Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ku Nyanja ya Galileya
TSOPANO atumwiwo abwerera ku Galileya, monga momwe Yesu adawalangizira kuchita poyamba. Koma iwo sali otsimikizira za chimene ayenera kuchita kumeneko. Patapita nthaŵi, Petro auza Tomasi, Nataniyeli, Yakobo ndi mbale wake Yohane, ndi atumwi ena aŵiri kuti: “Ndinka kukasodza.”
Asanu ndi mmodziwo ayankha nati: “Ifenso tipita nawe.”
Usiku wonse, iwo alephera kugwira kalikonse. Komabe, pamene kuwunika kungoyamba, Yesu awonekera pa gombe, koma atumwiwo sakuzindikira kuti iye ndi Yesu. Iye afuula kuti: “Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi?”
‘Iyayi!’ iwo afuula modutsa madzi.
Iye akunena kuti: “Ponyani khoka ku mbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza.” Ndipo pamene atero, iwo akulephera kukoka khoka lawo chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Yohane akuwa nati, “Ndiye Ambuye.” Petro avala chofunda chake chapamwamba, nadziponya m’nyanja, nasambira pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi kupita ku mtunda. Atumwi ena atsatira m’ngalawa yaing’ono, akumaguza khoka lodzala ndi nsomba.
Pamene afika kumtunda, iko kuli moto wamakala, pomwe pali nsomba, ndipo pali mkate. Yesu akunena kuti: “Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano.” Petro akwera m’ngalawa nakokera khokalo kumtunda. Ilo liri ndi nsomba zazikulu 153!
“Idzani mufisule,” Yesu akuwaitanira.
Palibe ndi mmodzi yemwe wa iwo amene akulimba mtima ndi kufunsa kuti, “Ndinu yani?” chifukwa chakuti iwo akudziŵa kuti ndi Yesu. Uku ndikuwonekera kwake kwachisanu ndi chiŵiri pambuyo pa kuuka, ndipo kwachitatu kwa atumwi ake monga gulu. Iye tsopano akupereka chakudya chofisula, kupatsa aliyense wa iwo mkate ndi nsomba.
Atatsiriza kudya, Yesu mwinamwake agwedezera mutu ku nsomba zambiri zogwidwazo ndikufunsa Petro kuti: “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa [izi, NW]?” Mwinamwake iye akutanthauza kuti, Kodi ndiwe womamatira koposa kumalonda osodza kuposa ndi ntchito imene ndakukonzekeretsa iwe kuchita?
‘Mudziŵa kuti ndikukondani inu,’ Petro akuyankha motero.
“Dyetsa ana a nkhosa anga,” Yesu ayankha motero.
Kachiŵirinso, iye akufunsa kuti: “Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi?”
‘Inde, Ambuye; mudziŵa kuti ndikukondani inu,’ Petro akuyankha.
‘Ŵeta nkhosa zanga,’ Yesu amulamuliranso.
Komabe, kwanthaŵi yachitatu, iye akufunsa kuti: “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine?”
Panthaŵi ino Petro wamva chisoni. Iye angakhale akudabwa kuti Yesu akukaikira kukhulupirika kwake. Ndiiko komwe, pamene Yesu amazengedwa mlandu posachedwapa kaamba ka moyo wake, Petro kwanthaŵi zitatu anamkana iye kuti sanamdziŵa. Chotero Petro akunena kuti: ‘Ambuye, mudziŵa inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani inu.’
“Dyetsa nkhosa zanga,” Yesu akumlamulira kwanthaŵi yachitatu.
Mwakutero Yesu akugwiritsira ntchito Petro monga wokuzira mawu kukhomereza pa enawonso ntchito imene iye akufuna kuti iwo achite. Iye posachedwapa adzalisiya dziko lapansi, ndipo akufuna kuti iwo akhale patsogolo m’kutumikira awo omwe adzaloŵetsedwa m’khola lankhosa la Mulungu.
Monga momwe Yesu anamangidwira ndi kunyongedwa chifukwa chakuti anachita ntchito imene Mulungu anamlamulira iye kuchita, chotero, iye tsopano akuvumbula, kuti Petro adzavutika ndi chokumana nacho chofananacho. “Pamene unali mnyamata,” Yesu akumuuza, ‘unadzimangira wekha m’chiuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.’ Mosasamala kanthu za imfa yophedwera chikhulupiriro yoyembekezera Petro, Yesu amlimbikitsa kuti: ‘Nditsate ine.’
Pocheuka, Petro awona Yohane nafunsa kuti: “Ambuye, koma nanga uyu?”
‘Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza ine,’ Yesu akuyankha, ‘kuli chiyani ndi iwe? Unditsate ine iwe.’
Mawu a Yesu ameneŵa anadzamvedwa ndi ambiri a ophunzirawo kukhala akutanthauza kuti mtumwi Yohane sakafa konse. Komabe, monga momwe mtumwi Yohane pambuyo pake anafotokozera, Yesu sananene kuti iye sakafa ayi, koma Yesu anangonena kuti: ‘Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?’ Yohane 21:1-25; Mateyu 26:32; 28:7, 10.
◆ Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti atumwiwo ngosatsimikizira za chomwe ayenera kuchita ku Galileya?
◆ Kodi atumwiwo amzindikira motani Yesu ku Nyanja ya Galileya?
◆ Kodi ndi nthaŵi zingati zimene Yesu wawonekera tsopano kuyambira pa kuuka kwake?
◆ Kodi Yesu akugogomezera motani chimene iye akufuna kuti atumwiwo achite?
◆ Kodi Yesu akusonyeza motani njira imene Petro adzafera?
◆ Kodi ndi ndemanga zotani za Yesu zonena za Yohane zimene ambiri a ophunzirawo azinamva molakwa?