Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 87 tsamba 204-tsamba 205 ndime 3
  • Chakudya Chamadzulo Chomaliza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chakudya Chamadzulo Chomaliza
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Kulabadira Mawu a Yesu Otsazikira
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chakudya Chamadzulo Cha Ambuye
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • M’chipinda Chapamwamba
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 87 tsamba 204-tsamba 205 ndime 3
Yesu akuyambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi atumwi ake okhulupirika 11

MUTU 87

Chakudya Chamadzulo Chomaliza

Ayuda ankachita chikondwerero cha Pasika pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani. Ankachita zimenezi pokumbukira zimene Mulungu anachita powapulumutsa ku Iguputo kuti akakhale m’Dziko Lolonjezedwa. Mu 33 C.E., Yesu ndi atumwi ake anachita mwambowu ku Yerusalemu m’chipinda cham’mwamba. Pomaliza, Yesu ananena kuti: ‘Mmodzi wa inu adzandipereka.’ Atumwiwo anadabwa kwambiri ndipo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukunena ndani?’ Yesu anayankha kuti: ‘Amene ndimupatse mkatewu.’ Kenako anapereka mkate kwa Yudasi Isikariyoti. Nthawi yomweyo Yudasi anatuluka.

Yesu anapemphera ndipo kenako ananyemanyema mkate n’kupereka kwa atumwiwo. Ndipo anati: ‘Idyani mkatewu. Ukuimira thupi langa limene ndidzapereke chifukwa cha inu.’ Kenako anapempheranso n’kupereka vinyo kwa atumwiwo. Ananena kuti: ‘Imwani vinyoyu. Akuimira magazi anga amene ndidzapereke n’cholinga choti machimo a anthu akhululukidwe. Muzichita zimenezi chaka chilichonse pondikumbukira. Ndikukulonjezani kuti tidzakalamulira limodzi kumwamba.’ Kuyambira nthawi imeneyo, otsatira a Khristu amachita mwambo wokumbukira imfa yake chaka chilichonse. Mwambo umenewu umatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.

Atangomaliza mwambowu, atumwiwo anayamba kukangana. Nkhani yake inali yoti wamkulu ndi ndani. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Wamkulu kwambiri pa nonsenu, ndi amene amadziona kuti ndi wamng’ono kwambiri.

‘Inutu ndinu anzanga. Ndimakuuzani chilichonse chimene Atate wanga wafuna kuti ndikuuzeni. Posachedwapa ndipita kumwamba kwa Atate anga. Anthu adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mumakondana. Choncho muzikondana ngati mmene ine ndimakukonderani.’

Pomaliza, Yesu anapempha Yehova kuti ateteze ophunzira ake onse. Anapemphanso kuti awathandize kuti azichita zinthu mogwirizana komanso mwamtendere. Kenako anapempha kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Ndiyeno Yesu ndi atumwiwo anaimba nyimbo zotamanda Yehova kenako anatuluka m’chipindamo. Apa tsopano nthawi yoti Yesu amangidwe inali itayandikira.

“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.”​—Luka 12:32

Mafunso: Kodi Yesu anawalonjeza chiyani atumwi ake? Kodi Yesu anaphunzitsa atumwi ake mfundo zofunika ziti?

Mateyu 26:20-30; Luka 22:14-26; Yohane 13:1, 2, 26, 30, 34, 35; 15:12-19; 17:3-26

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena