Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 20 tsamba 100-108
  • Uphungu Umalimbikitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uphungu Umalimbikitsa
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Malangizo kwa Oyang’anira Sukulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 20 tsamba 100-108

Phunziro 20

Uphungu Umalimbikitsa

1, 2. N’chifukwa chiyani timafunikira uphungu, ndipo timaulandira m’njira yotani?

1 Alambiri a Mulungu woona, nthaŵi zonse ndipo mosakayika konse, amafuna chitsogozo kwa iye m’njira zawo zonse. Mmodzi wa olemba masalmo a Baibulo analemba mwachidaliro kuti: “Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu.” (Sal. 73:24) Ndipo m’pemphero lake lochokera pansi pa mtima Yeremiya anati: “Palibe chokulakani Inu; . . . dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu; wamkulu mu upo [“uphungu,” NW], wamphamvu m’ntchito.”—Yer. 32:17-19.

2 Uphungu wa Yehova umadza kwa alambiri ake achikristu lerolino kupyolera m’Mawu ake olembedwa komanso kupyolera m’gulu la atumiki ake enieni. Choncho awo amene alembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase amazindikira mwamsanga kuti uphungu umene amalandirawo, komanso mmene aphunguwo amauperekera, amatsatiradi chiphunzitso chabwino cha m’Baibulo.

3-5. Fotokozani mmene silipi la Uphungu wa Kulankhula ndi nkhani za m’Maphunziro 21 mpaka 37 zakonzedwera kuti zigwiritsidwe ntchito limodzi.

3 Uphungu wopita patsogolo. Pofuna kuthandiza ophunzira komanso woyang’anira sukulu, pali silipi la Uphungu wa Kulankhula limene laperekedwa. Pasilipi limenelo andandalikapo mfundo zokwanira 36 zoti zithandize ophunzira pokulitsa luso lofotokoza choonadi mogwira mtima. Mfundo iliyonse yalongosoledwa momvekera bwino m’Maphunziro 21 mpaka 37 a buku lino, ndipo phunziro lililonse alisonyeza ndi nambala pasilipi la Uphungu wa Kulankhula. Maphunziro ameneŵa ndi oti agwiritsidwe ntchito limodzi ndi silipi la uphungu. Mudzaona kuti kaŵirikaŵiri maluso aŵiri kapena atatu ogwirizana kwambiri akalankhulidwe aphatikizidwa m’Phunziro limodzi. Izi zakhala choncho chifukwa taona kuti ndi bwino kuwapenda nthaŵi imodzi.

4 Kudzakhala kowapindulitsa aja olembetsa chatsopano m’sukulu kumakonzekera bwino lomwe, akumaganiza mfundo zondandalikidwa pasilipi la Uphungu wa Kulankhula. Pankhani yawo yoyamba m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase, woyang’anira sukulu (kapena phungu wina ngati olembetsa ndi ochuluka) adzangoyamikira wophunzirayo pamfundo zimene wachitapo bwino. Kenako, phunguyo asumike maganizo pamfundo yofunikira kwambiri chisamaliro kuti wophunzirayo awongolere kalankhulidwe kake, ndipo agaŵire wophunzirayo mfundo yoti akagwirirepo ntchito pankhani yake yotsatira. Ngati wophunzira aliyense afika poti wakhoza bwino pamfundo inayake, phungu ayenera kum’dziŵitsa kuti tsopano apite pamfundo ina pasilipi la uphungu.

5 Ena ophunzira kulankhula nkhani angapite patsogolo mofulumirirapo kwambiri, pamene ena angafunikire kulimbikira pamfundo imodzi yokha panthaŵi imodzi m’malo moyesa kukwaniritsa mfundo zonse zofotokozedwa m’Phunziro lonse. Ndipo ophunzira ena angalangizidwe kulankhula nkhani zingapo pamene akugwirira ntchito pamfundo imodzi yovuta, kotero kuti alidziŵe bwino kwambiri luso lakulankhula limenelo asanapite ku lina.

6, 7. Ndi mfundo zotani zimene woyang’anira sukulu ayenera kuperekapo uphungu?

6 Uphungu wopatsidwa kwa wophunzira aliyense atatha nkhani yake uyenera kuperekedwa mokoma mtima, ndi cholinga chothandiza wophunzirayo kuti apite patsogolo powongolera luso lake lakulankhula. Komabe, uphungu uliwonse wopatsidwa kwa wopereka nkhani yolangiza kapena mfundo zazikulu za m’Baibulo, uyenera kuperekedwa m’seri sukulu itatha. Mlankhuli ameneyu ayenera kupatsidwa uphungu makamaka ngati wadya nthaŵi yosonyezedwayo. Wolankhula nkhani yolangiza ayenera kuyesetsa kupereka nkhani yachitsanzo m’mbali zonse, ndipo akatero uphungu wam’seri ungakhale wosafunikira.

7 Nthaŵi zonse uphungu uyenera kuperekedwa pamfundo zimene wophunzirayo analangizidwa kuti agwirirepo ntchito. Komabe, ngati pali mbali ina pankhaniyo imene iye wachita bwino kwambiri, phunguyo angaiphatikize pakuyamikira kwake, koma mfundo imeneyo asaichonge pasilipi la uphungu. Zizindikiro zogwiritsa ntchito ndi izi: “L” (Limbikirani chimenechi) ngati wophunzirayo afunikirabe kuyesetsa kuwongolera luso limenelo la kulankhula; “W” (Wawongolera) ngati wophunzira anayesapo kale kukonza luso limenelo ndipo akuonetsa kuti wawongolera koma ulendo wina angachite bwino koposa; “B” (Bwino) ngati luso limene akugwirirapo ntchito walisonyeza bwino moti afunikira kupita pamfundo ina pokonzekera nkhani yotsatira m’sukuluyo. Ngati wophunzira ali ndi nkhani yoŵerenga, phungu adzapereka uphungu woyenerana ndi nkhani yamtundu umenewo.

8-10. Pochonga silipi la uphungu, kodi woyang’anira sukulu ayenera kukumbukira chiyani pofuna kulimbikitsa ena kupita patsogolo?

8 M’pofunika kuti woyang’anira sukulu azikhala wosamala kwambiri kuti apindulitse onse ndi uphungu wake. Ngati wolankhula nkhani ali watsopano kwambiri, chofunika kwambiri ndicho kungom’limbikitsa. Komanso alipo ophunzira ena amene akhala kanthaŵi ndithu m’sukulu, oti ali ndi khama lokonzekera nkhani zawo, nayesa kusamalira maluso a kulankhula amene amagaŵiridwa kugwirirapo ntchito, koma luso lawo n’kukhalabe lochepa. M’zochitika zoterozo, ngati iwo aonetsa luso lina ngakhale pamlingo wochepa chabe, woyang’anira sukulu angalembe “B” pasilipi la uphungu ndi kulola wophunzirayo kupita pamfundo ina.

9 Komanso, mlankhuli wina angakhale ndi chidziŵitso chochulukirapo kapena luso lachibadwa lokulirapo, koma, mwina chifukwa chotanganidwa ndi ntchito zina, sanapatule nthaŵi yoti aŵerenge za maluso akulankhula amene anagaŵiridwa kwa iye, ndiye n’kulephera kulankhula bwino nkhani yake. Zikakhala choncho, kungakhale kulepheretsa wophunzirayo kupita patsogolo ngati woyang’anira sukulu alemba “B” pasilipi la uphungu namuuza kupita pamfundo ina. Ngati nkhaniyo inali yamtundu woti mfundo yogaŵiridwayo ikanasonyezedwa, phunguyo alembe “L” (Limbikirani chimenechi) ndi kupereka chithandizo mokoma mtima kwa wophunzirayo kuti apite patsogolo. Mwa njira imeneyi ophunzira adzalimbikitsidwa kuona nkhani iliyonse kukhala chizindikiro chosonyeza kupita kwawo patsogolo, osati chabe kukwaniritsa gawo lawo.

10 Kumbukirani kuti kuphunzira kalankhulidwe ka nkhani kumeneku n’kwapang’onopang’ono. Musayembekeze kukhala mlankhuli wokhoza bwino nthaŵi yomweyo. Zimachitika pang’onopang’ono, koma wina akhoza kuchita mofulumirirapo ngati aikirapo khama kwambiri. Ngati mudzasinkhasinkha panjira zosiyanasiyana zoperekedwa m’pologalamu imeneyi yophunzitsa kalankhulidwe ndi kuchita khama kumakonzekera nkhani zanu, kupita patsogolo kwanu kudzaonekera kwa onse.—1 Tim. 4:15.

11-16. Ndi malangizo otani amene phungu amatsatira pofuna kulimbikitsa ena ndi uphungu wake?

11 Phungu. Woyang’anira sukulu ayenera kupenda mosamala nkhani za mlungu uliwonse kotero kuti adziŵe ngati nkhaniyo yalankhulidwa bwino ndi kuti akhoze kuwongolera zolakwa zilizonse. Komabe, sayenera kufika pamlingo woti sakondweranso ndi nkhanizo chifukwa chokhala wosuliza kwambiri za mmene nkhani zikulankhulidwira. Iyenso ayenera kupindula ndi choonadi chabwino chomwe chikulongosoledwa.

12 Popereka uphungu nthaŵi zonse ayenera kuyamba ndi mawu oyamikira khama la wophunzira. Ndiyeno apitirize kukambapo pamfundo za pasilipi la uphungu zimene mlankhuliyo akugwirirapo ntchito. Ngati mfundo ina ikufunikirabe kuwongolera, si bwino kugogomeza mmene mlankhuliyo walepherera, koma mmene angawongolere mfundoyo. Akatero uphunguwo udzalimbikitsa mlankhuliyo komanso ena omvetsera.

13 Sikokwanira kungouza mlankhuli kuti wachita bwino kapena kuti afunikira kulimbikirabe paluso lakutilakuti la kulankhula. Kudzakhala kothandiza wina aliyense amene alipo ngati phunguyo afotokoza chifukwa chake nkhaniyo inali bwino kapena chifukwa chake pakufunikira kuwongolera komanso mmene kuwongolerako angakuchitire. Ndiponso, kudzakhala kopindulitsa ngati iye asonyeza mmene luso la kulankhula limene akufotokozalo liliri lofunika kaamba ka utumiki wakumunda kapena pamisonkhano yampingo. Mwa kutero, adzathandiza mpingo wonse kuzindikira mfundo imeneyo ndipo adzalimbikitsanso wophunzirayo kupitirizabe kuisamalira.

14 Si udindo wake phunguyo kubwereramo m’nkhani ya wophunzira. Iye ayenera kuchita mwachidule ndipo molunjika pamfundo ya uphungu wake, akumasamala kuthera mphindi ziŵiri zokha pankhani iliyonse ya wophunzira. Mwa kutero, uphunguwo ndi maganizo operekedwawo sadzaphimbika ndi mawu ambirimbiri. Ndiponso, m’pofunika kutchulira wophunzirayo masamba pamene angapeze chidziŵitso chochulukirapo pamfundo imene mwafotokoza.

15 Zolakwa zazing’ono monga katchulidwe ka mawu kapena galamala si zinthu zazikulu zoti n’kuziyang’anira. M’malo mwake, phungu ayenera kusamala za mmene kalankhulidwe ka wolankhulayo kakukhudzira anthu. Kodi nkhaniyo n’njopindulitsa ndi yopatsa chidziŵitso? Kodi n’njolinganizika bwino komanso yosavuta kutsatira? Kodi ikulankhulidwa moona mtima, mosamala, ndi mokhutiritsa? Kodi nkhope yake ndi manja ake polankhula zikusonyeza kuti akukhulupirira zimene akunenazo ndi kuti akufunitsitsa kuti omvetserawo amve choonadi chabwino m’malo mokopeka ndi kalankhulidwe kake? Ngati mbali zofunika zimenezi zasamalidwa bwino, omvetsera sadzaona n’komwe zolakwa za apa ndi apo m’katchulidwe ka mawu kapena m’galamala.

16 Uphungu woperekedwa m’sukulu yateokalase nthaŵi zonse uyenera kuperekedwa m’njira yokoma mtima ndi yothandiza. Cholinga chachikulu chiyenera kukhala chothandiza wophunzirayo. Ganizirani za umunthu wa amene mukufuna kum’patsa uphunguyo. Kodi n’ngwa mtima wapachala? Kodi sanaphunzire kwenikweni kusukulu? Kodi pali zifukwa zololera zolakwa zake? Uphungu uyenera kupangitsa woulandirayo kuona kuti akuthandizidwa, osati kusulizidwa. Tsimikizani kuti akuumvetsa uphunguwo ndipo akuuona kukhala woyenera.

17-19. Kuti apange kuwongolera kwakukulu pankhani iliyonse, kodi wophunzira ayenera kuchitanji asanakonze nkhani iliyonse ndi pambuyo poilankhula?

17 Kupindula ndi uphungu. Mukapatsidwa nkhani m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase kumbukirani kuti cholinga chanu chokalankhulira nkhaniyo sindicho kungolongosolera mpingo mfundo zolangiza, komanso kuwongolera luso lanu la kalankhulidwe. Kuti mukhale wokhoza m’mbali imeneyi, m’pofunika kupatula nthaŵi yopenda maluso a kulankhula amene mwapatsidwa kuti mugwirirepo ntchito. Ŵerengani mosamalitsa Phunziro lonselo m’buku lino pamene akulongosola mfundo imeneyo, kuti mudziŵe mmene iyenera kukhudzira kukonzekera kwanu ndi mmene mungasonyezere luso la kulankhulalo polankhula nkhani yanu. Pofuna kukuthandizani, mbali zazikuluzo za luso lililonse la kulankhula zalembedwa m’zilembo zazikulu zakuda m’buku lino. Zimenezi ndizo mbali zazikulu zoti muzisamalire.

18 Mutalankhula nkhani yanu, mvetserani mosamala uphungu wa pakamwa umene ukuperekedwa. Ulandireni moyamikira. Ndiyeno gwirirani ntchito pambali zofunikira kuwongolera. Ngati mukufuna kufulumiza kupita kwanu patsogolo, musayembekeze kufikira mutapatsidwa nkhani ina. Ŵerengani m’buku lino mbali zimene zikufotokoza mfundo zimene mukufunikira kugwirirapo ntchito. Yesetsani kugwiritsa ntchito maganizo operekedwawo m’kulankhula kwanu kwa tsiku ndi tsiku. Ndipo pofika nthaŵi yoti mulankhule nkhani yanu yotsatira ya wophunzira mungakhale mutazidziŵa bwino.

19 Wophunzira aliyense cholinga chake chiyenera kukhala kuwongokera pankhani iliyonse imene apereka m’sukulu. N’zoona kuti zimenezo zidzafuna khama losalekeza, koma mosapeneka konse, zotsatirapo zake ndi dalitso la Yehova. Kwa aja amene angapeze phindu lalikulu m’maphunziro a Sukulu ya Utumiki Wateokalase, mawu a pa Miyambo 19:20 amakhala ndi tanthauzo lalikulu kwa iwo: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimariziro chako.”

[Tchati pamasamba 104, 105]

UPHUNGU WA KULANKHULA

Mlankhuli ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

(Dzina Lonse)

Zizindikiro: L - Limbikirani chimenechi

W - Wawongolera

B - Bwino

Deti Na. ya

Nkhani

Mfundo zopatsa chidziŵitso (21)*

Kumveka bwino (21)

Mawu oyamba odzutsa chidwi (22)

Mawu oyamba oyenerana ndi mutu wa nkhani (22)

Mawu oyamba autali woyenera (22)

Mphamvu ya mawu (23)

Kupuma (23)

Kulimbikitsa omvetsera kuŵerenga Baibulo (24)

Kutulutsa malemba koyenera (24)

Kuŵerenga malemba ndi chigogomezo (25)

Kumveketsa bwino tanthauzo la malemba (25)

Kubwereza kogogomeza (26)

Manja (26)

Kugogomeza mutu wa nkhani (27)

Kupangitsa mfundo zazikulu kuonekera (27)

Kuyendera limodzi ndi omvetsera, ntchito ya notsi (28)

Ntchito ya autilaini (28)

Mawu:․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

* Nambala iliyonse m’mabulaketi ikusonyeza Phunziro la mu Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase mmene luso la kulankhulalo lafotokozedwa.

S-48-CN 3/85 J.G.

Deti Na. ya

Nkhani

Kusadodoma (29)

Mkhalidwe wokambirana (29)

Katchulidwe ka mawu (29)

Kugwirizanitsa nkhani ndi mawu olumikizira (30)

Kulankhula kotsatirika ndi kogwirizanika (30)

Kufotokoza kokhutiritsa (31)

Kuthandiza omvetsera kulingalira (31)

Kugogomeza ganizo (32)

Kusinthasintha mawu (32)

Kutengeka mtima (33)

Mzimu waubwenzi ndi wachifundo (33)

Mafanizo oyenerana ndi nkhani (34)

Mafanizo oyenerana ndi omvetsera (34)

Kugwirizanitsa nkhani ndi utumiki wakumunda (35)

Mawu omalizira oyenera, ogwira mtima (36)

Mawu omalizira autali woyenera (36)

Kusunga nthaŵi (36)

Chidaliro ndi kukhazikika maganizo (37)

Maonekedwe a munthu (37)

DZIŴANI IZI: Pankhani iliyonse phungu adzapereka uphungu wachindunji, mosatsatira kwenikweni dongosolo la mfundozo. Koma adzasamala makamaka mbali zimene wophunzirayo afunikira kuwongolera. Malowo osalembedwapo kanthu pafomupo mungawagwiritse ntchito kupatsira uphungu ophunzira pamfundo zimene sizinandandalikidwe, monga kunena zinthu zolondola, kutchula bwino mawu, kaimidwe, kusankha bwino mawu, galamala, zizoloŵezi, kulankhula zoyenerera, luso lophunzitsa, ndi kumveka bwino kwa liwu ngati kukhala kofunikira. Phungu ayenera kulemba mozungulira m’kabokosi ka mfundo yotsatira pamene wophunzira wamaliza kugwirira ntchito pa mfundo ina. Nambala ya mfundo imeneyo iyenera kusonyezedwa pa silipi lotsatira la Nkhani ya m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase (S-89).

Tchati pamasamba 106, 107

KUFOTOKOZA MWACHIDULE MALUSO A KULANKHULA

Mfundo zopatsa chidziŵitso (21)

Mfundo zolunjika

Zopatsa chidziŵitso omvetsera

Mfundo zothandiza

Kunena mawu olondola

Mfundo zowonjezera zothandiza kumveketsa bwino nkhani

Kumveka bwino (21)

Kufotokoza kosavuta kumva

Kufotokoza mawu osazoloŵereka

Kusachulukitsa mfundo

Mawu oyamba odzutsa chidwi (22)

Mawu oyamba oyenerana ndi mutu wa nkhani (22)

Mawu oyamba autali woyenera (22)

Mphamvu ya mawu (23)

Mphamvu ya mawu pamlingo woyenera

Mphamvu ya mawu yoyenerana ndi mikhalidwe

Mphamvu ya mawu yoyenerana ndi nkhani

Kupuma (23)

Kupuma pachizindikiro chopumira

Kupuma posintha ganizo

Kupuma kogogomeza

Kupuma pamene mkhalidwe wafuna kuti mutero

Kulimbikitsa omvetsera kuŵerenga Baibulo (24)

Mwa Kungotchula lemba

Mwa kulola nthaŵi kuti apeze lemba

Kutulutsa malemba koyenera (24)

Kudzutsa chidwi pa malemba

Kutchula chifukwa choŵerengera lemba

Kuŵerenga malemba ndi chigogomezo (25)

Kugogomeza mawu oyenera

Kugogomeza mwa njira yogwira mtima

Malemba oŵerengedwa ndi mwininyumba

Kumveketsa bwino tanthauzo la malemba (25)

