PHUNZIRO 17
Kulankhula Zomveka
1 Akorinto 14:9
MFUNDO YAIKULU: Muzilankhula m’njira yoti anthu azimvetsa zimene mukunena.
MMENE MUNGACHITIRE:
Yesetsani kuti muidziwe bwino nkhani yanu. Mukaidziwa bwino nkhani yanu mukhoza kuifotokoza mosavuta m’mawu anuanu.
Muzigwiritsa ntchito ziganizo zifupizifupi zosavuta kumva. Ngakhale kuti pena mukhoza kugwiritsa ntchito ziganizo zitalizitali, muzizidula moyenerera mukamafotokoza mfundo yofunika.
Muzifotokoza mawu ovuta. Pewani kugwiritsa ntchito mawu amene anthu sawadziwa. Muzifotokozera mawu ovuta, anthu a m’Baibulo osadziwika kwambiri komanso miyeso ndi zikhalidwe zakale.