Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 19 tsamba 96-99
  • Kugwiritsa Ntchito Sukulu Kuwongolera Utumiki Wakumunda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Sukulu Kuwongolera Utumiki Wakumunda
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Kupindula Kwambiri ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 19 tsamba 96-99

Phunziro 19

Kugwiritsa Ntchito Sukulu Kuwongolera Utumiki Wakumunda

1. Pokonzekera nkhani zathu za ophunzira, kodi tiyenera kukumbukira kuti cholinga cha sukuluyo n’chiyani?

1 Chimodzi cha zolinga zazikulu za Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndicho kutithandiza kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki wakumunda. Nthaŵi zonse kumbukirani chimenecho pokonzekera nkhani zanu. Chidwi chanu chisangokhala pakupeza chidziŵitso, komanso onani mmene mungagwiritsire ntchito chidziŵitsocho polalikira ndi pophunzitsa ena mu utumiki wakumunda.

2. Kodi nkhani za ophunzira zingayesedwe motani pofuna kupereka umboni?

2 Ena amagwiritsa ntchito bwino nkhani zawo mwa kuziyesa kwa mabwenzi, anansi, aphunzitsi a kusukulu, achibale osakhulupirira ndi ena omwe angamvetsere. Zimenezi zimatheketsa zinthu zingapo. Wophunzirayo atha kuona mmene nkhaniyo ikuwakhudzira ena ndipo angawongolere mwina ndi mwina kuti ikhale bwino. Ndiponso, wina angachite chidwi ndi Baibulo pamene amva mfundo zopindulitsa zikufotokozedwa. Ingakhale njira yomuitanira ku sukulu yateokalase. Anthu ambiri aitanidwa ku Nyumba ya Ufumu mwa njira imeneyi. Mboni ina ku Japan inayesera nkhani yake ya m’sukulu yateokalase kwa mayi wina wa tchalitchi amene anakam’chezera. Mutu wa nkhani yakeyo unali wakuti “Anthu a Mulungu akuuzidwa kuti atuluke ‘m’Babulo.’” Mayiyo anasonyeza chidwi ndipo anavomera kuphunzira naye Baibulo.

3. Kodi n’chiyani chidzatilimbikitsa kugwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda zimene timamva pasukulu?

3 Ganizirani za utumiki wakumunda. M’sukulu yateokalase mumamva mfundo zamtengo wapatali kwambiri, ndipo zambiri mutha kuzigwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda. Papologalamuyo timakambirana nkhani monga zifukwa zokhulupirira Baibulo, mayankho pamafunso a ziphunzitso, kukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo, malongosoledwe a malemba osiyanasiyana, ndi mmene mapulinsipulo a Baibulo angagwiritsidwire ntchito pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Yesetsani kupeza mipata imene mungagwiritsirepo ntchito mfundo zimenezi mu utumiki wakumunda. Musayembekeze mpaka wina akachite kufunsa. Ngati kuli koyenera, yambitsani nkhani inuyo. Mwakutero, mudzakhomezera kwambiri nkhaniyo m’maganizo mwanu ndipo mudzakhala wokhoza kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana mu utumiki.

