Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 44 tsamba 108-tsamba 109 ndime 3
  • Nyumba ya Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyumba ya Yehova
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Solomo Amanga Kachisi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Solomo Anali Mfumu Yanzeru
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Kodi Solomo Ndi Chitsanzo Chabwino Kapena Choipa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 44 tsamba 108-tsamba 109 ndime 3
Moto wochokera kumwamba ukupsereza nsembe yomwe ili paguwa

MUTU 44

Nyumba ya Yehova

Mfumu Solomo

Solomo atakhala mfumu ya Isiraeli, Yehova anamufunsa kuti: ‘Kodi ukufuna ndikupatse chiyani?’ Solomo anayankha kuti: ‘Ndine mwana ndipo sindikudziwa zambiri. Ndipatseni nzeru kuti ndizitha kulamulira bwino anthu anu.’ Yehova anamuyankha kuti: ‘Popeza wandipempha nzeru, ndipangitsa kuti ukhale munthu wanzeru kuposa wina aliyense. Koma ndikupatsanso chuma. Ndipo ukamandimvera, udzakhala ndi moyo wautali.’

Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Anagwiritsa ntchito golide, siliva, mitengo komanso miyala ndipo zonsezi zinali zamtengo wapatali. Panali amuna ndi akazi aluso amene ankagwira ntchito yomanga nyumbayo. Patadutsa zaka 7 ntchito yomangayi inatha ndipo inali nthawi yoti nyumbayo aipereke kwa Yehova. Nyumbayi inali ndi guwa pomwe anaikapo nsembe. Solomo anagwada patsogolo pa guwalo n’kupemphera kuti: ‘Yehova, nyumbayi si yokongola kwambiri komanso si yaikulu kwambiri moti inu n’kukwanamo. Koma tiloleni kuti tizikulambirani m’nyumbayi ndipo muzimva mapemphero athu.’ Kodi Yehova anamva bwanji ndi zimene Solomo ananena m’pempheroli? Solomo atangomaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba n’kupsereza nsembe zonse zimene zinali paguwa zija. Izi zinasonyeza kuti Yehova anasangalala ndi nyumbayi ndipo Aisiraeli ataona zimenezi, anasangalala kwambiri.

Moto wochokera kumwamba ukupsereza nsembe yomwe ili paguwa

Mfumu Solomo ankadziwika mu Isiraeli monse komanso m’madera akutali kuti anali wanzeru. Anthu ankabwera kwa iye kuti adzawathandize pa mavuto awo. Nayonso mfumukazi ya ku Seba inabwera kudzamuyesa pomufunsa mafunso ovuta. Koma itamva mayankho a Solomo inati: ‘Sindinkakhulupirira zimene anthu anandiuza zokhudza inu. Koma panopa ndaona kuti mulidi ndi nzeru kwambiri kuposanso mmene anthuwo ankafotokozera. Yehova Mulungu wanu wakudalitsani kwambiri.’ Zonse zinkayenda bwino ku Isiraeli ndipo anthu ankasangalala. Koma patapita nthawi zinthu zinasintha.

“Tsopano wina woposa Solomo ali pano.”—Mateyu 12:42

Mafunso: N’chifukwa chiyani Yehova anapatsa Solomo nzeru zapadera? Kodi Yehova anatani posonyeza kuti wasangalala ndi nyumbayo?

1 Mafumu 2:12; 3:4-28; 4:29-34; 5:1-18; 6:37, 38; 7:15-51; 8:1-66; 10:1-13; 2 Mbiri 7:1; 9:22

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena