Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 92 tsamba 214-tsamba 215 ndime 1
  • Yesu Anakumana ndi asodzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anakumana ndi asodzi
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anaonekera M’mbali Mwanyanja ya Galileya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Ku Nyanja ya Galileya
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kunyanja ya Galileya
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kutumikira Monga Asodzi a Anthu
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 92 tsamba 214-tsamba 215 ndime 1
Yesu akulankhula ndi ophunzira ake uku nsomba zikupsa

MUTU 92

Yesu Anakumana ndi Asodzi

Patapita nthawi kuchokera pamene Yesu anakumana ndi atumwi, Petulo anaganiza zokapha nsomba kunyanja ya Galileya. Tomasi, Yakobo ndi Yohane nawonso anapita naye. Iwo anagwira ntchito yosodza usiku wonse koma sanaphe kalikonse.

Kutacha, anaona munthu wina ataima m’mbali mwa nyanja. Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Koma mwapha nsomba inu?’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi ndithu.’ Ndiyeno anawauza kuti: ‘Ponyani ukonde wanuwo mbali yakumanja.’ Atatero mu ukondemo munadzadza nsomba zambiri moti analephera kuzikokera kumtunda. Nthawi yomweyo, Yohane anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu ndipo anati: ‘Aa eti ndi Ambuye!’ Petulo atangomva zimenezi analumphira m’madzi n’kuyamba kusambira kupita kumtunda. Ophunzira enawo anamutsatira pa ngalawa.

Atafika kumtunda, anapeza nsomba ndi mkate zili pamoto. Yesu anawauza kuti amupatseko nsomba zina kuti awonjezere chakudyacho. Kenako anawauza kuti: ‘Bwerani tidye chakudya cham’mawa.’

Petulo wakumana ndi Yesu ndipo ophunzira ena akubwera

Atatha kudya, Yesu anafunsa Petulo kuti: ‘Kodi umandikonda kuposa ntchito yausodzi?’ Petulo anayankha kuti: ‘Inde Ambuye. Inunso mukudziwa zimenezo.’ Yesu anati: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako Yesu anafunsanso kuti: ‘Petulo, kodi umandikonda?’ Iye anayankha kuti: ‘Ambuye, inu mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu anati: “Weta ana a nkhosa anga.” Ndiyeno anamufunsanso kachitatu ndipo Petulo anamva chisoni n’kuyankha kuti: ‘Ambuye, inu mumadziwa zonse. Mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu ananenanso kuti: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako anamuuzanso kuti: “Pitiriza kunditsatira.”

“[Yesu] anawauza kuti: ‘Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.”​—Mateyu 4:19, 20

Mafunso: Kodi Yesu anachita zinthu ziti zodabwitsa atakumana ndi asodzi? Ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yesu anafunsa Petulo katatu kuti, “Kodi umandikonda?”

Yohane 21:1-19, 25; Machitidwe 1:1-3

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena