Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 72 tsamba 170-tsamba 171 ndime 2
  • Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Analandira Chitsogozo cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Ankateteza ndi Kusamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Yesu Anakulira ku Nazareti
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 72 tsamba 170-tsamba 171 ndime 2
Yesu ali ndi zaka 12 wakhala pakati pa aphunzitsi m’kachisi

MUTU 72

Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono

Yosefe ndi Mariya ankakhala ku Nazareti. Ankakhala limodzi ndi Yesu komanso ana awo ena aamuna ndi aakazi. Yosefe ankagwira ntchito ya ukalipentala kuti azipeza ndalama zothandizira banja lake. Iye ankaphunzitsanso banja lakelo za Yehova komanso Chilamulo chake. Yosefe ndi banja lake ankapita kusunagoge kukalambira Yehova nthawi zonse. Komanso chaka chilichonse banjali linkayenda ulendo wautali wopita ku Yerusalemu kukachita nawo chikondwerero cha Pasika.

Yesu ali ndi zaka 12, banja lawo linapitanso ku Yerusalemu ngati mmene linkachitira zaka zonse. Ku Yerusalemuko kunali anthu ambirimbiri amene anabwera kudzachitanso chikondwerero cha Pasika. Chikondwererochi chitatha Yosefe ndi Mariya komanso anthu ena anayamba ulendo wobwerera kunyumba. Iwo ankaganiza kuti Yesu ali nawo limodzi. Koma kenako anazindikira kuti Yesu palibe. Anamuyang’ana pakati pa achibale onse koma sanamupeze.

Yosefe ndi Mariya anabwereranso ku Yerusalemu ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamupeze. Kenako anapita kukamuyang’ana m’kachisi. Anamupeza atakhala pakati pa aphunzitsi angapo ndipo ankamvetsera zimene iwo ankanena komanso ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo anachita chidwi kwambiri ndi Yesu moti anayamba kumufunsa mafunso. Koma anadabwa kwambiri ndi mmene iye ankawayankhira. Anazindikira kuti Yesu ankadziwa bwino Chilamulo cha Yehova.

Yosefe ndi Mariya anali ndi nkhawa kwambiri. Atakumana naye, Mariya ananena kuti: ‘Takhala tikukufufuza kwa nthawi yaitali. Unali kuti?’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’

Yesu ananyamuka ndi makolo akewo n’kumapita ku Nazareti. Yosefe anaphunzitsa Yesu ntchito ya ukalipentala. Kodi ukuganiza kuti Yesu ali wamng’ono anali munthu wotani? Pamene iye ankakula nzeru zakenso zinkawonjezeka ndipo ankakondedwa ndi Mulungu komanso anthu.

Yosefe ndi Mariya akhala ndi Yesu komanso azichimwene ndi azichemwali ake a Yesuyo

“Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.”​—Salimo 40:8

Mafunso: Kodi makolo a Yesu anamupeza ali kuti? N’chifukwa chiyani Yesu anapezeka kumeneko?

Mateyu 13:55, 56; Maliko 6:3; Luka 2:40-52; 4:16; Deuteronomo 16:15, 16

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena