NYIMBO 71
Ndife Gulu Lankhondo la Yehova
Losindikizidwa
1. Ndife gulu lankhondo
La M’lungu wathu,
Lotsogoleredwa ndi
Mwana wake Yesu.
Ngakhale titsutsidwe
Sitimasiya,
Sitiopa kanthu
Ndife olimba.
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza
Ufumu wayamba
Kulamulira.
2. Ndife anthu a M’lungu.
Tikufufuza
Anthu omwe ndi nkhosa
Zosowa za M’lungu
Ndipo tikawapeza,
Tiwaphunzitse,
Tiwalimbikitse
Tizisonkhana.
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza
Ufumu wayamba
Kulamulira.
3. Ndife gulu lankhondo
Lomvera Yesu,
Lokonzekera nkhondo
Ndi lolimba mtima.
Koma tikhale tcheru
Kuti tisagwe,
Zinthu zikavuta
Tisafooke.
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza
Ufumu wayamba
Kulamulira.
(Onaninso Afil. 1:7; Filim. 2.)