Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 53 tsamba 128
  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yehova Amadalitsa Anthu Amene Amachita Zinthu Molimba Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Mzimayi Woipa Komanso Wodzimva Analangidwa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 53 tsamba 128
Mkulu wa Ansembe Yehoyada akuonetsa anthu Mfumu Yehoasi

MUTU 53

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Yezebeli anali ndi mwana wamkazi dzina lake Ataliya. Mwanayu anali woipa ngati mayi ake. Ataliya anakwatiwa ndi mfumu ya Yuda. Mwamuna wake atamwalira, mwana wake wamwamuna anakhala mfumu. Ndiyeno mwana wakeyo atamwaliranso, Ataliya anayamba kulamulira. Iye anayesetsa kupha anthu onse akubanja lachifumu amene akanalowa ufumu. Anapha ngakhale adzukulu ake ndipo anthu onse ankamuopa kwambiri.

Mkulu wa Ansembe Yehoyada ndi mkazi wake Yehoseba anadziwa kuti zimene Ataliya ankachitazi zinali zoipa. Choncho anatenga Yehoasi, yemwe anali mdzukulu wake wa Ataliya, n’kukamubisa m’kachisi ndipo anakulira kumeneko. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti Ataliya akazindikira akhoza kuwapha.

Yehoasi atakwanitsa zaka 7, Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali ndi Alevi n’kuwauza kuti: ‘Muime pamakomo a kachisi ndipo muonetsetse kuti aliyense asalowe muno.’ Ndiyeno Yehoyada anamuika Yehoasi kukhala mfumu ya Yuda n’kumuveka chipewa chachifumu. Atatero, Ayuda anafuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’

Mfumukazi Ataliya ikukuwa

Ataliya atamva phokoso la anthu, anathamangira kukachisi. Ataona mfumu yatsopanoyo, anafuula kuti: ‘Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!’ Zitatero atsogoleri a asilikali aja anamugwira n’kumutulutsira kunja ndipo anakamupha. Koma Ataliya anali atasocheretsa kwambiri Ayuda.

Yehoyada anathandiza kuti Ayuda achite pangano ndi Yehova ndipo analonjeza kuti azilambira iye yekha. Anawauzanso kuti akagwetse kachisi wa Baala n’kuphwanya mafano onse. Kuwonjezera apo, anasankha ansembe ndi Alevi oti azitumikira pakachisi kuti anthu ayambirenso kulambira Yehova. Ndiponso anaika alonda oti azikhala pageti n’cholinga choti azionetsetsa kuti aliyense wodetsedwa asalowe. Ndiyeno Yehoyada ndi atsogoleri a magulu a asilikali aja anatenga Yehoasi n’kupita naye kunyumba ndipo anamukhazika pampando wachifumu. Ayuda anasangalala kwambiri. Apa tsopano iwo akanatha kulambira Yehova bwinobwino, popanda kuopsezedwa ndi Ataliya kapena kusokonezedwa ndi anthu olambira Baala. Kodi waona mmene kulimba mtima kwa Yehoyada kunathandiza anthu ambiri?

“Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangathe kupha moyo. Mʼmalomwake, muziopa amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe mʼGehena.”​—Mateyu 10:28

Mafunso: Kodi Yehoyada anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima? Kodi ukuona kuti Yehova angakuthandizenso iweyo kuti ukhale wolimba mtima?

2 Mafumu 11:1-21; 12:1-12; 2 Mbiri 21:1-6; 22:10-12; 23:1-21; 24:1-16

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena