Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 25
  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Wotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Wotani?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Chifuno Chenicheni cha Moyo
    Galamukani!—1992
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Mulungu Ndi Ndani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 25
Phunziro 25. Mmene dziko limaonekera mumlengalenga.

PHUNZIRO 25

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Wotani?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Baibulo limanena kuti munthu “amakhala ndi moyo waufupi komanso wodzaza ndi mavuto.” (Yobu 14:1) Kodi Mulungu amafuna kuti tizikhala ndi moyo woterewu? Ngati si choncho, ndiye kodi amafuna kuti tikhale ndi moyo wotani? Kodi zidzatheka kukhala ndi moyo umene Mulungu amafunawo? Baibulo lili ndi mayankho olimbikitsa a mafunso amenewa. Tiyeni tiwaone.

1. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wotani?

Yehova amafuna kuti tizikhala moyo wabwino kwambiri. Iye atalenga Adamu ndi Hava omwe ndi anthu oyambirira, anawaika m’Paradaiso wokongola, wotchedwa munda wa Edeni. Kenako “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.’” (Genesis 1:28) Yehova ankafuna kuti iwo abereke ana, asamalire dziko lonse lapansi kuti likhale paradaiso ndiponso kuti azisamalira zinyama. Cholinga chake chinali chakuti anthu onse akhale ndi thanzi labwino n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale.

Ngakhale kuti masiku ano anthu sitikukhala ndi moyo umene Mulungu ankafunawu,a cholinga chake sichinasinthe. (Yesaya 46:10, 11) Mulungu amafunabe kuti anthu amene amamumvera adzakhale ndi moyo wopanda mavuto mpaka kalekale.​—Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.

2. Tingatani kuti tizisangalala ndi moyo panopa?

Yehova anatilenga m’njira yakuti tizitha kuzindikira ‘zosowa zathu za uzimu,’ kutanthauza kuti timakhala ndi mtima wofuna kumudziwa ndi kumulambira. (Werengani Mateyu 5:3-6.) Iye amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba, ‘tiziyenda m’njira zake zonse, kumukonda’ komanso kumutumikira ‘ndi mtima wathu wonse.’ (Deuteronomo 10:12; Salimo 25:14) Zimenezi zingatithandize kuti tizisangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikamatumikira Yehova timakhala ndi moyo wosangalala chifukwa chakuti timachita zinthu mogwirizana ndi zimene iye amafuna.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza pamene ankalenga dzikoli kuti anthufe tikhalemo komanso zimene Mawu ake amanena zokhudza cholinga cha moyo.

Adamu ndi Hava akuyang’ana munda wawo wokongola womwe uli ndi zomera komanso zinyama zambirimbiri.

3. Yehova amafuna kuti anthu azikhala moyo wabwino kwambiri

Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

VIDIYO: N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?​—Kachigawo Kake (1:41)

  • N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi lomwe ndi lokongola?

Werengani Mlaliki 3:11, kenako mukambirane funso ili:

  • Malinga ndi lembali, mwaphunzira zotani zokhudza Yehova?

4. Cholinga cha Yehova sichinasinthe

Werengani Salimo 37:11, 29 ndi Yesaya 55:11, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga cha Yehova chokhudza anthufe sichinasinthe?

A. Nyumba yowonongeka. Denga lake ndi losasuka, mawindo ndi ophwanyika komanso pabwalo pake ndi ponyansa chifukwa pali zinyalala zambirimbiri. B. Nyumba yomwe yakonzedwanso ndipo ikuoneka bwino kwambiri komanso panja pake pakonzedwa bwino.

Nyumba yomwe yawonongeka ikhoza kukonzedwanso. N’chimodzimodzi ndi dzikoli. Anthu aliwononga kwambiri koma Mulungu adzalikonza kuti anthu amene iye amawakonda azidzakhalamo

5. Tikamalambira Yehova timakhala ndi moyo wosangalala

Kudziwa cholinga cha moyo, kumatithandiza kuti tizikhala mosangalala. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

VIDIYO: Ndinazindikira Kuti Moyo Uli ndi Cholinga (5:03)

  • Kodi kudziwa kuti moyo uli ndi cholinga kunathandiza bwanji Terumi?

Werengani Mlaliki 12:13, kenako mukambirane funso ili:

  • Tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova pa zinthu zonse zimene watichitira?

MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?”

  • Mungamuyankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wopanda mavuto mpaka kalekale padzikoli. Tikamamulambira ndi mtima wonse timakhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale panopa.

Kubwereza

  • Kodi Yehova ankafuna kuti Adamu ndi Hava azikhala moyo wotani?

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu sichinasinthe?

  • Kodi mungatani kuti muzikhala moyo wosangalala?

Zoti Muchite

ONANI ZINANSO

Onani umboni wosonyeza kuti munda wa Edeni unalipodi.

“Kodi Kunalidi Munda wa Edeni?” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2011)

Onani chifukwa chake sitikayikira kuti dzikoli lidzakhalapo mpaka kalekale.

“Kodi Dzikoli Lidzatha?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani mmene Baibulo lingakuthandizireni kudziwa cholinga cha moyo.

“Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Munthu yemwe ankaganiza kuti ali ndi chilichonse pa moyo anazindikira kuti pali chinachake chimene ankachisowa. Onani chimene chinamuthandiza kudziwa cholinga cha moyo.

Panopa Ndinadziwa Cholinga cha Moyo (3:55)

a M’phunziro lotsatira, tidzaphunzira chifukwa chake masiku ano anthufe timakumana ndi mavuto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena