Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 70 tsamba 166-tsamba 167 ndime 2
  • Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Anabadwa Liti Ndipo Anabadwira Kuti?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Abadwira m’khola
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kubadwa kwa Yesu—Kuti Ndipo Liti?
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Yesu Khristu Tizimukumbukira Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 70 tsamba 166-tsamba 167 ndime 2
Angelo akulengeza kwa abusa za kubadwa kwa Yesu

MUTU 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Pa nthawi ina mu ulamuliro wa Kaisara Augusito, panaperekedwa lamulo loti Ayuda onse abwerere m’mizinda ya kwawo kuti akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu komwe kunali kwawo kwa Yosefe. Apa n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubereka.

Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse zogona alendo ndi zodzaza moti anagona m’khola. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu abadwire m’kholamo. Mariya anakulunga mwanayo ndi nsalu zabwino n’kumugoneka modyetsera ziweto.

Pa nthawiyo, abusa ena ankagona kutchire pafupi ndi ku Betelehemu n’kumayang’anira nkhosa zawo. Mwadzidzidzi, mngelo anafika ndipo pamalo onsewo panawala kusonyeza ulemerero wa Yehova. Abusawo anachita mantha koma mngeloyo anati: ‘Musaope. Ndabwera ndi uthenga wosangalatsa. Lero Mesiya wabadwa ku Betelehemu.’ Nthawi yomweyo, angelo ambirimbiri anaoneka mumlengalenga ndipo ankanena kuti: ‘Alemekezeke Mulungu kumwamba ndipo mtendere ukhale padziko lapansi.’ Kenako angelowo sanaonekenso. Kodi ukudziwa zimene abusawo anachita?

Abusawo anauzana kuti: ‘Tiyeni ku Betelehemu pompanopompano.’ Nthawi yomweyo ananyamuka ndipo atafika anaona Yosefe ndi Mariya ali ndi kamwana kawo m’khola.

Aliyense amene anamva zimene angelowo anauza abusawo anadabwa kwambiri. Mariya anaganizira kwambiri mawu a angelowo ndipo sanawaiwale. Abusawo anabwerera kutchire kuja uku akuthokoza Yehova chifukwa cha zonse zimene anaona.

“Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga koma Iyeyo ndi amene anandituma.”​—Yohane 8:42

Mafunso: Kodi angelo analengeza bwanji za kubadwa kwa Yesu? Kodi abusa aja atafika ku Betelehemu anaona zotani?

Luka 2:1-20; Yesaya 9:6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena