GAWO 1
“Kumwamba Kunatseguka”
MFUNDO YAIKULU: Tiona mwachidule zokhudza kumwamba kumene Yehova amakhala
Palibe munthu amene angaone Yehova, Mulungu wamphamvuyonse n’kukhalabe ndi moyo. (Eks. 33:20) Koma Yehova anaonetsa Ezekieli masomphenya amene amatithandiza kudziwa mbali yakumwamba ya gulu lake. Masomphenya amenewa amatichititsa mantha komanso amatipangitsa kuti tiziyamikira kwambiri mwayi umene tili nawo wolambira Mulungu woona.