choncho anafunika kusankha zoti adzachite ndi moyo wake. Kodi anasankha chiyani?
Zomwe anasankha zinadziwika atakwanitsa zaka 40. Baibulo limati: “Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa limodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita machimo nʼkusangalala kwa nthawi yochepa.” Iye anasankha mwanzeru. Zomwe anasankhazi zimasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro komanso wolimba mtima. Ngakhale zinali choncho, iye analakwitsapo zinthu zina.
Mose ankaona kuti Aisiraeli ndi “abale ake” ndipo ankafuna kuwathandiza chifukwa ankachitiridwa nkhanza. Tsiku lina anapita kuti akaone mavuto omwe anthuwo ankakumana nawo. Kumeneko anaona nzika ina ya ku Iguputo imene mwina inali yoyang’anira antchito, ikumenya kapolo wa Chiheberi. Sitikudziwa ngati Mose anakuwa kuti munthuyo asiye zomwe ankachitazo. Kaya zinthu zinali bwanji, koma Mose “anayangʼana uku ndi uku” mwina kuti aone ngati panali aliyense amene akanathandiza kapoloyo. Koma sanaone aliyense. Choncho anaganiza zoteteza kapoloyo moti “anapha munthu wa ku Iguputoyo.” Kodi anamupha mwadala kapena zinangochitika mwangozi chifukwa chomumenya mwamphamvu? Nkhaniyi siinena chilichonse. Koma Mose anadziwa kuti zake zaipa ndipo anabisa mtembowo mumchenga.
Mawa lake atapitanso, anaona Aheberi awiri akumenyana n’kuyamba kuwalanditsa. Koma mmodzi analankhula mawu omwe anamuchititsa mantha. Iye anafunsa kuti “Ndi ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera nzika ya mu Iguputo ija?” Apa Mose anadziwa kuti anthu amutulukira ndipo anachita mantha kwambiri.
Zinthu sizinachitike mmene iye ankaganizira. Mogwirizana ndi zomwe Baibulo limanena, Mose “ankaganiza kuti abale akewo azindikira kuti Mulungu akuwapulumutsa pogwiritsa ntchito dzanja lake, koma iwo sanaizindikire mfundo imeneyi.” Zikuoneka kuti Mose ankakhulupirira kuti Mulungu anamusankha kuti adzatsogolere Aisiraeli ndi kuwachotsa ku ukapolo ku Iguputo. Koma iye sankadziwa kuti nthawi yake inali isanakwane. Komanso sanamvetse kuti n’chifukwa chiyani Aisiraeli anzakewo sanamuzindikire.
Kodi Mose anasankha chuma ndi kutchuka, kapena anasankha kuthandiza anthu a Yehova?
Mose ankaganiza kuti anali atakonzeka kuti atsogolere anthu a Yehova kuti achoke ku Iguputo. Koma Yehova ankadziwa kuti Mose ankafunikira kumuphunzitsa kaye ngakhale kuti anali wolimba mtima. Mose anali wamphamvu komanso “ankalankhula mwamphamvu.” Komabe ankafunikira kukhala wofatsa, khalidwe lomwe Yehova amasangalala nalo kwambiri. Iye anachita phuma popha nzika ya ku Iguputo ndipo pasanapite nthawi yaitali, Farao anamva zomwe zinachitika.
Popanda kumupatsa mpata woti afotokoze mbali yake, Farao anakonza zoti Mose aphedwe. Choncho Mose anathawa ndipo sanaganizirenso za chuma, moyo wabwino, komanso kutchuka zomwe akanakhala nazo. Anafunikiradi kukhala wolimba mtima kuti akwanitse kuchoka kwawo n’kupita dera lakutali ku Midiyani. Iye anakhala kumeneko monga “mlendo” kwa zaka zambiri. Koma kodi akanalimba mtima kuti akhale munthu wofatsa komanso wodzichepetsa ngati mmene Yehova ankafunira? Tiona ngati anakwanitsadi kuchita zimenezi.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Adakali wachinyamata, kodi Mose anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi ofukula zinthu zakale anapeza umboni wotani wotsimikizira kuti Aisiraeli analidi akapolo ku Iguputo ngati mmene Baibulo limanenera? (w20.03 30) A
Courtesy Brooklyn Museum, gift of Theodora Wilbour
Chithunzi A: Mbali ina ya mpukutu wa ku Iguputo wokhala ndi mayina a akapolo a Chiyuda oposa 40. Umboni woti Aisiraeli analidi akapolo ku Iguputo
2. Kodi Mose anaphunzira chiyani kwa makolo ake, nanga anaphunzira chiyani pamene “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo”? (Mac. 7:22; w02 6/15 10 ¶2-5)
3. Kodi anthu a ku Iguputo ankaika bwanji mtembo wa munthu? Nanga n’kutheka kuti anamva bwanji Mose atapha nzika ya ku Iguputo komanso kubisa mtembo wake m’malo moukonza ndi mankhwala kuti usawonongeke n’kuuika m’manda? (it “Iguputo, Munthu wa ku Iguputo” ¶28-wcgr) B
Chithunzi B: Mtembo wa munthu wa ku Iguputo wokonzedwa ndi mankhwala kuti usawonongeke
4. Mose anathawira ku Midiyani. Kodi Amidiyani ndi Aisiraeli ankafanana pa zinthu ziti? (it “Midiyani” Na. 2 ¶1-2-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi nkhani ya Mose ingakuphunzitseni bwanji kufunika kougwira mtima mukakwiya?
Kodi achinyamata mungaphunzire chiyani kwa Mose pa nkhani ya kulimba mtima mukamasankha zoti mudzachite pa moyo wanu? C
Chithunzi C
Kodi mwaphunziranso njira ina iti yomwe mungakhalire wolimba mtima ngati Mose?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Mose akadzaukitsidwa zokhudza moyo wake ali wachinyamata?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene tingatsanzirire kudzipereka kumene Mose anasonyeza.
Muzitsanzira Anthu a Chikhulupiriro, Osati Opanda Chikhulupiriro—Mose, Osati Farao (2:27)
Mose anasiya moyo wapamwamba kuti ayambe kutumikira Yehova. Kodi zimenezi zingachitikenso masiku ano?