GAWO 5
“Ndidzakhala Pakati pa Aisiraeli”—Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
MFUNDO YAIKULU: Zinthu zimene zili m’masomphenya a kachisi komanso zimene zinthuzo zikutiphunzitsa zokhudza kulambira koyera
Yehova anapereka masomphenya kwa mneneri Ezekieli komanso mtumwi Yohane amene akufanana m’njira zambiri. Zimene zili m’masomphenyawa zikutiphunzitsa mfundo zofunika kwambiri zimene zingatithandize kuti tizilambira Yehova m’njira yovomerezeka panopa. Komanso zikutithandiza kuona mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso mu Ufumu wa Mulungu.