4. Kodi sukuluyo ingatithandize motani paluso lathu logwiritsa ntchito Baibulo?

4 Kugwiritsa ntchito Baibulo mwachindunji ndi mbali yaikulu ya ntchito yathu. Koma ofalitsa ena kumawavuta kuti apeze msanga malemba ofunikira. Kodi inunso muli nalo vuto limenelo? Ngati muli nalo, sukuluyi ingakuthandizeni kuwongolera. Motani? Tsatirani mlankhuli aliyense pa sukulu yateokalase ndi Baibulo lanu. Pamene mlankhuliyo aŵerenga lemba, nthaŵi zonse litseguleni m’Baibulo lanu. Pamene mutsegula malemba nthaŵi ndi nthaŵi, mudzafika powadziŵa bwino ndipo mudzadziŵanso kumene mungawapeze. Chofunika ndicho kukhala ndi chizoloŵezi chotsegula malemba nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo mungamachite zimenezo osati chabe pamene muli mu utumiki wakumunda, komanso mlungu uliwonse pamene muli pasukulu imeneyi. Ndiponso mungapindule nako kufufuza kumene alankhuli onse amakuchita. Iwo amasankha malemba oyenerana bwino kwambiri ndi nkhani zawo. Pamene mutsatira alankhuliwo, bwanji osachonga mawu ofunika kwambiri pamalembawo amene muona kuti mungafune kuwagwiritsa ntchito mu utumiki wanu? Mungawalembenso, limodzi ndi mutu wa nkhaniyo, m’kati mwa chikutiro cha Baibulo lanu. M’njira imeneyi kudzakhala kosavuta kwa inu kugwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda zimene mumaphunzira pasukuluyo.

5, 6. Kodi kugwiritsa ntchito mikhalidwe yoonetsa zochitika zenizeni m’nkhani zathu kungatithandize motani?

5 Pokonza nkhani yanu, kusankha bwino chochitika kudzakuthandizaninso kupeza mapindu ochokera m’sukuluyo ogwiritsa ntchito mu utumiki wanu wakumunda. Pamene kuli kotheka, gwiritsani ntchito mikhalidwe imene imapezekadi mu utumiki. Nthaŵi zina mungapeze kuti nkhani yanu imayenera ulaliki wa kunyumba ndi nyumba kapena umboni wa mwamwayi. Nthaŵi zina ingakhale yopindulitsa kwambiri utakhala ulendo wobwereza. Kapena mwina kungakhale kukambirana mfundo imene ingabuke paphunziro la Baibulo lapanyumba. Nthaŵi zonse yesetsani kusonyeza zofanana ndi zenizeni. Pofuna kuchita zimenezo, nthaŵi zina chochitikacho chingakhale chosonyeza mwininyumba wotsutsa zimene mukunena. Kenako sonyezani mmene mungachitire ndi mkhalidwewo. Si nthaŵi zonse pamene nkhani zochita ndi utumiki wakumunda zimakhala ndi chipambano nthaŵi yomweyo; n’kopindulitsanso kusonyeza mmene tingachitire ndi anthu amphwayi.

6 Pamene mwapatsidwa mbali ya mwininyumba, inunso mungapindule podziŵa zochitika mu utumiki wakumunda. Gwiritsani ntchito mwayi umenewo kuti muzindikire mmene eninyumba amaganizira, ndi zifukwa zimene amatsutsira. Pamene musonyeza mkhalidwe weniweni wa mwininyumba, ndi kuonetsetsa mmene mwininkhaniyo akuchitira ndi mkhalidwewo, mudzaphunzira mmene mungakhalire wogwira mtima mu utumiki.

7. Pofuna kupita patsogolo nthaŵi zonse, ndi mbali iti imene tidzafuna kuwongolera mu utumiki wathu wakumunda mlungu uliwonse?

7 Pamene nkhaniyo itengedwa mu Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase, pendani malangizowo ndi cholinga choti muwongolere ulaliki wanu, kaya wa kunyumba ndi nyumba kapena kwina kulikonse. Bwanji osakhala ndi cholinga chimenecho mlungu umenewo, cha kuwongolera utumiki wanu? Mwachitsanzo, pamene nkhaniyo ikunena za kufunika kwa mutu wa nkhani, dzifunseni ngati ulaliki wanu mu utumiki wakumunda umakhala ndi mutu wa nkhani. Kodi mumaupangitsa kuonekera bwino kwambiri moti eninyumba amausunga m’maganizo mutakambirana nawo? Ngati simutero, limbikirani chimenecho mlungu umenewo. Komanso, mudzamva nkhani zimene amaŵerenga ndi kutanthauzira malemba. Pamene mumvetsera nkhani zimenezi, pendani mmene inuyo mumagwiritsira ntchito malemba. Kodi mumangowaŵerenga kwa mwininyumba osawafotokoza? Kodi mavesiwo mumawagwirizanitsa motani ndi mutu wa nkhani yanu? Kodi mumawatanthauzira motani kwa mwininyumba? Kupenda koteroko kungathandize kuŵerenga ndi kutanthauzira malemba. Kodi nkhani yanu ikunena za kugwiritsa ntchito mafanizo? Kodi mungawongolere motani kagwiritsidwe ka mafanizo? Mwinanso nkhaniyo ingakhale yonena za kuphunzitsa paphunziro la Baibulo lapanyumba. Yesani njira zanuzanu kuti muone mmene mungagwiritsire ntchito nkhaniyo pophunzitsa paphunziro lanu la Baibulo lapanyumba, ndipo chitani zimenezo mlungu womwewo. Mwa njira imeneyo, mudzakhala mukugwiritsa ntchito zimene mumaphunzira pa Sukulu ya Utumiki Wateokalase kuwongolera utumiki wanu wakumunda.

8. Pamene tili mu utumiki wakumunda, kodi ndi motani mmene tingadzipatsire uphungu wopindulitsa ife eni?

8 Pendani ulaliki wanu. Pasukulupo kaŵirikaŵiri mumamva uphungu ukuperekedwa ndi kuona mapindu ake. N’chosatheka kuti woyang’anira sukulu azikhala nanu kumakomo mu utumiki wakumunda, choncho bwanji osakhala ndi chizoloŵezi chomadzipatsa nokha uphungu? Mutamaliza kulankhula ndi mwininyumba ndipo mukupita kunyumba ina, dzifunseni kuti: Kodi ndikanachita motani kuti ndikhale wogwira mtima kwambiri? Popeza ndadziŵa tsopano mmene ndachitira, kodi ndidzatani ndikapitakonso tsiku lina kuti ndikachite bwino koposa? Kupenda koteroko kungakuthandizeni tsiku lomwelo, chifukwa mutha kukumana ndi mkhalidwe wofananawo panyumba ina. Ngati mukhala ndi chizoloŵezi chopenda maulaliki anu pamene muli muulaliki, kupita patsogolo kwanu kudzakhala kosalekeza. Komabe, pamene mugwira ntchito ndi wofalitsa wina, mungafunsirenso maganizo kwa mnzanuyo.

9, 10. Poyesa ulaliki wathu kunyumba, n’chiyani chimene tingachite chotithandiza kugwiritsa ntchito m’munda zimene timaphunzira pasukuluyo?

9 Njira yabwino kwambiri yokulitsira luso lanu la kulalikira ndiyo mwa kuyesera maulalikiwo ndi ena, ndiyeno kuwapendera limodzi. Mungachite zimenezo ndi apabanja panu kapena ndi ena mumpingo. Iwo angatenge mbali ya eninyumba, akumatsutsa muja ambiri amachitira. Pamene atsutsa, yesani kuyankha ngati mungathe. Ngati simudziŵa mmene mungayankhire, imani kaye ndi kufunsira maganizo kwa ena omwe alipo. Ndiyeno pitirizani mwa kugwiritsa ntchito ena a maganizo operekedwawo. Mutamaliza, pendani limodzi nawo ndi kuona ngati zimene mwachitazo zinali zogwira mtima. Kuyesera koteroko kunyumba kungawongolere ulaliki wanu, ndiponso kumakupatsani mwayi wa kuwongolera zolakwa musanaloŵe m’munda. Kungakuthandizeni kugwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda njira zimene mumaphunzira m’sukuluyo. Kumbukirani kuti, mtumwi Paulo ananena kuti anthu achikulire ali awo “amene mwa kugwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Aheb. 5:14, NW) Njira imodzi yonolera mphamvu za kuzindikira ndiyo mwa kuzigwiritsa ntchito nthaŵi zonse.

10 Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi imodzi mwa njira zambiri zimene Yehova amatiphunzitsira. Pamene tikuphunzira mwakhama ndi kugwiritsa ntchito zimene timaphunzira tidzakhoza kunena mawu a mneneri akuti: “Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m’maŵa ndi m’maŵa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.”—Yes. 50:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena