PHUNZIRO 41
Lankhulani Zomveka Bwino kwa Ena
PAMENE mulankhula, musangopereka mfundo zokha. Yesetsani kumveketsa bwino kwa omvera anu zimene mukunena. Zimenezi zingakuthandizeni kulankhula mogwira mtima, kaya mukulankhula pamaso pa mpingo kapena kwa anthu amene si Mboni.
Pali njira zosiyanasiyana zothandiza kuti kulankhula kuzimveka bwino. Zina tazifotokoza mu Phunziro 26 lakuti, “Kukamba Nkhani M’njira Yotsatirika.” Njira zina tazifotokoza mu Phunziro 30 lakuti, “Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo.” Mu Phunziro lino, tikambirananso mfundo zingapo zowonjezera.
Mawu Osavuta, Kalankhulidwe Kosavuta. Mawu osavuta komanso masentensi afupiafupi ndi zida zamphamvu pothandiza kulankhulana mogwira mtima. Ulaliki wa Yesu wa pa Phiri ndi chitsanzo chabwino koposa cha nkhani imene anthu onse akhoza kumva mosavuta, mosasamala kanthu kuti ndi anthu otani kapena amakhala kuti. Malingalirowo angakhale atsopano kwa iwo. Komabe atha kumva zimene Yesu ananena chifukwa analankhula zinthu zotikhudza tonse: mmene tingapezere chimwemwe, mmene tingakhalitsirane bwino wina ndi mnzake, mmene tingathanire ndi nkhaŵa, ndi mmene tingakhalire ndi moyo watanthauzo. Ndipo pofotokoza maganizo ake anagwiritsa ntchito mawu osavuta. (Mat., macha. 5-7) Inde, Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri zosonyeza kusiyanasiyana kwa masentensi, mu utali ndi kapangidwe kake. Cholinga chanu chachikulu chiyenera kukhala kufotokoza malingaliro anu m’njira yosavuta ndi yomveka bwino.
Ngakhale pamene mukamba nkhani yozama kwambiri, kulankhula mwa njira yosavuta kungathandize kuti nkhaniyo imveke bwino. Kodi mungalankhule motani m’njira yosavuta? Musapanikize omvera anu mwa kuwafotokozera zinthu zambirimbiri zosafunika kwenikweni. Sanjani mfundo zanu m’njira yakuti zithandizire mfundo zazikulu. Sankhani mosamala malemba ofunika kwambiri. M’malo mongoŵerenga lemba kenako n’kupita pa lina, ŵerengani malemba ndi kuwafotokoza bwinobwino. Musaphimbe lingaliro lofunikira ndi mawu ambiri.
Pamene mupangitsa phunziro la Baibulo, tsatirani njira zimenezo. Musayese kufotokoza zinthu zonse. Thandizani omvera anu kumvetsa malingaliro aakulu. Mbali zinazo adzazidziŵa kudzera m’phunziro laumwini ndi misonkhano ya mpingo.
Kuti mukambe nkhani m’njira yosavuta kumva, muyenera kukonzekera bwino. Muyenera kuimvetsa bwino nkhani yanu inumwini kotero kuti mukaimveketse bwino kwa ena. Ngati chinthu mwachimvetsa bwino, mumatha kupereka zifukwa zimene chinthucho chili choncho. Mumathanso kuchifotokoza m’mawu anuanu.
Fotokozani Mawu Achilendo. Nthaŵi zina pofuna kumveketsa zinthu muyenera kufotokoza tanthauzo la mawu osazoloŵereka kwa omvera anu. Musaone ngati omvera anu amadziŵa zonse, komanso musawaone ngati alibe luntha lozindikira zinthu. Chifukwa cha kuphunzira kwanu Baibulo, nthaŵi zina mungatchule mawu omwe angamveke achilendo kwa anthu ena. Popanda kuwafotokozera, anthu osadziŵa bwino Mboni za Yehova sangazindikire kuti mawu akuti “otsalira,” “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” “nkhosa zina,” ndi “khamu lalikulu” amatanthauza magulu akutiakuti a anthu. (Aroma 11:5; Mat. 24:45; Yoh. 10:16; Chiv. 7:9) Mofananamo, ngati munthu salidziŵa bwino gulu la Mboni za Yehova, sangadziŵe tanthauzo la mawu ngati “wofalitsa,” “mpainiya,” “woyang’anira dera,” ndi “Chikumbutso.”
Mawu ena a m’Baibulo amene ngakhale anthu omwe si Mboni amawagwiritsa ntchito, angafunikire kuwafotokoza. Kwa anthu ambiri, “Armagedo” imatanthauza chiwonongeko cha nyukiliya. “Ufumu wa Mulungu” kwa iwo ndi mtima wa munthu kapena kumwamba, osati boma. Akamva mawu akuti “mzimu” amaganiza za mbali ya munthu imene amati siifa munthu akamwalira. Malinga ndi zimene mamiliyoni a anthu aphunzitsidwa, “mzimu woyera” ndi munthu; amati ndi mbali imodzi ya Utatu Woyera. Chifukwa chakuti anthu ambiri asiya makhalidwe a m’Baibulo, angafunikire kuwathandiza kuti azindikire ngakhale chimene Baibulo limatanthauza pamene limati: “Thaŵani dama.”—1 Akor. 6:18.
Ngati anthuwo ndi oti saŵerenga Baibulo nthaŵi zonse, sangadziŵe amene mukutanthauza ngati mungonena kuti, “Paulo analemba kuti . . .” kapena “Luka anati . . .” Iwo angakhale ndi mabwenzi kapena anansi a mayina amenewo. Mungachite bwino kuwonjezera mawu ena odziŵitsa kuti munthuyo anali mtumwi wachikristu kapena wolemba Baibulo.
Anthu a masiku ano nthaŵi zambiri amafunikira kuwathandiza kumvetsa malemba amene ali ndi miyeso kapena zizoloŵezi zamakedzana. Mwachitsanzo, sangatolepo kanthu kwenikweni pa mawu akuti, chingalawa cha Nowa chinali mikono mazana atatu m’litali mwake, mikono makumi asanu m’mimba mwake, mikono makumi atatu m’msinkhu mwake. (Gen. 6:15) Koma ngati mungatchule miyeso imeneyo m’njira zamakono, omvera anu angakhale msanga ndi chithunzi cha ukulu wa chingalawacho.
Perekani Mafotokozedwe Ofunikira. Kuti nkhani yanu imveke bwino kwa omvera anu, mungafunikirenso kupereka mafotokozedwe ena kuwonjezera pa kumasulira tanthauzo la mawu. M’masiku a Ezara ku Yerusalemu, anali kuti akaŵerenga Chilamulo panali kukhalanso kufotokozera mbali zina zofunika. Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa zinthu, Alevi anafotokoza Chilamulo ndi cholinga chake malinga ndi mikhalidwe ya panthaŵiyo. (Neh. 8:8, 12) Mofananamo, fotokozani mofatsa malemba amene mukuŵerenga ndi kusonyeza cholinga chake.
Yesu atamwalira ndi kuuka, anafotokozera ophunzira ake kuti zimene zinamuonekerazo zinakwaniritsa Malemba. Anatsindikanso udindo wawo wokhala mboni za zinthu zinachitikazo. (Luka 24:44-48) Mukathandiza anthu kuona mmene zimene aphunzira zimakhudzira miyoyo yawo, amazindikira msanga tanthauzo lake.
Zimadaliranso Mtima wa Munthu. Mafotokozedwe anu angakhale omveka bwino lomwe, koma kuti munthuyo amvetse zimadaliranso mbali zina. Ngati mtima wa munthu sulabadira, umakhala chopinga pa kuzindikira kwake zimene mukunena. (Mat. 13:13-15) Kwa aja oumirira kuona zinthu mwakuthupi, zinthu zauzimu amaziona kukhala zopusa zokhazokha. (1 Akor. 2:14) Ngati munthu asonyeza mzimu umenewo, chinthu chanzeru ndi kuleka kukambirana naye—mwina mungadzayesenso m’tsogolo.
Komabe, nthaŵi zina mtima umakhala wosalabadira chifukwa cha mikhalidwe yovuta ya moyo. Atakhala ndi mpata womvera choonadi cha Baibulo kwa nthaŵi yakutiyakuti, mtima wa munthu wotero ungayambe kulabadira. Yesu atauza atumwi ake kuti iye akakwapulidwa ndi kuphedwa, iwo sanamvetse. Chifukwa chiyani? Si zimene anayembekezera ndiponso si zimene anafuna m’pang’ono pomwe! (Luka 18:31-34) Komabe m’kupita kwa nthaŵi, 11 mwa ophunzira ake anamvetsa, ndipo anasonyeza zimenezo pochita mogwirizana ndi zimene Yesu anali atawaphunzitsa.
Mmene Chitsanzo Chabwino Chimathandizira. Chimene chimathandiza anthu kumvetsa si mawu athu okha, komanso zochita zathu. Ponena za nthaŵi yawo yoyamba pa Nyumba ya Ufumu, anthu ambiri amati amakumbukira chikondi chimene anaona, osati zimene anamva. Mofananamo, chimwemwe chimene timasonyeza chathandiza eninyumba ambiri kulabadira choonadi cha Baibulo. Anthu ena poona chikondi chimene anthu a Yehova amasonyezana ndi kuthandizana pakaoneka zovuta, atsimikiza okha kuti Mboni zilidi ndi chipembedzo choona. Choncho, pamene mukuyesetsa kuthandiza anthu kumvetsa choonadi cha m’Baibulo, lingalirani njira imene mumachifotokozera ndi chitsanzo chimene mumapereka.