Kulekanitsa mawu ofunika kuwatanthauzira

Mfundo ya mawu oyamba poŵerenga lemba imveketsedwa

Kubwereza kogogomeza (26)

Kubwereza mfundo zazikulu

Kubwereza mfundo zimene sizinamveke

Manja (26)

Manja ofotokoza

Manja ogogomeza

Kugogomeza mutu wa nkhani (27)

Mutu wa nkhani woyenerera

Kubwereza mawu kapena ganizo la mutu wankhani

Kupangitsa mfundo zazikulu kuonekera (27)

Kusachulukitsa mfundo zazikulu

Kufotokoza mfundo zazikulu payokhapayokha

Mfundo zazing’ono ziloza ku mfundo zazikulu

Kuyendera limodzi ndi omvetsera, ntchito ya notsi (28)

Kuyendera limodzi ndi omvetsera mwa kuwayang’ana

Kuyendera limodzi ndi omvetsera mwa mawu owaphatikizamo

Ntchito ya autilaini (28)

Kusadodoma (29)

Mkhalidwe wokambirana (29)

Kugwiritsa ntchito mawu okambirana

Kulankhula nkhani m’njira yokambirana

Katchulidwe ka mawu (29)

Kugwirizanitsa nkhani ndi mawu olumikizira (30)

Ntchito ya mawu olumikizira

Kugwirizanika koyenerana ndi omvetsera anu

Kulankhula kotsatirika ndi kogwirizanika (30)

Mfundo zosanjidwa m’dongosolo labwino

Kugwiritsa ntchito mfundo zoyenerera zokhazokha

Kusasiya mfundo zazikulu

Kufotokoza kokhutiritsa (31)

Kukhazikitsa maziko

Kupereka umboni womveka

Kulongosola kwachidule kogwira mtima

Kuthandiza omvetsera kulingalira (31)

Kusataya mfundo yogwirizanapo

Kufotokoza mfundo momveka bwino

Kuonetsa omvetsera mmene nkhaniyo ikuwakhudzira

Kugogomeza ganizo (32)

Kugogomeza mawu opereka ganizo m’sentensi

Kugogomeza mfundo zazikulu m’nkhani

Kusinthasintha mawu (32)

Kusinthasintha mphamvu ya mawu

Kusinthasintha liŵiro polankhula

Kusinthasintha ukulu wa mawu

Kusinthasintha mawu koyenerana ndi ganizo kapena mzimu wake

Kutengeka mtima (33)

Kuonetsa kutengeka mtima mwa kalankhulidwe kaumoyo

Kutengeka mtima koyenerana ndi nkhani

Mzimu waubwenzi ndi wachifundo (33)

Mzimu waubwenzi uonekera pankhope

Mzimu waubwenzi ndi wachifundo zionekera m’kamvekedwe ka mawu

Mzimu waubwenzi ndi wachifundo woyenerana ndi nkhani

Mafanizo oyenerana ndi nkhani (34)

Osavuta

Kumveketsa bwino tanthauzo lake

Kugogomeza mfundo zofunika kwambiri

Mafanizo oyenerana ndi omvetsera (34)

Onena za zinthu zodziŵika bwino

Abwino

Kugwirizanitsa nkhani ndi utumiki wakumunda (35)

Kumveketsa mawu kwa anthu

Kusankha mfundo zoyenerera

Kuunika phindu la mfundo zoperekedwa

Mawu omalizira oyenera, ogwira mtima (36)

Mawu omalizira ogwirizana mwachindunji ndi mutu wa nkhani

Mawu omalizira osonyeza omvetsera chochita

Mawu omalizira autali woyenera (36)

Kusunga nthaŵi (36)

Chidaliro ndi kukhazikika maganizo (37)

Kukhazikika maganizo kuonekera m’kaimidwe ka munthu

Kukhazikika maganizo kuonekera mwa kulamulira mawu

Maonekedwe a munthu (37)

Kuvalidwe ndi kapesedwe kabwino

Kaimidwe koyenera

Zipangizo zosamalika bwino

Musasonyeze nkhope yosemphana ndi nkhani

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena