Kupindula Kwambiri ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki
1 Sukulu Yautumiki Wateokratiki yakhala yothandiza kwambiri pakutiphunzitsa “luso la kuphunzitsa” kotero kuti tiuze ena choonadi cha Baibulo mogwira mtima. (2 Tim. 4:2, NW) Mlungu uliwonse timalandira chidziŵitso chopindulitsa pa nkhani zosiyanasiyana za Baibulo. Kodi tingatsimikizire motani kuti tikupeza phindu lalikulu m’malangizo ofunika kwambiri operekedwa ndi sukulu imeneyi?
2 Mvetserani mosamalitsa ndemanga zotsegulira za woyang’anira sukulu pamene akutchula nsonga zina zokondweretsa zimene mungaphunzire pa msonkhanowo. Ganizirani pa mafunso alionse amene iye angadzutse ndi mmene mungagwiritsire ntchito mayankhowo mu utumiki wanu.
3 Nkhani yachilangizo sili chabe kupenda nkhani yosindikizidwa. Imagogomezera phindu logwira ntchito la chidziŵitsocho ndi mmene chingakupindulitsireni inu pa nokha. Kukonzekera pasadakhale kudzakuthandizani kusumika maganizo anu bwino lomwe pa nsonga zazikulu ndi kutengamo mbali m’kupendanso kwa pakamwa kotsatira.
4 Kusaphonya kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu kungakulitse chiyamikiro chanu kaamba ka Mawu a Mulungu. Kufufuza kowonjezereka kungavumbule mfundo zosiyanasiyana zatsopano ndi zokondweretsa zimene zidzakulitsa kumvetsetsa kwanu choonadi. Kuperekedwa kwa mfundo zazikulu za Baibulo sikuli chabe kungobwereza nkhani za m’Baibulo. Pambuyo pa kupenda nkhani yonse mwachidule, wokamba nkhaniyo amasonyeza nsonga zapadera zimene zili m’chigawo chogaŵiridwacho ndi kusonyeza mmene zimakhudzira moyo ndi kulambira kwathu. Mvetserani mwatcheru kuti muphunzire mmene mungaŵiritsire ntchito bwino malangizo a Baibulo.—Sal. 119:105.
5 Ngati mwagawiridwa nkhani ya wophunzira, samalirani nsonga ya uphungu imene mukugwirirapo ntchito panthaŵi ino. Ŵerengani malingaliro operekedwa mu Bukhu Lolangiza la Sukulu onena za mkhalidwe umenewo wa kulankhula, ndipo yesani kuwagwiritsira ntchito. Posankha mfundo za nkhani yanu, yesani kugogomezera nsonga zimene zidzakhala zogwira ntchito m’munda.—sg-CN mas. 96-9.
6 Ngati ndinu mlongo amene mwagaŵiridwa kukamba Nkhani Na. 3 kapena Nkhani Na. 4, yesani kukamba nkhaniyo mumkhalidwe wosonyeza zenizeni. Mwininyumba angavomereze kapena kutsutsa zonse zimene mukunena; yesetsani kusonyeza mmene mungathandizire munthuyo kulingalira pa malamulo a mkhalidwe a Baibulo okhudza nkhaniyo. (sg-CN mas. 153-8) Zimenezi zimathandiza omvetsera kuona mmene angachitire ndi zitsutso zofanana ndi zimenezo zimene amakumana nazo muutumiki wakumunda. Konzekerani pasadakhale kukali nthaŵi yaitali, ndipo linganizani kuyeseza kwa pasadakhale ndi mwininyumba wanu. Sikuli koyenera kuyesa msonkhanowo utayamba.
7 Ophunzira amene akukamba nkhani amalimbikitsidwa kukhala pafupi ndi kutsogolo kwa holo. Zimenezi zimasungitsa nthaŵi ndi kutheketsa woyang’anira sukulu kupereka ndemanga zake mwachindunji kwa wophunzirayo. Onse angapindule ndi malingaliro okoma mtima, achindunji amene iye amapereka ochokera mu Bukhu Lolangiza la Sukulu. Iye mwina sangatsatire nsonga za kulankhula malinga ndi mmene zandandalikidwira pa silipi la Uphungu wa Kulankhula; angasankhe nsonga ya uphungu yozikidwa pa zimene mufunikira panthaŵiyo kuti mupite patsogolo bwino.
8 Zonsezi ndi zifukwa zabwino kwa ife zokonzekerera ndi kupezeka pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki mlungu uliwonse. Malangizo amene timalandira amatithandiza kukhala anzeru ndi aluso muutumiki wathu.—Miy. 1:5.