Anachita Chifuniro cha Yehova
Ulendo Umene Unali Wopindulitsa Kwambiri
ULENDO wochokera ku Seba kupita ku Yerusalemu uyenera kuti unali wotopetsa kwambiri kwa mfumu yaikaziyo. Inazoloŵera moyo wa umataya. Tsopano, inali kuyenda pa ngamira ulendo wa makilomita 2,400, mtunda wochuluka wa umenewo anayenda m’chipululu motentha kwambiri. Malinga ndi kuyerekezera kwina, ulendo wake uyenera kuti unatenga masiku mwina ngati 75, popita pokha!a
Chifukwa chiyani mfumu yaikazi yolemera ngati imeneyi inachoka ku nyumba yake yabwino ku Seba ndi kuyenda ulendo wotopetsa ngati umenewu?
Mbiri Yochititsa Chidwi
Mfumu yaikazi ya ku Seba inapita ku Yerusalemu ‘itamva mbiri ya Solomo yakubukitsa dzina la Yehova.’ (1 Mafumu 10:1) Zimene mfumu yaikazi inamva kwenikweni sizinalembedwe. Komabe, tikudziŵa kuti Yehova anadalitsa Solomo ndi nzeru zapadera, chuma, ndi ulemu. (2 Mbiri 1:11, 12) Kodi mfumu yaikazi inadziŵa bwanji zimenezi? Popeza Seba anali pachimake pamalonda, ayenera kuti anamva mbiri ya Solomo kwa amalonda amene ankabwera m’dziko lake. Ena mwa iwo ayenera kuti ankafika ku Ofiri, dziko limene Solomo anachita nalo malonda kwambiri.—1 Mafumu 9:26-28.
Muli monse mmene zinaliri, mfumu yaikazi inafika ku Yerusalemu “ndi ulendo wake waukulu, ngamira zakunyamula zonunkhira, golidi wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali.” (1 Mafumu 10:2a) Ena amati ‘ulendo waukulu’ umenewo unaphatikizapo anthu okhala ndi zida. Izi zingakhale zomveka, popeza kuti mfumu yaikazi inali munthu wolemekezeka kwambiri ndipo inali kuyenda ndi katundu wamtengo wapatali wa ndalama mamiliyoni ambiri zedi.b
Komabe, onani kuti, mfumu yaikazi inamva mbiri ya Solomo “yakubukitsa dzina la Yehova.” Choncho uwu sunali ulendo wokachita malonda chabe. Mwachionekere, mfumu yaikaziyi kwenikweni inapita kuti ikamve nzeru za Solomo—mwinanso kukaphunzira zina za Mulungu wake, Yehova. Popeza iyenera kuti inabadwa kwa Semu kapena Hamu, amene anali alambiri a Yehova, iyenera kuti inali yachidwi ndi chipembedzo cha makolo ake.
Miyambi Yododometsa, Mayankho Okhutiritsa
Atakumana ndi Solomo, mfumu yaikaziyo inayamba kumuyesa ndi “miyambi yododometsa.” (1 Mafumu 10:1) Liwu lachihebri logwiritsidwa ntchito pano lingatanthauze “ndagi.” Koma izi sizitanthauza kuti mfumu yaikaziyo inali kucheza ndi Solomo nkhani zopanda pake. Chosangalatsa n’chakuti, pa Salmo 49:4, liwu lachihebri lomweli likugwiritsidwa ntchito pofotokoza za mafunso ofunika kwambiri okhudza uchimo, imfa, ndi chiwombolo. Choncho, kungakhale kuti mfumu yaikazi ya ku Seba inali kukambirana ndi Solomo nkhani zozama zimene zinayesa kuya kwa nzeru zake. Baibulo limati iye “anakamba naye zonse za m’mtima mwake.” Ndipo Solomo, “anamuyankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamufotokozera iye.”—1 Mafumu 10:2b, 3.
Mfumu yaikazi ya ku Seba inachita chidwi ndi nzeru za Solomo komanso ulemerero wa ufumu wake kotero kuti “anakhululuka malungo.” (1 Mafumu 10:4, 5) Ena amati mawu ameneŵa amatanthauza kuti mfumu yaikaziyo “inabanika.” Katswiri wamaphunziro wina mpakana ananena kuti mwinamwake inakomoka! Zilizonse zimene zinachitikazo, mfumu yaikaziyi inadabwa ndi zimene inaona ndi kumva. Inatcha anyamata a Solomo kukhala odala popeza anali kumva nzeru za mfumu imeneyi, ndipo inayamika Yehova chifukwa chopatsa Solomo ufumu. Kenako mfumu yaikaziyi inapereka kwa mfumuyo mphatso zamtengo wapamwamba, golide yekha wokwana ndalama pafupifupi $40,000,000 malinga ndi ndalama za masiku ano. Nayenso Solomo anapereka mphatso, anapatsa mfumu yaikaziyo ‘chifuniro chake chonse chimene anapempha.’c—1 Mafumu 10:6-13.
Phunziro kwa Ife
Yesu anagwiritsa ntchito mfumu yaikazi ya ku Seba monga chitsanzo kwa alembi ndi Afarisi. “Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa,” iye anawauza choncho, “chifukwa iye anachokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.” (Mateyu 12:42) Inde, mfumu yaikazi ya ku Seba inasonyeza kuyamikira kwambiri nzeru yopatsidwa ndi Mulungu. Ngati inayenda ulendo wa makilomita 2,400 kuti ikamvetsere Solomo, ndithudi alembi ndi Afarisi anayenera kumvetsera Yesu mosamalitsa, amene anali naye pafupi.
Ife lerolino tingasonyeze kuyamikira kwambiri Solomo Wamkulu, Yesu Kristu. Motani? Njira imodzi ndiyo mwa kutsatira chitsogozo chake ‘chophunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19) Njira ina ndiyo kuyang’anitsitsa chitsanzo cha Yesu ndi mkhalidwe wake wa maganizo kenako n’kumatsatira zimenezi.—Afilipi 2:5; Ahebri 12:2, 3.
Ndithudi, kutsatira chitsanzo cha Solomo Wamkulu kumafuna kuyesetsa. Komatu, tidzafupidwa kwambiri. Indedi, Yehova amalonjeza anthu ake kuti ngati asonyeza mzimu wodzimana, iye ‘adzatsegula mazenera a kumwamba, ndi kutsanula madalitso akuti adzasoweka malo akuwalandirira.’—Malaki 3:10.
[Mawu a M’munsi]
a Akatswiri amaphunziro ambiri amakhulupirira kuti Seba anali kumwera chakumadzulo kwa Arabia, dziko limene tsopano likutchedwa Republic of Yemen.
b Malinga ndi kunena kwa Mgiriki wakale wodziŵa za malo a dziko Strabo, anthu a ku Seba anali olemera kwambiri. Akuti anali kugwiritsa ntchito golide mowononga popanga mipando, ziwiya zapanyumba, ngakhalenso makoma, zitseko, ndi madenga a nyumba zawo.
c Ena amati mawu ameneŵa amatanthauza kuti mfumu yaikaziyo inachita chigololo ndi Solomo. Nthano zina zimati mpaka anabereka mwana wamwamuna. Komabe, palibe umboni wochirikiza chilichonse cha zimenezi.