NYIMBO 115
Tizithokoza Kuleza Mtima kwa Mulungu
Losindikizidwa
1. Yehova Mulungu wamphamvu
Mumakonda chilungamo.
Ngakhale zoipa m’dziko
Zikungochulukirabe,
Tikudziwa simukuchedwa
Posachedwa mudzazichotsa.
(KOLASI)
Tikudikira mwachidwi.
Timatamanda dzina lanu.
2. Zaka zambiritu kwa inu
Ndi nthawi yochepa chabe.
Tsiku lanu lalikulu
Layandikira kwambiri.
Anthu ochimwa akalapa
Mumasangalala kwambiri.
(KOLASI)
Tikudikira mwachidwi.
Timatamanda dzina lanu.
(Onaninso Neh. 9:30; Luka 15:7; 2 Pet. 3:8, 9.)