Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 33 tsamba 150-tsamba 153
  • Anateteza Mfumu Yosankhidwa ndi Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anateteza Mfumu Yosankhidwa ndi Yehova
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yehova Amadalitsa Anthu Amene Amachita Zinthu Molimba Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 33 tsamba 150-tsamba 153

33 YEHOYADA

Anateteza Mfumu Yosankhidwa ndi Yehova

Losindikizidwa
Losindikizidwa

YEHOYADA anali wachikulire komabe anali wamphamvu. Ankachitabe zambiri potumikira Yehova komanso ankafunitsitsa kuchita zoyenera. Iye anali mtsogoleri wa anthu a Mulungu pa nthawi yovuta ndipo ankatumikira ku Yerusalemu ngati mkulu wa ansembe.

Zoipa zambiri zimene zinkachitika ku Isiraeli, ankachititsa ndi mayi wina dzina lake Ataliya. Iye anali mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli ndipo mayi ake anali Yezebeli. Anthu amenewa anali oipa kwambiri moti Yehova analamula kuti anthu onse amumzere wa mafumu am’banja la Ahabu adzaphedwe. Ngakhale kuti Ataliya anakwatirana ndi mfumu ya ku Yuda ankadana ndi kulambira koona. Mwamuna wake atamwalira, mwana wake anayamba kulamulira monga mfumu. Koma Yehova anamupha. Kenako Ataliya anadziika kukhala mfumu, ngakhale kuti Yehova ankasankha amuna okha kuti azikhala mafumu komanso ankawasankha kuchokera kubanja la Davide. Pofuna kuteteza udindo wake, Ataliya anaganiza kuti aphe aliyense amene akanakhala mfumu. Ena mwa anthu odzakhala mafumu anali adzukulu ake enieni, choncho analamula kuti nawonso aphedwe.

Mkulu wa ansembe ndi mkazi wake anaika moyo wawo pangozi poteteza mwana kuti asaphedwe ndi mfumukazi yoipa

Yehoyada anakwatira mayi wanzeru kwambiri dzina lake Yehoseba. Mayi ameneyu ankadziwikanso kuti Yehosabati ndipo anali wam’banja lachifumu. Iye ndi mwamuna wake sanalole kuti Ataliya aphe ana onse aamuna amumzere wa Davide. Yehova anali atalonjeza kuti mbadwa ya Davide idzalamulira mpaka kalekale. (2 Sam. 7:​12, 13) Choncho Yehoseba anaganiza zoteteza mwana wina yemwe anali mmodzi mwa ana odzalowa ufumu. Mwanayu anali asanakwanitse chaka. Yehoseba anatenga mwanayo ndi mayi amene ankamusamalira n’kupita nawo kwa Yehoyada, mkulu wa ansembe yemwenso anali mwamuna wake. Yehoyadayo anasankha chipinda chinachake m’kachisi chomwe anabisamo mwanayo kuti anthu asamuone.

Mkulu wa ansembe Yehoyada ndi mkazi wake Yehoseba akulowa m’kachisi usiku mozemba ndipo Yehoseba wanyamula Yehoasi ali wakhanda. Iwo alinso ndi mayi wosamalira mwanayo.

Mwanayu dzina lake linali Yehoasi ndipo Yehoyada anakhala akumuteteza komanso kumusunga mwachinsinsi m’nyumba ya Yehova, kwa zaka 6. Nthawi imeneyi inali yoopsa kwambiri chifukwa Ataliya akanangodziwa, bwenzi atapha Yehoyada ndi mkazi wake. Koma kenako nthawi inafika yoti Yehoyada achite zinthu molimba mtima. Iye anaitanitsa akuluakulu 5 a asilikali omwe anali okhulupirika ndipo anawafotokozera kuti pali kamnyamata kena ka m’banja la Davide koyenera kukhala mfumu. Anawauza kuti aike asilikali 500 oti azilondera kachisi komanso malo ozungulira. Asilikaliwo ananyamula zishango ndi zida zina ndipo anazungulira mnyamatayo pamene Yehoyada ankaikidwa kukhala mfumu. Anthu anasangalala komanso kuwomba m’manja ndipo Ataliya anatulukira akuthamanga.

Iye atangofika m’bwalo la kachisi, nthawi yomweyo anazindikira zomwe zinkachitika ndipo anayesetsa kuti Yehoasi asaikidwe kukhala mfumu. Anafuula kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!” Ananena zimenezi ngakhale kuti iyeyo ndi amene anachita chiwembu poyamba. Ngati ankaganiza kuti anthu ena amuthandiza kuti apitirizebe kulamulira, analemba m’madzi. Yehoyada anachita zinthu molimba mtima. Analamula akuluakulu a asilikali kuti atulutse m’kachisi mfumukazi yoipayi n’kupita nayo kunja. Iwo anaitulutsadi ndipo anakaiphera kunjako. Yehova anali atalamula kuti “anthu onse a mʼnyumba ya Ahabu adzaphedwa.” (2 Maf. 9:8) Ndipo mwina Ataliya anali womaliza kuphedwa pa anthu oipa amenewa.

Pambuyo pa zimenezi, Yehoyada anachitanso zinthu zina. Iye anathandiza anthuwo komanso Mfumu Yehoasi kuchita pangano loti adzakhala okhulupirika kwa Yehova. Kenako analamula anthu kuti agwetse kachisi wa Baala komanso kupha ansembe ake. Pambuyo pa zonsezi, Yehoyada anayesetsa kuthandiza Yehoasi kuti akhale mfumu yabwino komanso yokhulupirika. Pa nthawi yonse imene Yehoyada anali ndi moyo, Yehoasi anali wokhulupirika kwa Yehova. Koma kenako Yehoyada anamwalira ali ndi zaka 130. Iye anaikidwa m’manda a mafumu amene analamulira ku Yerusalemu.

N’zomvetsa chisoni kuti Yehoyada atamwalira, Yehoasi anasiya kukhala wokhulupirika. Iye anamvera akalonga a Ayuda omwe anali osakhulupirika ndipo anayamba kulimbikitsa kulambira mafano. Sanamvere aneneri omwe anayesetsa kumuthandiza kuti asinthe. Mmodzi mwa aneneriwa anali Zekariya, mwana wa Yehoyada, yemwe anafunsa anthu onse kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova?” M’malo momvera, Yehoasi analamula kuti Zekariya aphedwe. Koma Zekariya anapitiriza kuchita zinthu molimba mtima ngati bambo ake mpaka imfa yake. Patapita zaka mahandiredi ambiri, Yesu Khristu ananena zabwino zokhudza Zekariya. Mofanana ndi Yehova, Yesu saiwala amuna ndi akazi okhulupirika omwe anali olimba mtima.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • 2 Mafumu 11:​1-21; 12:​1, 2

  • 2 Mbiri 22:​10-12; 23:​1-21; 24:​1, 2, 7, 15-22

  • Mateyu 23:35

Funso lokambirana:

Kodi Yehoyada anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi akatswiri ena amati “asilikali olondera mfumu a Chikariya” amene anathandiza Yehoyada kupha Ataliya anali ndani? (2 Maf. 11:​4, 19; it “Asilikali Olondera Mfumu a Chikariya”-wcgr)

  2. 2. N’chifukwa chiyani Yehoyada anaika “mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu” pamutu pa Yehoasi? (2 Maf. 11:12; w91 2/1 31 ¶5-6-wcgr) A

    Mkulu wa ansembe Yehoyada akuika mpukutu pamutu pa Mfumu Yehoasi.

    Chithunzi A

  3. 3. N’chifukwa chiyani Yehoasi analamula kuti nyumba ya Yehova ikonzedwe? (2 Mbiri 24:​4-7, 11-14; it “Yehoasi” Na. 1 ¶5-wcgr)

  4. 4. Zekariya anali mwana wa Yehoyada. Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu anamutchula kuti mwana wa Barakiya? (“mwana wa Barakiya” mfundo yothandiza pophunzira pa Mat. 23:​35, nwtsty-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • N’kutheka kuti Yehoyada anali ndi zaka 100 pamene anabisa Yehoasi. Kodi chitsanzo chake chingathandize bwanji atumiki a Yehova achikulire? (Sal. 92:​12, 14) B

    M’bale wachikulire, yemwe akugwiritsa ntchito choyendera, akupereka moni kwa mnyamata, amene akulowa m’Nyumba ya Ufumu ndi makolo ake.

    Chithunzi B

  • Zinthu zinkamuyendera bwino Yehoasi pa nthawi yonse imene ankamvera malangizo a Yehoyada. Kodi achinyamata akuphunzirapo chiyani?

  • Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Yehoyada m’njira ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yehoyada akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yehoasi pa nkhani yosankha mwanzeru anthu ocheza nawo?

“Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa” (w09 4/1 24-25)

Onani zimene tingaphunzire kwa Yehoyada pa nkhani ya zopereka zothandizira kulambira koona.

“Zopereka Zimene Zimakondweretsa Mulungu” (w05 11/1 26-27)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena