Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 25
  • Kumvetsa Maulosi a Ezekieli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumvetsa Maulosi a Ezekieli
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Nkhani Yofanana
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Mfundo Zachidule za M’buku la Ezekieli
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • “Mapeto Akufikira”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 25
Zithunzi: Kumvetsa Maulosi a Ezekieli. 1. Masomphenya: munthu wamaonekedwe a kopa wanyamula chingwe cha fulakesi ndi bango loyezera. 2. Mafanizo: mphika uli pamoto. 3. Kuyerekezera: Ezekieli akumanga mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira njerwa.

BOKOSI 2A

Kumvetsa Maulosi a Ezekieli

TANTHAUZO​—KODI ULOSI N’CHIYANI?

M’Baibulo mawu a Chiheberi akuti na·vaʼʹ, amene anawamasulira kuti “ulosi,” kwenikweni amatanthauza kuphunzitsa makhalidwe abwino, kupereka uthenga wouziridwa, chiweruzo kapena malamulo ochokera kwa Mulungu. Angatanthauzenso kupereka uthenga wochokera kwa Mulungu, wa zinthu zimene zichitike m’tsogolo. M’maulosi a Ezekieli muli mauthenga a mitundu yonseyi.​—Ezek. 3:10, 11; 11:4-8; 14:6, 7; 37:9, 10; 38:1-4.

MMENE ANKAPEREKERA UTHENGAWO

  • Munthu wamaonekedwe a kopa wanyamula chingwe cha fulakesi ndi bango loyezera.

    MASOMPHENYA

  • Mphika uli pamoto.

    MAFANIZO

  • Ezekieli akumanga mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira njerwa.

    KUYEREKEZERA

M’buku la Ezekieli muli masomphenya, mafanizo, miyambi komanso zinthu zongoyerekezera zomwe zili ndi uthenga waulosi.

KUKWANIRITSIDWA KWAKE

Nthawi zina maulosi amene Ezekieli ananena amakwaniritsidwa m’njira zingapo. Mwachitsanzo, mbali yaing’ono ya maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera, inakwaniritsidwa pamene anthu a Mulungu anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa. Koma mogwirizana ndi zimene zafotokozedwa m’mutu 9 wa buku lino, maulosi ambiri okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera akukwaniritsidwa masiku ano ndipo adzakwaniritsidwanso m’tsogolo.

M’mbuyomu, tinkaona kuti zinthu zina zimene zinatchulidwa m’maulosi a Ezekieli zinkaimira zinthu zinazake. Koma bukuli silinafotokoze kuti munthu, chinthu, malo kapena chochitika chinachake ndi chaulosi ndipo chikuimira chinachake masiku ano pokhapokha ngati pali zifukwa za m’Malemba zonenera zimenezo.a M’malomwake, likufotokoza mmene maulosi ambiri a Ezekieli adzakwaniritsidwire m’njira yaikulu. Likufotokozanso zimene tikuphunzira kuchokera m’mauthenga a Ezekieli komanso kwa anthu, malo ndi zochitika zina zimene iye anatchula.

Bwererani ku mutu 2, ndime 30

a Kuti muone nkhani yofotokoza kuti zinthu zina zinkaimira zinazake, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015, tsa. 9-11, ndime 7-12; komanso “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” tsa. 17-18 m’magazini yomweyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena