GAWO 3
‘Ndidzakusonkhanitsani Pamodzi’—Mulungu Analonjeza Kuti Adzabwezeretsa Kulambira Koyera
MFUNDO YAIKULU: Maulosi a Ezekieli anasonyeza kuti kulambira koyera kudzabwezeretsedwa
Mpatuko unachititsa kuti zinthu zisokonekere mu Isiraeli ndipo anthu sankagwirizananso. Zonsezi zinkachitika chifukwa choti Aisiraeli anadetsa kulambira koyera komanso ananyoza dzina la Mulungu. Pa nthawi ya mavutoyi, Yehova anauza Ezekieli kuti anene maulosi osiyanasiyana amene anawapatsa chiyembekezo. Yehova anagwiritsa ntchito mawu ochititsa chidwi komanso masomphenya ochititsa mantha kuti alimbikitse Aisiraeli amene anali ku ukapolo komanso anthu onse amene ankafunitsitsa kuti kulambira koyera kubwezeretsedwe.