BOKOSI 2B
Moyo Wa Ezekieli Komanso Mmene Zinthu Zinalili M’nthawi Yake
Dzina lakuti Ezekieli limatanthauza kuti “Mulungu Amapereka Mphamvu.” Ngakhale kuti m’maulosi ambiri amene Ezekieli ananena muli machenjezo ambiri, uthenga waukulu umene uli m’maulosiwa ndi wogwirizana ndi tanthauzo la dzina lakeli ndipo umalimbitsa chikhulupiriro cha anthu amene akufuna kulambira Mulungu m’njira yoyenera.
ANENERI AMENE ANALIPO M’NTHAWI YA EZEKIELI
YEREMIYA,
ankachokera m’banja la ansembe, anatumikira kwambiri ku Yerusalemu (647-580 B.C.E.)
HULIDA
anatumikira pa nthawi imene buku la Chilamulo linapezeka m’kachisi cha m’ma 642 B.C.E.
DANIELI,
anali wa m’banja lachifumu la fuko la Yuda ndipo anatengedwa kupita ku Babulo mu 617 B.C.E.
HABAKUKU
zikuoneka kuti ankatumikira ku Yuda kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu
OBADIYA
analosera zokhudza Edomu ndipo n’kutheka kuti anachita zimenezi pa nthawi imene Yerusalemu anawonongedwa
KODI ANALOSERA PA NTHAWI ITI? (MADETI ONSE NDI A MU B.C.E.)
ZINTHU ZIKULUZIKULU ZIMENE ZINACHITIKA M’NTHAWI YA EZEKIELI (MADETI ONSE NDI A MU B.C.E.)
cha m’ma 643: Kubadwa
617: Kutengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo
613: Anayamba kulosera; anaona masomphenya a Yehova
612: Anaona masomphenya ampatuko umene unkachitika pakachisi
611: Anayamba kupereka uthenga wachiweruzo kwa Yerusalemu
609: Mkazi wake anamwalira ndipo mzinda wa Yerusalemu unayamba kuzunguliridwa komaliza
607: Analandira uthenga wotsimikizira kuti Yerusalemu wawonongedwa
593: Anaona masomphenya a kachisi
591: Analosera kuti Nebukadinezara adzaukira dziko la Iguputo; anamaliza kulemba
MAFUMU A YUDA NDI BABULO
659-629: Yosiya ankalimbikitsa kulambira koyera koma anakafera kunkhondo pomenyana ndi Farao Neko
628: Yehoahazi anali mfumu yoipa ndipo analamulira kwa miyezi itatu kenako anatengedwa ndi Farao Neko
628-618: Yehoyakimu anali mfumu yoipa ndipo ankalamulira moyang’aniridwa ndi Farao Neko
625: Nebukadinezara anagonjetsa asilikali a ku Iguputo
620: Nebukadinezara anagonjetsa Yuda kwa nthawi yoyamba ndipo anachititsa kuti Yehoyakimu, amene ankalamulira ali ku Yerusalemu, akhale pansi pa ufumu wake
618: Yehoyakimu anagalukira Nebukadinezara koma zikuoneka kuti anamwalira pa ulendo wachiwiri pamene Ababulo analowa m’Dziko Lolonjezedwa
617: Yehoyakini amene ankadziwikanso kuti Yekoniya, anali mfumu yoipa ndipo analamulira kwa miyezi itatu kenako anadzipereka m’manja mwa Nebukadinezara
617-607: Zedekiya amene anali mfumu yoipa kwambiri komanso yamantha, anakhala pansi pa ulamuliro wa Nebukadinezara
609: Zedekiya anagalukira Nebukadinezara amene pambuyo pake anagonjetsa Yuda kachitatu
607: Nebukadinezara anawononga Yerusalemu, anagwira Zedekiya n’kumuchititsa khungu kenako anapita naye ku Babulo