9 SIFIRA , PUWA , AMURAMU , YOKEBEDI NDI MIRIAMU
‘Chifukwa cha Chikhulupiriro Anabisa Mose’
PATADUTSA zaka zoposa 60 Yosefe atamwalira, Aiguputo anali ataiwaliratu za munthu wokhulupirikayu ngakhale kuti Yehova anamugwiritsa ntchito kuwapulumutsa ku njala. Pa nthawiyi, dzikoli linkalamuliridwa ndi Farao wina, koma ankadana kwambiri ndi Aisiraeli chifukwa Yehova ankawadalitsa ndipo anapitiriza kuchuluka. Choncho Farao anasandutsa Aisiraeliwa kukhala akapolo n’kumawachitira nkhanza. Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kuchuluka.
Farao anakonzanso chinthu china choipa kwambiri. Anaitanitsa azamba awiri a Chiheberi, Sifira ndi Puwa ndi kuwalamula kuti akamathandiza azimayi oyembekezera, azipha ana onse aamuna. Tangoganizirani mmene anamvera atauzidwa zimenezi. Koma azimayi olimba mtimawa, “ankaopa Mulungu woona.” Iwo ankadziwa kuti palibe aliyense ngakhale itakhala mfumu yamphamvu bwanji, imene ingawaletse kumvera Yehova Mfumu yachilengedwe chonse. Chifukwa choopa Mulungu, iwo anachita zinthu molimba mtima kwambiri. “Sanachite zimene mfumu ya Iguputo inawauza,” koma anayesetsa kuteteza ana ambiri. Farao anakwiya kwambiri, koma mochenjera iwo sanaulule zomwe ankachita. Yehova ankaona zimene azambawa ankachita ndipo patapita nthawi “anawadalitsa” powapatsa ana awoawo.
Kodi Mose zikanamuthera bwanji zikanakhala kuti azamba, makolo ake komanso mchemwali wake sanasonyeze kulimba mtima?
Farao ataona kuti chiwembu choyambachi chakanika, anakonza zoti Aiguputo azikatayira mumtsinje wa Nailo ana onse aamuna a Chiisiraeli. Pa nthawiyi, banja lina la Chiheberi la Amuramu ndi Yokebedi, linkafunika kusankha zochita pa nkhani yovuta kwambiri. Iwo anali kale ndi ana awiri, Miriamu ndi Aroni. Koma Yokebedi atakhalanso woyembekezera, iwo anadziwa kuti ngati mwana amene ankayembekezerayo anali wamwamuna, ndiye kuti moyo wake unali pangozi. Mwanayo atabadwa anayesetsa kumubisa kwa kanthawi ndithu. Koma sizinali zophweka kubisa mwana wakhanda. Atakwanitsa miyezi itatu, Yokebedi anatenga basiketi yagumbwa nʼkuipaka phula kenako anaikamo mwanayo, n’kukaibisa pakati pa mabango mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo. Koma mwana wake wamkazi Miriamu, anakabisala chapatali kuti aziona zimene zingachitikire mchimwene wakeyo.
Posakhalitsa, mwana wamkazi wa Farao anafika kumtsinjeko kuti akasambe. Iye anaona basiketi ija ndipo anauza kapolo wake kuti akamutengere. Ataitsegula, anapezamo kamwana kakamuna kokongola kakulira ndipo anakamvera chisoni. Iye anaganiza zotenga mwanayo ngati wake, koma anaona kuti pakufunika munthu woti azimuyamwitsa. Nthawi yomweyo Miriamu anadziwa zochita. Anathamangira komweko n’kumuuza kuti akhoza kumupezera munthu woti aziyamwitsa mwanayo ndipo iye anavomera. Kenako Miriamu anakaitana mayi ake. Tangoganizirani mmene Yokebedi anasangalalira atadziwa kuti tsopano azilera mwana wake mopanda mantha, kwinakunso akulandira malipiro. Iye ndi Amuramu anachita zonse zomwe akanatha kuti aphunzitse mwanayo zokhudza Yehova. Ngakhale zinali choncho, nthawi itafika anakapereka mwanayo kwa mwana wamkazi wa Farao ndipo iye anamupatsa dzina lakuti Mose.
Kodi Yehova anadalitsa Amuramu, Yokebedi ndi Miriamu chifukwa cha kukhulupirika kwawo komanso kulimba mtima? N’zosachita kufunsa. Amuramu ndi Yokebedi, anaphunzitsa Miriamu ndi Aroni kuti akhale atumiki okhulupirika a Yehova. Anaonanso kuti Yehova ankateteza Mose. Baibulo silifotokoza ngati makolo a Mose anali adakali moyo pamene mwana wawoyo anakula n’kuyamba kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova. (Eks. 6:20) Koma Miriamu ndi Aroni anaona Yehova akuchita zazikulu pogwiritsa ntchito Mose. Onse atatu anayamba kutumikira limodzi ndipo anasonyeza kuti anali okhulupirika komanso olimba mtima. M’mutu wotsatira, tidzaona mmene Mose anakulira komanso chifukwa chimene anasankhira kuti azitumikira Yehova.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi azamba komanso anthu am’banja la Mose anasonyeza m’njira ziti kuti anali olimba mtima?
Zoti Mufufuze
1. Kodi ofukula zinthu zakale anapeza zotani zomwe zimatsimikizira kuti nkhaniyi inachitikadi? (g04 4/8 20 ¶4–5)
2. Kodi pali umboni wotani wokhudza kuphedwa kwa ana komanso mmene anthu a ku Iguputo ankagwiritsira ntchito gumbwa, zimene zikutsimikizira kuti nkhaniyi inachitikadi? (g04 4/8 6 ¶1-2) A
Christine Osborne Pictures/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Ngakhale masiku ano, anthu amapangabe maboti agumbwa
3. Kodi timadziwa zotani zokhudza azamba a Chiheberi, nanga Yehova anawadalitsa bwanji? (w03 11/1 8 ¶3-4; it “Azamba”-wcgr) B
Chithunzi B
4. Ngakhale atakalamba, kodi Miriamu anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro? (ijwia nkhani 7 ¶14-18)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Amuramu ndi Yokobedi?
Kodi ana am’banja limodzi angaphunzire chiyani pa zomwe Miriamu anachita ali wamng’ono? C
Chithunzi C
Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Sifira ndi Puwa?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzawafunsa chiyani anthu otchulidwa munkhaniyi akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene tingapindulire ndi chitsanzo cha azimayi amene anakana kumvera lamulo la Farao.
“Akazi Amene Anakondweretsa Mtima wa Yehova” (w03 11/1 8-9 ¶3–5)
Timadziwa bwanji kuti Yehova adzapitiriza kusamalira anthu amene amamumvera monga wolamulira m’malo momvera anthu?