Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 82 tsamba 192-tsamba 193 ndime 2
  • Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake Kupemphera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake Kupemphera
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Pankhani ya Mapemphero Amene Mulungu Amamva
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yesu Atiphunzitsa Ife Kupemphera
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Tizipemphera kwa Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 82 tsamba 192-tsamba 193 ndime 2
Mfarisi akupemphera pamalo odutsa anthu ambiri ndipo anthu akuima n’kumamuyang’ana

MUTU 82

Yesu Anaphunzitsa Otsatira Ake Kupemphera

Afarisi ankakonda kuchita zinthu n’cholinga chongofuna kugometsa anthu. Akachitira munthu zabwino, ankafuna kuti aliyense adziwe. Ankakonda kupemphera pamene pamadutsa anthu ambiri kuti anthuwo aziwaona. Komanso iwo ankaloweza mapemphero n’kumawanena m’masunagoge kapena pamphambano n’cholinga choti anthu azimva. Choncho anthu anadabwa pamene Yesu anawauza kuti: ‘Musamapemphere ngati Afarisi. Iwo ankaganiza kuti Mulungu angachite chidwi ndi mapemphero awo aatali. Pemphero ndi nkhani ya pakati pa Yehova ndi munthu amene akupempherayo. Ndiponso musamabwereze zomwezomwezo popemphera. Yehova amafuna kuti muzimuuza zimene zili mumtima mwanu, osati zongoloweza.’

Mnyamata wagwada n’kumapemphera

Yesu ananenanso kuti: ‘Popemphera muzinena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Zofuna zanu zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.”’ Anawauzanso kuti angathe kupempha chakudya cha tsikulo. Komanso angapemphe kuti Mulungu awakhululukire machimo awo ndiponso kuti awathandize pa zinthu zina zokhudza iwowo.

Yesu anati: ‘Musasiye kupemphera. Pitirizani kupempha Atate wanu Yehova kuti akupatseni zinthu zabwino. Makolo amafunitsitsa kupatsa ana awo zinthu zabwino. Mwana wanu atakupemphani chakudya kodi mungamupatse mwala? Komanso ngati atakupemphani nsomba mungamupatse njoka?’

Kenako anati: ‘Ngati inu mumapatsa ana anu zinthu zabwino, ndiye kuli bwanji Atate wanu Yehova? Iye adzakupatsani mzimu woyera. Chofunika ndi kumupempha basi.’ Kodi iweyo umatsatira malangizo a Yesuwa? Kodi ukamapemphera umatchula zinthu ziti?

“Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.”​—Mateyu 7:7

Mafunso: Kodi Yesu ananena chiyani pophunzitsa otsatira ake kupemphera? Kodi ukamapemphera umatchula zinthu zofunika kwa iweyo?

Mateyu 6:2-18; 7:7-11; Luka 11:13

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena