Phunziro 35
Kugwirizanitsa Nkhani ndi Utumiki Wakumunda
1-3. N’chifukwa chiyani kuli kopindulitsa kuphunzira kugwirizanitsa nkhani ndi utumiki wakumunda?
1 Mbali yaikulu ya ntchito yathu monga atumiki achikristu lerolino ndiyo kulalikira ndi kuphunzitsa Mawu a Mulungu kwa anthu odziŵa zochepa kwambiri ponena za Baibulo. Ena a iwo sanakhalepo nalo n’komwe; ena ali nalo koma limangokhala pashelefu. Zimenezi zikutanthauza kuti, kuti iwo apindule kwenikweni ndi nkhani imene tikuwauza, tiyenera kugwirizanitsa nkhaniyo ndi mikhalidwe yawo. Osati kuti tisinthe uthengawo, koma kuti tiyesetse kulankhula m’mawu amene iwo angathe kumva bwino. Kwenikweni, kukonza nkhani yathu m’njira imeneyi kumasonyezanso kuti ifenso eniakefe taimvetsa bwino nkhaniyo.
2 Kugwirizanitsa kumene tikunena pano kumatanthauza kusinthira ku mikhalidwe yatsopano kuti pakhale kuyenerana kwabwino. Kumatanthauza kukonza chinthu china m’njira yakuti chikukhutiritseni kapena kuti chikhutiritse munthu wina. Kupenda mfundo yogwirizanitsa nkhani ndi utumiki wakumunda kuyenera kuonetsanso kufunika kopangitsa maulaliki a mu utumiki wakumunda kapena nkhani iliyonse kukhala yosavuta ndi yomveka kwa omvetsera, makamaka kwa atsopano amene tikumana nawo mu utumiki wakumunda. Chifukwa cha chimenecho, posonyeza luso limeneli m’sukulu, nthaŵi zonse muyenera kuona omvetsera anu mmene mumaonera anthu amene mumakumana nawo mu umboni wa kunyumba ndi nyumba.
3 Zimenezo sizitanthauza kuti pofuna kuonetsa luso limeneli papulatifomu, nkhani yanu muikambe ngati ulaliki wa kukhomo ndi khomo ayi. Nkhani zonse ziyenera kukambidwa motsatira malangizo ake a sukuluyo. Zimenezo zikutanthauza kuti, mosasamala kanthu za mtundu wa nkhani imene mukuilankhula, mfundo zimene mukuzifotokoza komanso mawu amene mukuwagwiritsa ntchito akhale oti mutha kuwagwiritsa ntchito kwa anthu amene mukumana nawo m’munda. Popeza kuti mbali yaikulu ya kulankhula kwathu timaichita mu utumiki wakumunda, zimenezi ziyenera kukuthandizani kuona kufunika kwa kulankhula m’njira yosavuta kumva, m’mawu amene anthu ambiri atha kumva pamene tili mu utumiki wakumunda. Luso limeneli mwalikonzekerapo m’Phunziro 21. Koma tsopano likupendedwa palokha chifukwa cha kufunika kwake kwakukulu.
4, 5. Fotokozani chifukwa chake tiyenera kumveketsa bwino mawu athu kwa anthu.
4 Kumveketsa mawu kwa anthu. Kufunika kwa luso limeneli kumaoneka mwa mawu amene abale ena amawagwiritsa ntchito mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi pamaphunziro atsopano. Kuzindikira kwathu Malemba kwatiphunzitsa mawu ena amene anthu ambiri sawadziŵa. Timatchula mawu akuti “otsalira,” “nkhosa zina,” ndi ena otero. Ngati tiwagwiritsa ntchito polankhula ndi anthu amene tikumana nawo mu utumiki wakumunda, mawu oterowo kaŵirikaŵiri sapereka tanthauzo lililonse kwa iwo. M’pofunika kuti tiwamveketse bwino mwa kugwiritsa ntchito mawu ena ofanana matanthauzo kapena tiwafotokoze kuti anthuwo awazindikire. Ngakhale kunena za “Armagedo” kapena “kukhazikitsidwa kwa Ufumu” sikutanthauza kanthu kwenikweni ngati sitifotokoza tanthauzo lake.
5 Popenda mbali imeneyi, phungu wanu adzakhala akudzifunsa kuti, Kodi munthu wosazindikira bwino choonadi cha m’Baibulo atha kumvetsa mfundo imeneyo kapena mawuwo? Sikuti iye adzakuletsani kugwiritsa ntchito mawu ateokalase oterowo ayi. Mawuwo ali mbali ya kalankhulidwe kathu ndipo timafuna kuti okondweretsedwa atsopano awadziŵe. Koma ngati mugwiritsa ntchito alionse a mawu amenewo, adzafuna aone ngati mudzawatanthauzira.
6-8. Pokonzekera nkhani zathu, n’chifukwa ninji tiyenera kusamala kuti tisankhe mfundo zoyenerera?
6 Kusankha mfundo zoyenerera. Mfundo zimene musankha zokalankhulana ndi anthu mu utumiki wakumunda ziyenera kukhala zosiyanasiyana, monganso mmene mawu amene mumagwiritsa ntchito amakhalira osiyanasiyana malinga ndi chochitikacho. Chifukwa chake n’chakuti zilipo zinthu zina zimene sitingasankhe kuti tikakambirane ndi watsopano. M’zochitika zoterozo nkhani yoti mukakambirane mudzasankha nokha osati wina aliyense. Koma pamene mupatsidwa gawo m’sukulu, nkhani yoti mukalankhule imakhala yosankhidwiratu. Chimene mudzangofunikira kusankha ndicho mfundo za m’nkhaniyo zimene mudzakambirana. Kodi kusankhako mudzakuchita motani?
7 Choyamba, popeza kuti simungagwiritse ntchito mfundo zina kupatulapo za m’nkhaniyo, muyenera kusankha chochitika kapena kuti njira imene mukambire nkhani yanu imene idzakulolani kusankha mfundo zambiri zoyenerera. Phungu wanu adzafuna kuona mfundo zimene mwasankha ndi mmene zikukhalira zoyenerana ndi mikhalidwe ya nkhani yanu. Chifukwa chake n’chakuti, pa luso limene likupendedwali, mukufuna kusonyeza kuti mikhalidwe yosiyanasiyana mu utumiki wakumunda imafuna mfundo zosiyanasiyananso. Mwachitsanzo, poitanira munthu watsopano ku msonkhano, simungagwiritse ntchito mfundo zimene mungakambirane ndi munthu mu ulaliki wa kukhomo ndi khomo. Choncho, kaya nkhani yanu ikufuna kukambirana ndi mwininyumba kapena ndi nkhani yapapulatifomu, lingalirani za omvetsera mwa zinthu zimene mudzanena ndi mfundo zimene musankha m’nkhani yanuyo.
8 Pofuna kudziŵa ngati mfundo zanu zili zoyenera kapena ayi, phungu wanu adzaganizira cholinga cha nkhani yanu. Pochezera anthu kunyumba ndi nyumba, cholinga chanu makamaka chimakhala kuphunzitsa ndi kulimbikitsa eninyumbawo kuti aphunzire zochuluka. Paulendo wobwereza cholinga chanu ndicho kukulitsa chidwi, ndipo ngati kuli kotheka, kuyambitsa phunziro la Baibulo. Ngati ali mawu apambuyo paphunziro, cholinga chake chiyenera kukhala kulimbikitsa mwininyumba kuti afike ku msonkhano kapena kuti aziloŵa mu utumiki wakumunda, ndi zina zotero.
9, 10. Nanga tingadziŵe motani ngati mfundo zimene tinasankha zili zoyenerera?
9 Ndithudi, ngakhale m’mbali imodzimodzi ya utumiki, mutha kusankha mfundo zosiyanasiyana malinga ndi omvetsera anu. Choncho ndi bwino kukumbukiranso chimenecho. Musaloŵetse m’nkhani yanu mfundo zina zimene muona kuti sizithandiza pacholinga chanu.
10 Chifukwa cha zimenezo, chochitika kapena njira yokambira nkhani yanu iyenera kusankhidwiratu nkhaniyo musanaikonzekere. Dzifunseni kuti: Kodi cholinga changa n’chiyani? Ndi mfundo ziti zimene ndiyenera kuzifotokoza kuti ndikwaniritse cholinga chimenecho, ndipo mfundo zimenezo ndingazisinthe motani kuti ziyenerane ndi mikhalidwe ya nkhaniyo? Pamene mwatsimikiza zinthu zimenezi, mutha kusankha mfundo zoyenerera mosavuta komanso kuzifotokoza m’njira yozigwirizanitsa ndi utumiki wakumunda.
11-13. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kusonyeza phindu lenileni la mfundo zimene tazifotokoza?
11 Kuunika phindu la mfundo zoperekedwa. Kuunika phindu la mfundo kumatanthauza kusonyeza mwininyumba momvekera bwino ndi mosalakwitsa kuti zikum’khudza iye, kuti ndi kanthu kena kamene iye akukafunikira kapena kamene angakagwiritse ntchito. Kuyambira pachiyambi penipeni pa nkhani, mwininyumba ayenera kuzindikira kuti “izi zikundikhudza ine.” Chimenecho n’chofunika kuti mukope chidwi cha omvetsera. Koma, kuti chidwicho chisatayike, m’pofunika kupitiriza kuloŵetsa munthuyo m’nkhaniyo mpaka kumapeto.
12 Zimenezo zimaphatikizapo zambiri kuposa chabe kuyendera limodzi ndi omvetsera ndi kuwathandiza kulingalira. Tsopano muyenera kupitirira pamenepo ndi kuloŵetsa mwininyumbayo m’cholinga cha nkhaniyo. Cholinga chathu mu utumiki wakumunda ndicho kuphunzitsa anthu choonadi cha Mawu a Mulungu ndi kuwathandiza kuphunzira njira ya chipulumutso. Choncho, mwaluso ndi mom’ganizira, muyenera kusonyeza mwininyumba wanu mapindu enieni amene angapeze ngati amvetsera ndi kuchitapo kanthu pazimene mukumuuza.
13 Ngakhale kuti mfundo imeneyi ya lusoli ikutchulidwa kumapeto, sikuti ndi yaing’ono ayi. Ndi mfundo yofunika kwambiri ndipo siiyenera kunyalanyazidwa. Limbikirani mfundo imeneyi chifukwa n’njofunika kwambiri mu utumiki wakumunda. Simungathe kukopa chidwi cha mwininyumba kwa nthaŵi yaitali popanda kum’chititsa kuona bwino lomwe kuti zimene mukunenazo n’zaphindu pamoyo wake.