NYIMBO 86
Tiziphunzitsidwa
Losindikizidwa
1. Bwerani mosangalala muphunzire.
“Bwerani mumwe madzi a moyo.”
Nonse anjala bwerani mudye
Ndi kudzalandira malangizo.
2. Tisasiyetu kusonkhana pamodzi.
Tiziphunzitsidwa ndi Mulungu.
Kuno n’kumene kuli abale,
Kuno kuli mzimu wa Mulungu.
3. Lilime lophunzitsidwa choonadi
Limasangalatsa kulimvera.
Tisonkhane ndi anthu a M’lungu.
Tizipezeka pamisonkhano.
(Onaninso Aheb. 10:24, 25; Chiv. 22:17.)