NYIMBO 143
Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso ndi Kudikira
Losindikizidwa
1. Nthawi ya Mulungu wathu
Yayandikira kwambiri
Yoti adzalamulire,
Umboni waoneka.
(KOLASI)
Pitirizani kugwira ntchito
Komanso kukhala maso
Pomwe mukudikira.
2. M’lungu anaika nthawi
Yoti Yesu agonjetse
Adani ake onsewa.
Iye adzapambana.
(KOLASI)
Pitirizani kugwira ntchito
Komanso kukhala maso
Pomwe mukudikira.
3. Mavuto m’chilengedwechi
Akuchuluka kwambiri.
Tiyembekeze Yehova
Adzatipulumutsa.
(KOLASI)
Pitirizani kugwira ntchito
Komanso kukhala maso
Pomwe mukudikira.
(Onaninso Mat. 25:13; Luka 12:36.)