Loweruka
“Kondwerani ndi chiyembekezocho. Pirirani chisautso”—AROMA 12:12
M’MAWA
9:20 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
9:30 Nyimbo Na. 68 ndi Pemphero
9:40 NKHANI YOSIYIRANA: Yehova ‘Amatonthoza Komanso Amapereka Mphamvu’ kwa . . .
Ofooka Komanso Amtima Wachisoni (Aroma 15:4, 5; 1 Atesalonika 5:14; 1 Petulo 5:7-10)
Anthu Ovutika (1 Timoteyo 6:18)
“Ana Amasiye” (Salimo 82:3)
Anthu Achikulire (Levitiko 19:32)
10:50 Nyimbo Na. 90 ndi Zilengezo
11:00 NKHANI YOSIYIRANA: Mangani Nyumba Yolimba
‘Muzikhala Okhutira Ndi Zimene Muli Nazo’ (Aheberi 13:5; Salimo 127:1, 2)
Muziteteza Ana Anu ku “Zinthu Zoipa” (Aroma 16:19; Salimo 127:3)
Muziphunzitsa Ana Anu ‘M’njira Yowayenerera’ (Miyambo 22:3, 6; Salimo 127:4, 5)
11:45 NKHANI YA UBATIZO: ‘Musamaope Chochititsa Mantha Chilichonse’ (1 Petulo 3:6, 12, 14)
12:15 Nyimbo Na. 139 ndi Kupuma
MASANA
1:35 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
1:45 Nyimbo Na. 43
1:50 NKHANI YOSIYIRANA: Muzitsanzira “Anthu Amene Anapirira”
Yosefe (Genesis 37:23-28; 39:17-20; Yakobo 5:11)
Yobu (Yobu 10:12; 30:9, 10)
Mwana Wamkazi wa Yefita (Oweruza 11:36-40)
Yeremiya (Yeremiya 1:8, 9)
2:35 SEWERO: Kumbukirani Mkazi wa Loti—Mbali Yachiwiri (Luka 17:28-33)
3:05 Nyimbo Na. 75 ndi Zilengezo
3:15 NKHANI YOSIYIRANA: Tingaphunzire Kupirira Kuchokera ku Zinthu za M’chilengedwe
Ngamila (Yuda 20)
Mitengo ya M’mapiri Yooneka Ngati Paini (Akolose 2:6, 7; 1 Petulo 5:9, 10)
Agulugufe (2 Akorinto 4:16)
Mbalame Zinazake za M’nyanja Zikuluzikulu (1 Akorinto 13:7)
Mbalame Zinazake Zolimba Mtima (Aheberi 10:39)
Mitengo ya Mthethe (Aefeso 6:13)
4:15 Ananu, Yehova Amasangalala Mukamapirira (Miyambo 27:11)
4:50 Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero Lomaliza