Ziwerengero Zonse za 2021
Nthambi za Mboni za Yehova: 87
Mayiko Amene Anatumiza Lipoti: 239
Mipingo Yonse: 119,297
Opezeka pa Chikumbutso Padziko Lonse: 21,367,603
Amene Anadya Zizindikiro Padziko Lonse: 20,746
Ofalitsa Onse Amene Anagwira Ntchito Yolalikiraa: 8,686,980
Avereji ya Ofalitsa Amene Ankalalikira Mwezi Uliwonse: 8,480,147
Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Kuchokera mu 2020: 0.7
Obatizidwa Onseb: 171,393
Avereji ya Apainiyac Okhazikika Mwezi Uliwonse: 1,350,138
Avereji ya Apainiya Othandiza Mwezi Uliwonse: 398,504
Maola Onse Amene Tinalalikira: 1,423,039,931
Avereji ya Maphunziro a Baibulod Mwezi Uliwonse: 5,908,167
M’chaka chautumiki cha 2021,e a Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 229 miliyoni posamalira apainiya apadera, amishonale ndi oyang’anira dera pa utumiki wawo. Padziko lonse pali abale ndi alongo okwana 20,595 amene akutumikira m’maofesi a nthambi. Onsewa ali m’Gulu Lapadziko Lonse la Atumiki Apadera a Nthawi Zonse a Mboni za Yehova.
a Wofalitsa ndi munthu amene amalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuti mudziwe mmene timapezera chiwerengerochi, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?”
b Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?”
c Mpainiya ndi wa Mboni wobatizidwa komanso wachitsanzo chabwino amene amadzipereka kuti azilalikira uthenga wabwino kwa maola enaake mwezi uliwonse.
d Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Phunziro la Baibulo Lomwe a Mboni za Yehova Amachititsa Limakhala Lotani?”
e Chaka chautumiki cha 2021 chinayamba pa 1 September 2020, ndipo chinatha pa 31 August 2021.