13 YOSWA
Anatsatira Malangizo Achilendo
YOSWA anaimirira n’kuyang’ana ku Yeriko, mzinda womwe Mulungu anamulamula kuti auwononge. Iye anakumbukira mawu amene Yehova anamuuza, Mose atatsala pang’ono kumwalira akuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.” (Deut. 31:23) Pa nthawi imene amafuna kuwononga mzinda wa Yerikoyi, panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yehova anamuuzanso mawu ofanana ndi amenewa akuti: “Ukhale wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu.” (Yos. 1:7) Yoswa, anafunikadi kukhala wolimba mtima. Koma n’chifukwa chiyani?
Ngakhale kuti mzinda wa Yeriko sunali waukulu kwambiri, koma unkatetezedwa ndi mpanda wolimba kwambiri. Ndipo unali mzinda woyambirira kuti Aisiraeli auwononge kuti atenge Dziko Lolonjezedwa. Anthu amumzindawu ankachita zinthu zoipa kwambiri. Zaka zambiri m’mbuyomo, Yehova anauza Abulahamu kuti ‘Aamori adzalangidwa,’ apa ankanena za anthu onse okhala m’chigawo chimenechi cha dziko la Kanani. Iye anati nthawi inali ‘isanakwane’ kuti awapatse chilangocho chifukwa cha khalidwe lawo loipa. (Gen. 15:16) Tsopano nthawi ija inafika. Anthuwa ankapembedza mafano, kuchita zauhule pakachisi, kugonana amuna okhaokha, kugona ana, kugona ndi nyama komanso kupereka ana nsembe ku milungu yonyansa. Akanani anafika poipa kwambiri moti zinali ngati kuti dzikolo likufuna kuwalavula. (Lev. 18:3, 6, 21-27) Kodi zimenezi zinachitika bwanji?
Yehova anauza Yoswa kuti akawononge mzinda wozunguliridwa ndi mpanda m’njira yooneka ngati yosathandiza
Yehova anasankha kuti mzinda wa Yeriko ukhale woyamba kuchotsamo anthu oipa. Choncho iye anagwiritsa ntchito Yoswa ndi gulu lake la asilikali kuwononga mzindawo. Asilikaliwa anali okonzeka kutsatira malangizo a Yehova. Komabe, malangizo amene Yehova anapatsa Yoswa anali achilendo kwambiri. Yehova sanawauze kuti awononge mzindawo mwadzidzidzi kapenanso kukonzekera zomanga misasa mouzungulira. Koma anangowauza kuti aziyenda n’kumazungulira mzindawo kwa masiku 6, kamodzi pa tsiku. Yehova analamulanso kuti ansembe aziyenda nawo pozungulira mzindawo atanyamula likasa la pangano kwinaku akuliza malipenga. Pa tsiku la 7, anauzidwa kuti adzazungulire mzindawo maulendo 7 kenako n’kufuula.
Yoswa anali atamenyapo nkhondo zina m’mbuyomo. Asilikali ambiri akhoza kuona kuti njirayi inali yosathandiza. Chikanachitika n’chiyani ngati Aisiraeli akanagonjetsedwa? N’zosakayikitsa kuti anthu okhala m’mizinda ina ku Kananiko akanadziona kuti ndi amphamvu kuposa Aisiraeli ndipo akanabwera kudzamenyana nawo.
Komabe, Yehova anali atathandiza Yoswa kuti azimudalira kwambiri. Yoswa atatumiza anthu awiri ku Yeriko kuti akazonde mzindawo, anazindikira kuti amuna a kumeneko ankachita mantha ndi Aisiraeli. Kenako, modabwitsa Yehova anagawanitsa madzi a mtsinje wa Yorodano mpaka Aisiraeli anawoloka bwinobwino.
Yoswa ankati akaganizira zimenezi, chikhulupiro chake pa Mulungu chinkalimba kwambiri ndipo anali ndi zifukwa zomveka zokhalira womvera. Choncho anatsogolera asilikali ake kuti ayende kuzungulira Yeriko. Ansembe analiza malipenga ndipo palibe aliyense amene anatuluka mumzindawo chifukwa anthu onse anali ndi mantha. Mawa lake, anapitanso kukazungulira mzindawo monga mmene Yehova anawauzira. Anachita zimenezi kwa masiku 6. Kenako tsiku la 7 linafika.
Pa tsikuli, Aisiraeli anazungulira Yeriko maulendo 7. Pambuyo pake, anachita zosiyana ndi maulendo ena onse. Yoswa anauza anthuwo kuti: “Fuulani! Chifukwa Yehova wakupatsani mzindawu!” Kenako, sipanadutse nthawi yaitali chifukwa Baibulo limasonyeza kuti zitangotero, “asilikaliwo anafuula mwamphamvu mfuu yankhondo ndipo mpanda wa mzindawo unagwa mpaka pansi.”
Yoswa ndi asilikali ake analowa mumzindawo n’kuyamba kuwononga chamoyo chilichonse mogwirizana ndi zomwe Yehova anawalamula. Yoswa ndi asilikali ake, anapitiriza kuwononga mizinda ndi mitundu yambiri ya anthu. Pomaliza, Yehova anaseseratu anthu onse ochita zoipa kapena kuti Aamori.
Komabe, kambali kena kakang’ono ka mpanda wa Yeriko sikanagwe. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mumzindawo munali mzimayi wina wolimba mtima kwambiri amene anakhulupirira Mulungu ndipo tidzakambirana nkhani yake m’mutu wotsatira.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yoswa anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi ndi mbali iti ya Baibulo yomwe inkapezeka m’nthawi ya Yoswa? (w09 12/1 17 ¶4, mawu a m’munsi) A
Chithunzi A
2. Kodi Yehova anamuuza chiyani Yoswa, Aisiraeli asanayambe kuzungulira Yeriko? N’chifukwa chiyani malangizowa ankaoneka ngati osathandiza kwenikweni? (Yos. 5:2-8; w18.10 23 ¶5–7)
3. Kodi pali umboni wotani wotsimikizira kuti asilikali analanda mzinda wa Yeriko atangouzungulira kwa nthawi yochepa? (w15 11/15 13) B
Kennedy, Titus (2023). The Bronze Age Destruction of Jericho, Archaeology, and the Book of Joshua. Accessed via researchgate.net. Licensed under CC by 4.0 DEED
Chithunzi B: Mbiya zopsa ndi moto zomwe ankasungiramo mbewu, zinapezeka pomwe panali mzinda wakale wa Yeriko
4. Kodi ulosi wa pa Yoswa 6:26 wonena za mzinda wa Yeriko, unakwaniritsidwa bwanji? (w98 9/15 21 ¶8-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
N’chiyani chinkathandiza Yoswa kutsimikizira kuti zomwe Yehova walonjeza zichitikadi? (Yos. 23:14) Nanga tingatani kuti ifenso tizikhala ndi chikhulupiriro ngati chimenecho?
Kodi chitsanzo cha Yoswa chingatithandize bwanji kutsatira malangizo omwe gulu la Yehova lingatipatse? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yoswa?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yoswa akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi chitsanzo cha Yoswa chingatilimbikitse bwanji kuphunzira zinthu kwa achikulire, kukhulupirira malonjezo a Mulungu komanso kukhalabe wokhulupirika ngakhale Akhristu anzathu atatikhumudwitsa?
Thandizani ana anu kuti azikumbukira zinthu zikuluzikulu zomwe zinachitika pa moyo wa Yoswa.