BOKOSI 13A
Akachisi Osiyana Ofotokoza Zinthu Zosiyana
Kachisi Amene Ezekieli Anaona M’masomphenya:
Anafotokozedwa ndi Ezekieli pofuna kuthandiza Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo
Ali ndi guwa lansembe pamene pankaperekedwa nsembe zambiri
Akusonyeza mfundo zolungama zimene Yehova amafuna kuti tizitsatira pomulambira
Akutithandiza kumvetsa kubwezeretsa kwauzimu kumene kunayambika mu 1919
Kachisi Wamkulu Wauzimu:
Anafotokozedwa ndi Paulo m’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi
Ali ndi guwa lansembe pamene panaperekedwa nsembe imodzi “kamodzi kokha” (Aheb. 10:10)
Akufotokoza za kulambira Yehova m’njira yovomerezeka kudzera mu nsembe ya dipo ya Khristu zomwe zinkaimiliridwa ndi chihema komanso akachisi
Amatithandiza kumvetsa ntchito imene Khristu anagwira monga Mkulu wa Ansembe wamkulu kuchokera mu 29 mpaka 33 C.E.